< Yesaya 50 >

1 Yehova akuti, “Kalata imene ndinasudzulira amayi anu ili kuti? Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole, ndinakugulitsani kwa ati? Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu; amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.
Thus says Jehovah, Where is the bill of your mother's divorcement, with which I have put her away? Or which of my creditors is it to whom I have sold you? Behold, for your iniquities ye were sold, and for your transgressions your mother was put away.
2 Nʼchifukwa chiyani pamene ndinabwera kudzakupulumutsani panalibe munthu? Pamene ndinayitana, nʼchifukwa chiyani panalibe wondiyankha? Kodi dzanja langa ndi lalifupi kuti nʼkulephera kukuwombolani? Kodi ndilibe mphamvu zokupulumutsirani? Ndi kudzudzula kokha ndinawumitsa nyanja yayikulu, mitsinje ndinayisandutsa chipululu; nsomba za mʼmenemo zinawola chifukwa chosowa madzi; ndipo zinafa ndi ludzu.
Why, when I came, was there no man? When I called, was there none to answer? Is my hand shortened at all, that it cannot redeem? Or have I no power to deliver? Behold, at my rebuke I dry up the sea. I make the rivers a wilderness. Their fish stink because there is no water, and die for thirst.
3 Ndinaphimba thambo ndi mdima ndipo chiguduli chinakhala chofunda chake.”
I clothe the heavens with blackness, and I make sackcloth their covering.
4 Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka. Mmawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.
The lord Jehovah has given me the tongue of those who are taught, that I may know how to sustain with words him who is weary. He awakens morning by morning. He awakens my ear to hear as those who are taught.
5 Ambuye Yehova wanditsekula makutu anga, ndipo sindinakhale munthu wowukira ndipo sindinabwerere mʼmbuyo.
The lord Jehovah has opened my ear, and I was not rebellious, nor turned away backward.
6 Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu; sindinawabisire nkhope yanga anthu ondinyoza ndi ondilavulira.
I gave my back to the smiters, and my cheeks to those who plucked off the hair. I did not hide my face from shame and spitting.
7 Popeza Ambuye Yehova amandithandiza, sindidzachita manyazi. Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi, chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.
For the lord Jehovah will help me. Therefore I have not been confounded. Therefore I have set my face like a flint, and I know that I shall not be put to shame.
8 Wondikhalira kumbuyo ali pafupi, ndaninso amene adzandiyimba mlandu? Abwere kuti tionane maso ndi maso! Mdani wanga ndi ndani? Abweretu kuti tilimbane!
He is near who justifies me. Who will contend with me? Let us stand up together. Who is my adversary? Let him come near to me.
9 Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza. Ndaninso amene adzanditsutsa? Onse adzatha ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.
Behold, the lord Jehovah will help me. Who is he who shall condemn me? Behold, all they shall grow old as a garment; the moth shall eat them up.
10 Ndani mwa inu amaopa Yehova ndi kumvera mawu a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, popanda chomuwunikira, iye akhulupirire dzina la Yehova ndi kudalira Mulungu wake.
Who is among you that fears Jehovah, who obeys the voice of his servant? He who walks in darkness, and has no light, let him trust in the name of Jehovah, and rely upon his God.
11 Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha moto ndi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu, lowani mʼmoto wanu womwewo. Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa. Ndipo ine Yehova ndiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.
Behold, all ye who kindle a fire, who gird yourselves about with firebrands, walk ye in the flame of your fire, and among the brands that ye have kindled. This ye shall have from my hand. Ye shall lie down in sorrow.

< Yesaya 50 >