< Luke 13 >

1 Now there were some present at the same time who told him about the Galilaye, whose blood Pilate had mixed with their sacrifices.
Nthawi yomweyo panali ena amene analipo omwe amamuwuza Yesu za Agalileya amene magazi awo Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo.
2 And he answered and said to them, "Do you think that these Galilaye were worse sinners than all the other Galilaye, because they suffered these things?
Yesu anayankha kuti, “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewa anali ochimwa kwambiri kuposa Agalileya ena onse chifukwa anavutika mʼnjira iyi?
3 I tell you, no, but unless you repent, you will all perish in the same way.
Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.
4 Or those eighteen, on whom the tower in Shilukha fell, and killed them; do you think that they were worse offenders than all the others who dwell in Urishlim?
Kapena anthu 18 aja amene anafa nsanja ya Siloamu itawagwera, kodi mukuganiza kuti iwo aja anali ochimwa kwambiri kuposa onse amene amakhala mu Yerusalemu?
5 I tell you, no, but, unless you repent, you will all perish in the same way."
Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.”
6 He spoke this parable. "A certain man had a fig tree planted in his vineyard, and he came seeking fruit on it, and found none.
Kenaka Iye anawawuza fanizo kuti, “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu, umene anadzala mʼmunda wamphesa, ndipo Iye anapita kukayangʼana zipatso, koma sanazipeze.
7 He said to the vine dresser, 'Look, these three years I have come looking for fruit on this fig tree, and found none. Cut it down. Why does it waste the soil?'
Tsono kwa munthu amene amasamalira munda wamphesawo anati, ‘Kwa zaka zitatu tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna chipatso pa mtengo uwu ndipo sindinachipeze. Udule! Nʼchifukwa chiyani ukuwononga nthaka?’
8 He answered, 'Lord, leave it alone this year also, until I dig around it, and fertilize it.
“Munthuyo anayankha kuti, ‘Bwana, tawusiyani kwa chaka chimodzi chokha ndipo ine ndikumba ngalande mozungulira ndi kuthira manyowa.
9 And if it bears fruit next time, [fine]; but if not, you can cut it down.'"
Ngati udzabale zipatso chaka chamawa, zili bwino! Koma ngati sudzabala, pamenepo mudzawudule.’”
10 He was teaching in one of the synagogues on the Sabbath day.
Pa Sabata Yesu ankaphunzitsa mʼsunagoge ina,
11 And look, a woman who had a spirit of infirmity eighteen years, and she was bent over, and could in no way straighten herself up.
ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe.
12 When Yeshua saw her, he called her, and said to her, "Woman, you are freed from your infirmity."
Yesu atamuona anamuyitana kutsogolo ndipo anati kwa iye, “Amayi, mwamasulidwa ku mavuto.”
13 He laid his hands on her, and immediately she stood up straight, and glorified God.
Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu.
14 The ruler of the synagogue, being indignant because Yeshua had healed on the Sabbath, said to the crowd, "There are six days when work should be done Therefore come on those days and be healed, and not on the Sabbath day."
Chifukwa cha kuyipidwa kuti Yesu anachiritsa pa Sabata, wolamulira sunagoge anati kwa anthu, “Pali masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Choncho bwerani kuti mudzachiritsidwe masiku amenewo osati pa Sabata.”
15 Therefore the Lord answered him, "You hypocrites. Does not each one of you free his ox or his donkey from the stall on the Sabbath, and lead him away to water?
Ambuye anamuyankha kuti, “Iwe wachiphamaso! Kodi nonsenu simumasula pa Sabata ngʼombe zanu kapena bulu kumuchotsa mʼkhola ndi kupita naye kukamupatsa madzi?
16 Ought not this woman, being a daughter of Avraham, whom Satana had bound, look, eighteen years, be freed from this bondage on the Sabbath day?"
Nanga mayiyu, amene ndi mwana wa Abrahamu, ndipo anamangidwa ndi Satana zaka 18, kodi siwoyenera kuti amasulidwe msinga imeneyi pa tsiku la Sabata?”
17 As he said these things, all his adversaries were disappointed, and all the crowd rejoiced for all the glorious things that were done by him.
Atanena izi, onse omutsutsa anachititsidwa manyazi, koma anthu anakondwera ndi zodabwitsa zonse zimene Iye anazichita.
18 Then he said, "What is the Kingdom of God like? And to what can I compare it?
Kenaka Yesu anafunsa kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani? Kodi Ine ndingawufanizire ndi chiyani?
19 It is like a grain of mustard seed, which a man took, and put in his own garden. It grew, and became a tree, and the birds of the sky lodged in its branches."
Uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Inakula, nʼkukhala mtengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinakhala mʼnthambi zake.”
20 And again he said, "To what can I compare the Kingdom of God?
Iye anafunsanso kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu ndingawufanizire ndi chiyani?
21 It is like yeast, which a woman took and hid in three measures of flour, until it was all leavened."
Uli ngati yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza ndi ufa wambiri mpaka anafufumitsa ufawo.”
22 He went on his way through cities and villages, teaching, and traveling on to Urishlim.
Ndipo Yesu anayendayenda mʼmizinda ndi mʼmidzi, kumaphunzitsa pamene Iye ankapita ku Yerusalemu.
23 One said to him, "Lord, are they few who are saved?" He said to them,
Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?” Iye anawawuza kuti,
24 "Strive to enter in by the narrow door, for many, I tell you, will seek to enter in, and will not be able.
“Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero.
25 When once the master of the house has risen up, and has shut the door, and you begin to stand outside, and to knock at the door, saying, 'Lord, open to us.' then he will answer and tell you, 'I do not know you or where you come from.'
Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’ “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’
26 Then you will begin to say, 'We ate and drank in your presence, and you taught in our streets.'
“Ndipo inu mudzati, tinkadya ndi kumwa ndi inu ndipo munkaphunzitsa mʼmisewu yathu.
27 But he will reply, 'I do not know where you come from. Depart from me, all you workers of iniquity.'
“Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’
28 There will be weeping and grinding of teeth, when you see Avraham, Iskhaq, Yaquv, and all the prophets, in the Kingdom of God, and yourselves being thrown outside.
“Mudzalira ndi kukuta mano mukadzaona Abrahamu, Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu koma inuyo mutaponyedwa kunja.
29 They will come from the east, west, north, and south, and will sit down in the Kingdom of God.
Anthu adzachokera kummawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kummwera, kudzakhala pa phwando mu ufumu wa Mulungu.
30 And look, there are some who are last who will be first, and there are some who are first who will be last."
Ndithudi otsirizira ndiye adzakhale oyambirira, ndipo oyambirira ndiye adzakhale otsirizira.”
31 In that same hour some Pharisees came, saying to him, "Get out of here, and go away, for Herod wants to kill you."
Pa nthawi imeneyo Afarisi anabwera kwa Yesu ndipo anati kwa Iye, “Chokani malo ano ndipo pitani kumalo ena aliwonse. Herode akufuna kukuphani.”
32 And he said to them, "Go and tell that fox, 'Look, I cast out demons and perform cures today and tomorrow, and the third day I complete my mission.
Iye anayankha kuti, “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.”
33 Nevertheless I must go on my way today and tomorrow and the next day, for it cannot be that a prophet perish outside of Urishlim.'
Mʼnjira ina iliyonse, Ine ndiyenera kupitirira ulendo wanga lero, mawa ndi mkuja. Zoona nʼzakuti mneneri sangafere kunja kwa Yerusalemu.
34 "Urishlim, Urishlim, that kills the prophets, and stones those who are sent to her. How often I wanted to gather your children together, like a hen gathers her own brood under her wings, and you refused.
Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri ndi kuwagenda miyala anthu amene atumizidwa kwa iwe. Nthawi zambiri ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune!
35 Look, your house is abandoned to you. And I tell you, you will not see me until you say, 'Blessed is he who comes in the name of the Lord.'"
Taona, nyumba yako yasanduka bwinja. Ine ndikukuwuza kuti, sudzandionanso mpaka pamene udzati, “Wodala amene akubwera mʼdzina la Ambuye!”

< Luke 13 >