< Књига пророка Амоса 3 >

1 Чујте реч коју говори Господ за вас, синови Израиљеви, за све племе које сам извео из земље мисирске, говорећи:
Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:
2 Само вас познах између свих племена земаљских, зато ћу вас походити за сва безакоња ваша.
“Inu nokha ndi amene ndinakusankhani pakati pa mabanja onse a dziko lapansi; nʼchifukwa chake ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu onse.”
3 Хоће ли двојица ићи заједно, ако се не састану?
Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodzi asanapangane?
4 Хоће ли рикнути лав у шуми, ако нема лова? Хоће ли лавић пустити глас свој из пећине своје, ако не ухвати шта?
Kodi mkango umabangula mʼnkhalango usanagwire nyama? Kodi msona wamkango umalira mʼphanga mwake pamene sunagwire kanthu?
5 Хоће ли птица пасти у мрежу на земљу, ако нема замке? Хоће ли се дигнути мрежа са земље, ако се ништа не ухвати?
Kodi mbalame nʼkutera pa msampha pamene palibe nyambo yake? Kodi msampha umafwamphuka usanakole kanthu?
6 Хоће ли труба трубити по граду, а народ да не дотрчи уплашен? Хоће ли бити несрећа у граду, а Господ да је не учини?
Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda, anthu sanjenjemera? Pamene tsoka lafika mu mzinda, kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo?
7 Јер Господ Господ не чини ништа не откривши тајне своје слугама својим пророцима.
Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu asanawulule zimene akufuna kuchita kwa atumiki ake, aneneri.
8 Кад лав рикне, ко се неће бојати? Кад Господ рече, ко неће пророковати?
Mkango wabangula, ndani amene sachita mantha? Ambuye Yehova wayankhula, ndani amene sanganenere?
9 Огласите по дворовима азотским и по дворовима у земљи мисирској, и реците: Скупите се на горе самаријске и видите велике нереде у њој, и насиље у њој.
Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto: “Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya; onani chisokonezo pakati pake ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”
10 Не знају чинити право, говори Господ, сабирају благо насиљем и грабежом у дворима својим.
“Iwo sadziwa kuchita zolungama, ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.
11 Зато овако вели Господ Господ: Непријатељ је око земље и обориће ти силу твоју, и оплениће се дворови твоји.
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi: “Mdani adzalizungulira dzikoli; iye adzagwetsa malinga ako, ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”
12 Овако вели Господ: Као кад пастир истргне из уста лаву две ноге или крај од уха, тако ће се истргнути синови Израиљеви који седе у Самарији на углу од одра и накрај постеље.
Yehova akuti, “Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu, moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli amene amakhala mu Samariya pa msonga za mabedi awo, ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”
13 Чујте и засведочите у дому Јаковљевом, говори Господ Господ Бог над војскама.
“Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
14 Кад походим Израиља за грехе његове, тада ћу походити и олтаре ветиљске, и одбиће се рогови олтару и пашће на земљу.
“Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake, ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli; nyanga za guwa zidzathyoka ndipo zidzagwa pansi.
15 И ударићу кућу зимну и летњу кућу, и пропашће куће од слонове кости, и нестаће великих кућа, говори Господ.
Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha; nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,” akutero Yehova.

< Књига пророка Амоса 3 >