< 2-е Тимофею 4 >

1 Итак заклинаю тебя пред Богом и Господом нашим Иисусом Христом, Который будет судить живых и мертвых в явление Его и Царствие Его:
Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa omwe pamene adzaonekera ndi ufumu wake, ndikukulamula kuti:
2 проповедуй слово, настой во время и не во время, обличай, запрещай, увещевай со всяким долготерпением и назиданием.
Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa.
3 Ибо будет время, когда здравого учения принимать не будут, но по своим прихотям будут избирать себе учителей, которые льстили бы слуху;
Pakuti idzafika nthawi imene anthu adzakana chiphunzitso choona. Mʼmalo mwake, chifukwa chokhumba kumva zowakomera zokha, adzasonkhanitsa aphunzitsi ambiri omawawuza zimene iwo akufuna kumva.
4 и от истины отвратят слух и обратятся к басням.
Sadzafuna kumva choona koma adzafuna kumva nthano chabe.
5 Но ты будь бдителен во всем, переноси скорби, совершай дело благовестника, исполняй служение твое.
Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya mlaliki, gwira ntchito zonse za utumiki wako.
6 Ибо я уже становлюсь жертвою, и время моего отшествия настало.
Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga.
7 Подвигом добрым я подвизался, течение совершил, веру сохранил;
Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro.
8 а теперь готовится мне венец правды, который даст мне Господь, праведный Судия, в день оный; и не только мне, но и всем, возлюбившим явление Его.
Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.
9 Постарайся придти ко мне скоро.
Uyesetse kubwera kuno msanga.
10 Ибо Димас оставил меня, возлюбив нынешний век, и пошел в Фессалонику, Крискент в Галатию, Тит в Далматию; один Лука со мною. (aiōn g165)
Paja Dema anandisiya chifukwa chokonda dziko lapansi lino, ndipo anapita ku Tesalonika. Kresike anapita ku Galatiya ndipo Tito anapita ku Dalimatiya. (aiōn g165)
11 Марка возьми и приведи с собою, ибо он мне нужен для служения.
Ndatsala ndi Luka yekha basi. Mutenge Marko ndipo ubwere naye kuno, chifukwa amandithandiza mu utumiki wanga.
12 Тихика я послал в Ефес.
Ndatumiza Tukiko ku Efeso.
13 Когда пойдешь, принеси фелонь, который я оставил в Троаде у Карпа, и книги, особенно кожаные.
Pobwera, unditengere chofunda pamwamba chimene ndinachisiya kwa Kupro ku Trowa. Unditengerenso mabuku anga, makamaka aja azikopawa.
14 Александр медник много сделал мне зла. Да воздаст ему Господь по делам его!
Alekisandro, mmisiri wa zitsulo anandichitira zoyipa kwambiri. Ambuye adzamubwezera pa zimene anachita.
15 Берегись его и ты, ибо он сильно противился нашим словам.
Iwenso ukhale naye tcheru chifukwa anatsutsa kwambiri uthenga wathu.
16 При первом моем ответе никого не было со мною, но все меня оставили. Да не вменится им!
Podziteteza koyamba pa mlandu wanga, panalibe ndi mmodzi yemwe amene anandithandiza, koma aliyense anandithawa. Mulungu awakhululukire.
17 Господь же предстал мне и укрепил меня, дабы через меня утвердилось благовестие и услышали все язычники; и я избавился из львиных челюстей.
Koma Ambuye anayima nane limodzi, ndipo anandipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, uthenga ulalikidwe kwambiri, ndikuti anthu a mitundu ina amve. Ndipo ndinalanditsidwa mʼkamwa mwa mkango.
18 И избавит меня Господь от всякого злого дела и сохранит для Своего Небесного Царства, Ему слава во веки веков. Аминь. (aiōn g165)
Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya. (aiōn g165)
19 Приветствуй Прискиллу и Акилу и дом Онисифоров.
Pereka moni kwa Prisila ndi Akura pamodzi ndi banja lonse la Onesiforo.
20 Ераст остался в Коринфе; Трофима же я оставил больного в Милите.
Erasto anatsalira ku Korinto. Trofimo ndinamusiya akudwala ku Mileto.
21 Постарайся придти до зимы. Приветствуют тебя Еввул, и Пуд, и Лин, и Клавдия, и все братия.
Uyesetse kubwera kuno nthawi yozizira isanafike. Eubulo akupereka moni, ndiponso Pude, Lino, Klaudiya ndi abale onse nawonso akupereka moni.
22 Господь Иисус Христос со духом твоим. Благодать с вами. Аминь.
Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale ndi inu nonse.

< 2-е Тимофею 4 >