< Бытие 43 >

1 Глад же одоле на земли.
Njala inakula kwambiri mʼdzikomo.
2 Бысть же егда скончаша пшеницу ядуще, юже принесоша из Египта: и рече им отец их: паки шедше купите нам мало пищи.
Tsono atatha kudya tirigu yense amene anakatenga ku Igupto, Yakobo anati kwa ana ake aja, “Pitani kuti mukatigulire chakudya china pangʼono.”
3 Рече же ему Иуда, глаголя: клятвою засвидетелствова нам муж господин земли (тоя) глаголя: не узрите лица моего, аще брат ваш менший не приидет с вами:
Koma Yuda anati kwa iye, “Munthu uja anatichenjeza monenetsa kuti, ‘Simudzandionanso ine pokhapokha mutabwera ndi mngʼono wanu.’
4 аще убо послеши брата нашего с нами, пойдем и купим тебе пищи:
Mukalola kuti mngʼono wathuyu apite nafe, ndiye ife tidzapita kukakugulirani chakudya.
5 аще же не послеши брата нашего с нами, не пойдем: муж бо рече нам, глаголя: не узрите лица моего, аще брат ваш менший не приидет с вами.
Koma mukapanda kumulola, ife sitipita, chifukwa munthuyo anatiwuza kuti, ‘Simudzandionanso pokhapokha mutabwera ndi mngʼono wanuyo.’”
6 Рече же Израиль: почто зло сотвористе ми, поведавше мужу, яко есть вам брат?
Tsono Israeli anafunsa kuti, “Bwanji inu munandiputira mavuto oterewa pomuwuza munthuyo kuti muli ndi mʼbale wanu wina?”
7 Они же реша: вопрошая вопроси нас муж и рода нашего, глаголя: аще еще отец ваш жив есть, и аще есть вам брат? И поведахом ему по вопросу сему: еда ведехом, яко речет нам: приведите брата вашего?
Iwo anayankha, “Munthuyo ankangofunsafunsa za ife ndi za banja lathu. Iye anatifunsa kuti, ‘Kodi abambo anu akanali ndi moyo? Kodi muli ndi mʼbale wanu wina?’ Ife tinkangoyankha mafunso ake. Ife tikanadziwa bwanji kuti adzanena kuti, ‘Mubwere naye kuno mʼbale wanu’?”
8 Рече же Иуда ко Израилю, отцу своему: отпусти отрочища со мною: и воставше пойдем, да живи будем и не умрем, и мы и ты и имение наше:
Ndipo Yuda anati kwa Israeli abambo ake, “Muloleni mnyamatayo apite ndi ine, ndipo tinyamuka nthawi yomweyo, kuti ife ndi inu pamodzi ndi ana athu tikhale ndi moyo.
9 аз же возму его: от руку моею взыщи его: аще не приведу его к тебе, и поставлю его пред тобою, грешен буду к тебе вся дни:
Ine ndidzipereka kuti ndikhale chikole cha moyo wa mnyamatayu. Ine ndidzamuteteza. Ngati sindibwera naye ndi kumupereka kwa inu, ndidzakhala wolakwa pamaso panu moyo wanga wonse.
10 аще бо быхом не умедлили, уже возвратилися бы дважды.
Mmene zililimu, tikanapanda kuchedwa, bwenzi titapita ndi kubwerako kawiri.”
11 Рече же им Израиль отец их: аще тако есть, сие сотворите: возмите от плодов земных в сосуды своя и донесите человеку дары, ритину, мед, фимиама же и стакти, и теревинф и орехи:
Tsono abambo awo Israeli anawawuza kuti, “Ngati pafunika kutero, ndiye muchite izi: Ikanimo zipatso zabwino kwambiri za dziko lino mʼmatumba mwanu ndi kumutengera munthuyo ngati mphatso. Mumutengere mafuta wopaka pangʼono, uchi pangʼono, mafuta wonunkhiritsa chakudya, mule, mtedza ndi alimoni.
12 и сребро сугубо возмите в руце свои, и сребро обретенное во вретищах ваших возвратите с собою, да не како неведение есть:
Mutenge ndalama zokwanira. Ndalama zina nʼzokamubwezera zija anakuyikirani mʼmatumba anu zija. Mwina anangolakwitsa.
13 и брата своего поимите, и воставше идите к мужу:
Mutengeninso mngʼono wanuyu ndi kubwerera kwa munthuyo msanga.
14 Бог же мой да даст вам благодать пред мужем и отпустит брата вашего единаго, и Вениамина: аз бо якоже обезчадех, обезчадех.
Ndipo Mulungu Wamphamvuzonse akuchitireni chifundo pamaso pa munthuyo kuti akamulole mʼbale wanu wina uja ndi Benjamini kuti abwerere ndi inu. Kukakhala kulira, ndine wolira basi.”
15 Вземше же мужие дары сия, и сребро сугубое взяша в руце свои, и Вениамина: и воставше приидоша во Египет, и сташа пред Иосифом.
Choncho abale aja anatenga mphatso, ndalama zokwanira ndi Benjamininso. Iwo anafulumira kupita ku Igupto ndipo anakaonekera kwa Yosefe.
16 Виде же их Иосиф, и Вениамина брата своего единоматерня, и рече строителю дому своего: введи мужы (сия) в дом, и заколи от скота, и уготовай: со мною бо ясти имут мужие (сии) хлеб в полудне.
Yosefe ataona Benjamini ali pamodzi ndi abale ake, anati kwa wantchito wa mʼnyumba mwake, “Atengereni anthu awa ku nyumba kwanga, ndipo uphe nyama ndi kukonza bwino chakudya popeza amenewa adya ndi ine masana ano.”
17 Сотвори же человек, якоже рече Иосиф, и введе мужы в дом Иосифов.
Wantchitoyo anachita monga momwe Yosefe ananenera, ndipo anawatengera abale aja ku nyumba kwa Yosefe.
18 Видевше же мужие, яко введоша их в дом Иосифов, реша: сребра ради возвращеннаго во вретищах наших первее, вводят ны, еже бы оклеветати нас и нанести на ны, да поймут нас в рабы, и ослы нашя.
Tsono anthu aja anachita mantha ataona kuti akuwatengera ku nyumba kwa Yosefe. Mʼmaganizo awo ankanena kuti, “Atibweretsa kuno chifukwa cha ndalama zija zinabwezeredwa mʼmatumba athu poyamba paja. Ameneyu akufuna kuti atipanikize ndi kutigwira ukapolo natilanda abulu athu.”
19 Приступивше же к человеку сущему над домом Иосифовым, рекоша ему при вратех дому,
Choncho atafika pa khomo la nyumba ya Yosefe anamuyandikira wantchito wa Yosefe nayankhula naye kuti,
20 глаголюще: молим тя, господине: приидохом первее купити пищи:
“Pepani mbuye wathu, ife tinabweranso ulendo woyamba kudzagula chakudya
21 бысть же егда приидохом на стан и отрешихом вретища своя, и се, сребро коегождо во вретищи его: тое сребро наше весом возвратихом ныне руками нашими:
koma titafika pa malo ena kuti tigone, tinatsekula matumba athu ndipo aliyense wa ife anapeza ndalama zake momwe zinalili zili pakamwa pa thumba lake. Ndiye tabwerera nazo.
22 и сребро другое принесохом с собою купити пищи: не вемы, кто вложи сребро во вретища наша.
Tabweretsanso ndalama zina kuti tigule chakudya. Sitikudziwa kuti kaya ndani anayika ndalamazo mʼmatumba athu.”
23 Рече же им: мир вам, не бойтеся: Бог ваш и Бог отец ваших даде вам сокровища во вретищах ваших: а сребро ваше за приятое имею. И изведе к ним Симеона:
Koma iye anati, “Mitima yanu ikhale pansi ndipo musachite mantha. Mulungu wanu, Mulungu wa abambo anu, anakuyikirani chumacho mʼmatumba anu. Ine ndinalandira ndalama zanu.” Ndipo anakawatulutsira Simeoni.
24 и принесе воду омыти нозе им, и даде пажити ослом их.
Wantchito uja anawalowetsa anthuwo mʼnyumba ya Yosefe, nawapatsa madzi kuti asambe mapazi awo. Anadyetsanso abulu awo.
25 Уготоваша же дары, дондеже приидет Иосиф в полудне: слышаша бо, яко тамо имать обедати.
Abale aja anakonzeratu mphatso zawo zija kuti adzapereke kwa Yosefe, popeza anamva kuti Yosefe adzadya komweko masana.
26 Прииде же Иосиф в дом: и принесоша ему дары, яже имяху в руках своих, в дом: и поклонишася ему лицем до земли.
Yosefe atafika ku nyumbako, iwo anapereka mphatso zija namuweramira pansi.
27 И вопроси их: здрави ли есте? И рече им: здрав ли есть отец ваш, старец, егоже рекосте, еще ли жив есть?
Yosefe anawafunsa za moyo wawo kenaka anati, “Kodi abambo anu wokalamba amene munkandiwuza aja ali bwanji? Ali ndi moyobe?”
28 Они же рекоша: здрав есть раб твой, отец наш, еще жив есть. И рече: благословен человек оный Богу. И приникше поклонишася ему.
Iwo anayankha kuti, “Mtumiki wanu abambo athu akanali ndi moyo ndipo ali bwino.” Ndipo anamugwadira namuweramira pansi.
29 Воззрев же очима своима Иосиф, виде Вениамина брата своего единоматерня и рече: сей ли есть брат ваш юнейший, егоже рекосте ко мне привести? И рече: Бог да помилует тя, чадо.
Pomwazamwaza maso Yosefe anaona Benjamini, mʼbale wake weniweni wa bere limodzi, ndipo anafunsa, “Kodi uyu ndiye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri amene munkandiwuza uja?” Kenaka anati, “Ambuye akukomere mtima mwana wanga.”
30 Возмутися же Иосиф: подвижеся бо утроба его о брате своем, и искаше плакати: вшед же в ложницу, плакася тамо.
Kenaka Yosefe anafulumira kutuluka chifukwa mtima wake unadzaza ndi chifundo cha mngʼono wake ndipo anafuna kulira. Tsono anakalowa mʼchipinda chakechake nakalira kumeneko.
31 И умыв лице, изшед удержася и рече: предложите хлебы.
Atatha kupukuta misozi mʼmaso mwake anatuluka, ndipo modzilimbitsa analamula kuti chakudya chibwere.
32 И предложиша ему единому, и оным особно, и Египтяном, иже с ним ядяху, особно: не можаху бо Египтяне ясти хлеба со Евреи: мерзость бо есть Египтяном (всяк пастух овчий).
Anamupatsira Yosefe chakudya payekha, abale ake aja pawokha, ndiponso Aigupto amene ankadya pamodzi ndi iye nawonso pawokha. Izi zinali choncho chifukwa Aigupto ankanyansidwa kudya pamodzi ndi Ahebri.
33 Седоша же прямо ему первенец по старейшинству своему и менший по меншеству своему, и дивляхуся мужие кийждо ко брату своему:
Abale aja anawakhazika patsogolo pa Yosefe. Iwo anawakhazika monga mwa mabadwidwe awo kuyambira woyamba kubadwa mpaka wotsirizira; ndipo ankangoyangʼanitsitsana modabwa.
34 и взяша части от него к себе: вящшая же бысть часть Вениаминова паче всех частей пятерицею, неже оных: пиша же и упишася с ним.
Tsono ankawagawira chakudya kuchokera pa tebulo la Yosefe. Koma chakudya cha Benjamini chinkaposa cha ena onsewa kasanu. Motero anadya ndi kumwa mpaka kukhuta, ndipo anasangalala pamodzi ndi Yosefe.

< Бытие 43 >