< Yoswa 20 >

1 Pambuyo pake Yehova anati kwa Yoswa:
And Jehovah spoke to Joshua, saying,
2 “Uza Aisraeli kuti apatule mizinda yopulumukiramo, monga ine ndinakulangizira kudzera mwa Mose,
Speak to the sons of Israel, saying, Assign for you the cities of refuge, of which I spoke to you by Moses,
3 kuti aliyense amene wapha munthu mosazindikira osati mwadala azithawirako. Motero adzatetezedwa kwa wolipsira.
that the manslayer who kills any soul unwittingly and unawares may flee there. And they shall be to you for a refuge from the avenger of blood.
4 Ngati munthu wathawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, akafike pa malo oweruzira milandu amene ali pa chipata cha mzindawo ndipo akafotokoze mlandu wake pamaso pa akuluakulu a mzindawo. Kenaka iwo adzamulola kulowa mu mzinda wawo ndi kumupatsa malo woti akhale nawo.
And he shall flee to one of those cities, and shall stand at the entrance of the gate of the city, and declare his case in the ears of the elders of that city. And they shall take him into the city to them, and give him a place, that he may dwell among them.
5 Ngati munthu wolipsirayo amutsatira komweko atsogoleriwo asapereke munthu wakuphayo chifukwa anapha Mwisraeli mnzakeyo mosazindikira, osati mwachiwembu.
And if the avenger of blood pursues after him, then they shall not deliver up the manslayer into his hand, because he smote his neighbor unawares, and did not hate him formerly.
6 Munthu wakuphayo adzakhalabe mu mzindawo mpaka atayimbidwa mlandu pamaso pa gulu lonse, ndiponso mpaka atamwalira mkulu wa ansembe amene akutumikira pa nthawiyo. Pamenepo munthuyo atha kubwereranso ku mudzi kwawo kumene anachoka mothawa kuja.”
And he shall dwell in that city, until he stands before the congregation for judgment, until the death of the high priest who shall be in those days. Then the manslayer shall return, and come to his own city, and to his own house, to the city from where he fled.
7 Choncho iwo anapatula Kedesi mʼdera la Galileya ku mapiri a Nafutali, Sekemu ku mapiri a Efereimu, ndi Kiriati Ariba (ndiye Hebroni) ku mapiri a Yuda.
And they set apart Kedesh in Galilee in the hill-country of Naphtali, and Shechem in the hill-country of Ephraim, and Kiriath-arba (the same is Hebron) in the hill-country of Judah.
8 Kummawa kwa Yorodani, mʼmapiri a chipululu a kummawa kwa Yeriko, anapatula Bezeri pakati pa dera la fuko la Rubeni. Anapatulanso Ramoti ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi, ndiponso Golani ku Basani mʼdera la fuko la Manase.
And beyond the Jordan at Jericho eastward, they assigned Bezer in the wilderness in the plain out of the tribe of Reuben, and Ramoth in Gilead out of the tribe of Gad, and Golan in Bashan out of the tribe of Manasseh.
9 Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraeli onse ngakhalenso mlendo wokhala pakati pawo. Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi ankathawira ku mizinda imeneyi. Munthu wolipsira sankaloledwa kuti aphe munthu wothawayo ngati mlandu wake sunazengedwe pamaso pa gulu lonse.
These were the appointed cities for all the sons of Israel, and for the stranger who sojourns among them, that whoever kills any soul unwittingly might flee there, and not die by the hand of the avenger of blood until he stood before the congregation.

< Yoswa 20 >