< Yesaya 28 >

1 Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu. Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa limene lili pa mutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde.
Woe to the crown of pride of the drunkards of Ephraim, and to the fading flower of his glorious beauty, which is on the head of the fat valley of those who are overcome with wine!
2 Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga. Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga, ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho; ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza.
Behold, the Lord has a mighty and strong one. As a tempest of hail, a destroying storm, as a tempest of mighty waters overflowing, he will cast down to the earth with the hand.
3 Ulamuliro wa atsogoleri oledzera a ku Efereimu adzawuthetsa.
The crown of pride of the drunkards of Ephraim shall be trodden under foot.
4 Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja, udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa imene munthu akangoyiona amayithyola nthawi yokolola isanakwane.
And the fading flower of his glorious beauty, which is on the head of the fat valley, shall be as the first-ripe fig before the summer, which, when he who looks upon it sees, while it is yet in his hand, he eats it up.
5 Tsiku limenelo Yehova Wamphamvuzonse adzakhala ngati nkhata yaufumu, chipewa chokongola kwa anthu ake otsala.
In that day Jehovah of hosts will become a crown of glory, and a diadem of beauty, to the residue of his people,
6 Iye adzapereka mtima wachilungamo kwa oweruza, adzakhala chilimbikitso kwa amene amabweza adani pa zipata za mzinda.
and a spirit of justice to him who sits in judgment, and strength to those who turn back the battle at the gate.
7 Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo ndipo akusochera chifukwa cha mowa: ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo; akusochera chifukwa cha mowa, akudzandira pamene akuona masomphenya, kupunthwa pamene akupereka chigamulo.
And even these reel with wine, and stagger with strong drink. The priest and the prophet reel with strong drink. They are swallowed up of wine. They stagger with strong drink; they err in vision; they stumble in judgment.
8 Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha ndipo palibenso malo wopanda zonyansa.
For all tables are full of vomit, filthiness, no place clean.
9 Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani? Uthengawu akufuna kufotokozera yani? Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa, kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?
Whom will he teach knowledge? And whom will he make to understand the message? Those who are weaned from the milk, and drawn from the breasts?
10 Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono.”
For it is precept upon precept, precept upon precept, line upon line, line upon line, here a little, there a little.
11 Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino. Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene
No, but by men of strange lips and with another tongue he will speak to this people,
12 anakuwuzani kuti, “Malo opumulira ndi ano, otopa apumule, malo owusira ndi ano.” Koma inu simunamvere.
to whom he said, This is the rest. Give ye rest to him who is weary. And this is the refreshing. Yet they would not hear.
13 Choncho Yehova adzakuphunzitsani pangʼonopangʼono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo, adzapweteka ndi kukodwa mu msampha ndipo adzakutengani ku ukapolo.
Therefore the word of Jehovah shall be to them precept upon precept, precept upon precept, line upon line, line upon line, here a little, there a little, that they may go, and fall backward, and be broken, and snared, and taken.
14 Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova, inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu.
Therefore hear the word of Jehovah, ye scoffers, who rule this people that is in Jerusalem.
15 Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa, ife tachita mgwirizano ndi manda. Pamene mliri woopsa ukadzafika sudzatikhudza ife, chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.” (Sheol h7585)
Because ye have said, We have made a covenant with death, and we are at agreement with Sheol. When the overflowing scourge shall pass through it shall not come to us, for we have made lies our refuge, and we have hid ourselves under falsehood. (Sheol h7585)
16 Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi: “Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri ngati maziko mu Ziyoni, mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu; munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.
Therefore thus says the lord Jehovah, Behold, I lay in Zion for a foundation, a stone, a tried stone, a precious corner-stone, a sure foundation. He who believes in him shall, no, not be shamed.
17 Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake, ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere; matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza, ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.
And I will make justice the line, and righteousness the plummet. And the hail shall sweep away the refuge of lies, and the waters shall overflow the hiding-place.
18 Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa; mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa. Pakuti mliri woopsa udzafika, ndipo udzakugonjetsani. (Sheol h7585)
And your covenant with death shall be annulled, and your agreement with Sheol shall not stand. When the overflowing scourge shall pass through, then ye shall be trodden down by it. (Sheol h7585)
19 Ndipo ukadzangofika udzakutengani. Udzafika mmawa uliwonse, usiku ndi usana.” Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu adzaopsedwa kwambiri.
As often as it passes though, it shall take you. For morning by morning it shall pass through, by day and by night. And it shall be nothing but terror to understand the report.
20 Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo; ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe.
For the bed is shorter than what a man can stretch himself on it, and the covering narrower than what he can wrap himself in it.
21 Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni; adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo, ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.
For Jehovah will rise up as in mount Perazim. He will be angry as in the valley of Gibeon, that he may do his work, his strange work, and bring to pass his act, his strange act.
22 Tsopano lekani kunyoza, mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri; Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti, “Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi.”
Now therefore be ye not scoffers, lest your bonds be made strong. For I have heard a decree of destruction from the Lord, Jehovah of hosts, upon the whole earth.
23 Tcherani khutu ndipo mumve mawu anga; mvetserani ndipo mumve zimene ndikunena.
Give ye ear, and hear my voice, hearken, and hear my speech.
24 Kodi mlimi wofuna kudzala mbewu amangokhalira kutipula kokhakokha? Kodi amangokhalira kugawula ndi kugalawuza kokhakokha?
Does he who plows to sow plow continually? Does he continually open and harrow his ground?
25 Pamene iye wasalaza mundawo, kodi samafesa mawere ndi chitowe? Kodi suja samadzala tirigu ndi barele mʼmizere yake, nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo?
When he has leveled the face of it, does he not cast abroad the chick-peas, and scatter the cummin, and put in the wheat in rows, and the barley in the appointed place, and the spelt in the border of it?
26 Mulungu wake amamulangiza ndi kumuphunzitsa njira yabwino.
For his God instructs him aright, and teaches him.
27 Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero, kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta; mawere amapuntha ndi ndodo ndipo chitowe amapuntha ndi kamtengo.
For the chick-peas are not threshed with a sharp instrument, nor is a cart wheel turned about upon the cummin, but the chick-peas are beaten out with a staff, and the cummin with a rod.
28 Tirigu ayenera kusinjidwa kuti apangire buledi, komabe munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo osalekeza, kuopa kuti angatekedzeke. Ngakhale kuti amapuntha tiriguyo poyendetsapo mikombero ya galeta, koma akavalo ake satekedza tiriguyo.
Bread grain is ground, for he will not be always threshing it. And though the wheel of his cart and his horses scatter it, he does not grind it.
29 Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.
This also comes forth from Jehovah of hosts, who is wonderful in counsel, and excellent in wisdom.

< Yesaya 28 >