< Masalimo 56 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Njiwa pa Mtengo wa Thundu wa Kutali.” Mikitamu ya Davide, pamene Afilisti anamugwira ku Gati. Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri; tsiku lonse akundithira nkhondo.
Be merciful to me, O God, for man would swallow me up. Fighting all the day long he oppresses me.
2 Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse, ambiri akumenyana nane monyada.
My enemies would swallow me up all the day long, for they are many who fight proudly against me.
3 Ndikachita mantha ndimadalira Inu.
What time I am afraid, I will put my trust in thee.
4 Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda, mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha. Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?
In God I will praise his word. In God I have put my trust. I will not be afraid. What can flesh do to me?
5 Tsiku lonse amatembenuza mawu anga; nthawi zonse amakonza zondivulaza.
All the day long they wrest my words. All their thoughts are against me for evil.
6 Iwo amakambirana, amandibisalira, amayangʼanitsitsa mayendedwe anga ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga.
They gather themselves together. They hide themselves. They mark my steps, even as they have waited for my soul.
7 Musalole konse kuti athawe; mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu.
Shall they escape by iniquity? In anger cast down the peoples, O God.
8 Mulembe za kulira kwanga, mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu. Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?
Thou number my wanderings. Put thou my tears into thy bottle. Are they not in thy book?
9 Adani anga adzabwerera mʼmbuyo pamene ndidzalirira kwa Inu. Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga.
Then shall my enemies turn back in the day that I call. This I know, that God is for me.
10 Mwa Mulungu amene mawu ake ndimawatamanda, mwa Yehova amene mawu ake ndimawatamanda,
In God I will praise his word. In Jehovah I will praise his word.
11 mwa Mulungu ine ndimadalira ndipo sindidzachita mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
In God I have put my trust. I will not be afraid. What can man do to me?
12 Ndiyenera kuchita zomwe ndinalumbira kwa Mulungu; ndidzapereka nsembe zanga zachiyamiko kwa inu.
Thy vows are upon me, O God. I will render thank offerings to thee.
13 Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa ndi mapazi anga kuti ndingagwe, kuti ndiyende pamaso pa Mulungu mʼkuwala kwa moyo.
For thou have delivered my soul from death, and my feet from falling, that I may walk before God in the light of the living.

< Masalimo 56 >