< 2-е Тимофею 3 >

1 Знай же, что в последние дни наступят времена тяжкие.
Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri.
2 Ибо люди будут самолюбивы, сребролюбивы, горды, надменны, злоречивы, родителям непокорны, неблагодарны, нечестивы, недружелюбны,
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero.
3 непримирительны, клеветники, невоздержны, жестоки, не любящие добра,
Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino,
4 предатели, наглы, напыщенны, более сластолюбивы, нежели боголюбивы,
opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu.
5 имеющие вид благочестия, силы же его отрекшиеся. Таковых удаляйся.
Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.
6 К сим принадлежат те, которые вкрадываются в домы и обольщают женщин, утопающих во грехах, водимых различными похотями,
Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu,
7 всегда учащихся и никогда не могущих дойти до познания истины.
amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi.
8 Как Ианний и Иамврий противились Моисею, так и сии противятся истине, люди, развращенные умом, невежды в вере.
Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa.
9 Но они не много успеют; ибо их безумие обнаружится перед всеми, как и с теми случилось.
Koma sadzapita nazo patali kwambiri zimenezi, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwawo monga anachitira Yanesi ndi Yambere.
10 А ты последовал мне в учении, житии, расположении, вере, великодушии, любви, терпении,
Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga,
11 в гонениях, страданиях, постигших меня в Антиохии, Иконии, Листрах; каковые гонения я перенес, и от всех избавил меня Господь.
mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi.
12 Да и все, желающие жить благочестиво во Христе Иисусе, будут гонимы.
Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,
13 Злые же люди и обманщики будут преуспевать во зле, вводя в заблуждение и заблуждаясь.
pomwe anthu oyipa ndi onyenga adzanka nayipirayipira, kunamiza ena, iwo nʼkumanamizidwanso.
14 А ты пребывай в том, чему научен и что тебе вверено, зная, кем ты научен.
Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi.
15 Притом же ты из детства знаешь священные писания, которые могут умудрить тебя во спасение верою во Христа Иисуса.
Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu.
16 Все Писание богодухновенно и полезно для научения, для обличения, для исправления, для наставления в праведности,
Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo
17 да будет совершен Божий человек, ко всякому доброму делу приготовлен.
kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.

< 2-е Тимофею 3 >