< Deuteronomo 23 >

1 Mwamuna aliyense wofulidwa kapena woduka chiwalo chachimuna asalowe nawo mu msonkhano wa Yehova.
He who is wounded in the testicles, or has his private part cut off, shall not enter into the assembly of Jehovah.
2 Aliyense wobadwa mʼbanja losavomerezeka, kapena mdzukulu wake wina aliyense, ngakhale mibado khumi pambuyo pake, asalowe mu msonkhano wa Yehova.
A bastard shall not enter into the assembly of Jehovah, even to the tenth generation none of his shall enter into the assembly of Jehovah.
3 Mwamoni kapena Mmowabu asalowe mu msonkhano wa anthu a Yehova ngakhale mibado khumi yobwera pambuyo pake.
An Ammonite or a Moabite shall not enter into the assembly of Jehovah, even to the tenth generation none belonging to them shall enter into the assembly of Jehovah forever,
4 Pakuti iwowa sanabwere kudzakulonjerani ndi chakudya kapena madzi pamene mumadutsa pochokera ku Igupto, mʼmalo mwake anakalemba ganyu Balaamu mwana wa Beori wochokera ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.
because they met you not with bread and with water on the way, when ye came forth out of Egypt, and because they hired against thee Balaam the son of Beor from Pethor of Mesopotamia, to curse thee.
5 Komabe Yehova Mulungu wanu sanamvere Balaamu koma anatembenuza temberero kukhala dalitso kwa inu chifukwa Yehova Mulungu wanu amakukondani.
Nevertheless Jehovah thy God would not hearken to Balaam, but Jehovah thy God turned the curse into a blessing to thee, because Jehovah thy God loved thee.
6 Musachite nawo mgwirizano uliwonse wa mtendere pa moyo wanu wonse.
Thou shall not seek their peace nor their prosperity all thy days forever.
7 Musapeputse Mwedomu pakuti ndi mʼbale wanu ndithu. Musapeputse Mwigupto chifukwa munali alendo mʼdziko lake.
Thou shall not abhor an Edomite, for he is thy brother. Thou shall not abhor an Egyptian, because thou were a sojourner in his land.
8 Mʼbado wachitatu wa ana awo akhoza kulowa mu msonkhano wa anthu a Yehova.
The sons of the third generation who are born to them shall enter into the assembly of Jehovah.
9 Mukamakhala pa msasa pokonzekera adani anu, musayandikane ndi china chilichonse chodetsedwa.
When the army goes forth against thine enemies, then thou shall keep thee from every evil thing.
10 Wina mwa asilikali anu akadziwonongera ndi umuna usiku, ayenera kuchoka pa msasapo ndipo akhale kunja kwa msasa.
If there be among you any man, who is not clean by reason of an accident by night, then he shall go abroad out of the camp. He shall not come inside the camp.
11 Koma dzuwa likapendeka ayenera kusamba ndipo polowa dzuwa akhoza kubwerera ku msasa.
But it shall be, when evening comes on, he shall bathe himself in water, and when the sun is down, he shall come inside the camp.
12 Mukonze malo kunja kwa msasa kumene mukhoza kukadzithandizirako.
Thou shall have a place also outside the camp, where thou shall go forth abroad.
13 Pakati pa zida zanu muzikhala ndi china chokumbira, ndipo pokadzithandiza muzikumba kadzenje ndi kukwirira chimbudzi chanu.
And thou shall have a paddle among thy weapons, and it shall be, when thou sit down abroad, thou shall dig with it, and shall turn back and cover that which comes from thee.
14 Pakuti Yehova Mulungu wanu amayendayenda ku msasa wanu kukutchinjirizani ndi kupereka adani anu kwa inu. Nʼchifukwa chake msasa wanu uzikhala wopatulika kuti mwina angaone china chonyansa nabwerera osakuyandikirani.
For Jehovah thy God walks in the midst of thy camp, to deliver thee, and to give up thine enemies before thee. Therefore thy camp shall be holy, that he may not see an unclean thing in thee, and turn away from thee.
15 Ngati kapolo wathawa mbuye wake nakabisala kwanu, musamuperekenso kwa mbuye wakeyo.
Thou shall not deliver to his master a servant who is escaped from his master to thee.
16 Mumulole akhale pakati panu, paliponse pamene angakonde, mʼmudzi umene angasankhe ndipo musamupondereze.
He shall dwell with thee, in the midst of thee, in the place which he shall choose within one of thy gates, where it pleases him best. Thou shall not oppress him.
17 Pasapezeke Mwisraeli wamwamuna kapena wamkazi wochita chiwerewere ku Nyumba ya Mulungu.
There shall be no prostitute of the daughters of Israel, neither shall there be a sodomite of the sons of Israel.
18 Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi.
Thou shall not bring the hire of a harlot, or the wages of a dog, into the house of Jehovah thy God for any vow, for even both these are an abomination to Jehovah thy God.
19 Musamalipitse mʼbale wanu chiwongoladzanja, kaya pa ndalama, kapena pa chakudya, kapena pa china chilichonse choti nʼkupereketsa chiwongoladzanja.
Thou shall not lend upon interest to thy brother: interest of money, interest of food, interest of anything that is lent upon interest.
20 Mlendo mukhoza kumulipitsa chiwongoladzanja koma osati mʼbale wanu Mwisraeli, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochitika zanu zonse mʼdziko mukulowamoli.
To a foreigner thou may lend upon interest, but to thy brother thou shall not lend upon interest, that Jehovah thy God may bless thee in all that thou put thy hand to, in the land where thou go in to possess it.
21 Mukalumbira kupereka kanthu kwa Yehova Mulungu wanu, musamachedwetse kupereka, chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakufunsanibe kanthuko ndipo mudzapezeka wochimwa.
When thou shall vow a vow to Jehovah thy God, thou shall not be slack to pay it. For Jehovah thy God will surely require it of thee, and it would be sin in thee.
22 Koma ngati mupewa kupanga mapangano simudzapezeka ochimwa.
But if thou shall forbear to vow, it shall be no sin in thee.
23 Zilizonse zimene mulumbira ndi pakamwa panu muzitsimikiza kuzichita, chifukwa mwalumbira mwaufulu pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi pakamwa panu.
That which has gone out of thy lips thou shall observe and do, according as thou have vowed to Jehovah thy God, a freewill offering, which thou have promised with thy mouth.
24 Mukalowa mʼmunda wamphesa wa mnzanu mukhoza kudya mphesa mmene mungafunire koma musayike zina mʼdengu mwanu.
When thou come into thy neighbor's vineyard, then thou may eat thy fill of grapes at thine own pleasure, but thou shall not put any in thy vessel.
25 Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mʼbale wanu, mukhoza kutengako ngala mʼmanja mwanu, koma osasenga tirigu ndi chikwakwa.
When thou come into thy neighbor's standing grain, then thou may pluck the ears with thy hand, but thou shall not move a sickle to thy neighbor's standing grain.

< Deuteronomo 23 >