< Masalimo 144 >

1 Salimo la Davide. Atamandike Yehova Thanthwe langa, amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; zala zanga kumenya nkhondo.
Blessed be Jehovah, my rock, who teaches my hands to war, and my fingers to fight,
2 Iye ndiye Mulungu wanga wachikondi ndi malo anga otetezedwa, linga langa ndi mpulumutsi wanga, chishango changa mmene ine ndimathawiramo, amene amagonjetsa mitundu ya anthu pansi panga.
my loving kindness, and my fortress, my high tower, and my deliverer, my shield, and he in whom I take refuge, who subdues my people under me.
3 Inu Yehova, munthu nʼchiyani kuti mumamusamalira, mwana wa munthu kuti muzimuganizira?
Jehovah, what is man, that thou take knowledge of him? Or the son of man, that thou make account of him?
4 Munthu ali ngati mpweya; masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.
Man is like vanity. His days are as a shadow that passes away.
5 Ngʼambani mayiko akumwamba, Inu Yehova, ndipo tsikani pansi; khudzani mapiri kuti atulutse utsi.
Bow thy heavens, O Jehovah, and come down. Touch the mountains, and they shall smoke.
6 Tumizani zingʼaningʼani ndi kubalalitsa adani; ponyani mivi yanu ndi kuwathamangitsa.
Cast forth lightning, and scatter them. Send out thine arrows, and discomfit them.
7 Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba; landitseni ndi kundipulumutsa, ku madzi amphamvu, mʼmanja mwa anthu achilendo,
Stretch forth thy hand from above. Rescue me, and deliver me out of great waters, out of the hand of aliens,
8 amene pakamwa pawo ndi podzala ndi mabodza, amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.
whose mouth speaks deceit, and whose right hand is a right hand of falsehood.
9 Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu; ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,
I will sing a new song to thee, O God. Upon a psaltery of ten strings I will sing praises to thee.
10 kwa Iye amene amapambanitsa mafumu, amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.
Thou are he who gives salvation to kings, who rescues David his servant from the hurtful sword.
11 Landitseni ndi kundipulumutsa, mʼmanja mwa anthu achilendo, amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza, amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.
Rescue me, and deliver me out of the hand of aliens, whose mouth speaks deceit, and whose right hand is a right hand of falsehood.
12 Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino, ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.
That our sons shall be as plants grown up in their youth, and our daughters as cornerstones hewn according to the fashion of a palace,
13 Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza ndi zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda pa mabusa athu.
our garners are full, affording all manner of store, our sheep bring forth thousands and ten thousands in our fields,
14 Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera. Sipadzakhala mingʼalu pa makoma, sipadzakhalanso kupita ku ukapolo, mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.
our oxen are well laden, no breaking in, and no going forth, and no outcry in our streets,
15 Odala anthu amene adzalandira madalitso awa; odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.
blessed are the people who are in such a case. Blessed are the people whose God is Jehovah.

< Masalimo 144 >