< Yobu 24 >

1 “Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze? Chifukwa chiyani iwo amene amadziwa Iyeyo amayembekezera pachabe masiku oterewa?
Why are times not laid up by the Almighty? And why do those who know him not see his days?
2 Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo; amadyetsa ziweto zimene aba.
There are men who remove the landmarks. They take away flocks violently, and feed them.
3 Amalanda abulu a ana amasiye ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole.
They drive away the donkey of the fatherless. They take the widow's ox for a pledge.
4 Amachotsa mʼmisewu anthu osauka, ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko.
They turn the needy out of the way. The poor of the earth all hide themselves.
5 Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu, amayendayenda kufuna chakudya; dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo.
Behold, as wild donkeys in the desert, they go forth to their work, seeking diligently for food. The wilderness yields them bread for their sons.
6 Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake, ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa.
They cut their provender in the field, and they glean the vintage of the wicked.
7 Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala; pa nthawi yozizira amasowa chofunda.
They lie all night naked without clothing, and have no covering in the cold.
8 Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo.
They are wet with the showers of the mountains, and embrace the rock for want of a shelter.
9 Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere; ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole.
There are men who pluck the fatherless from the breast, and take a pledge of the poor,
10 Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala; amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala.
so that they go about naked without clothing, and being hungry they carry the sheaves.
11 Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa; amapsinya mphesa, koma nʼkumamvabe ludzu.
They make oil within the walls of these men. They tread their winepresses, and suffer thirst.
12 Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda, anthu ovulala akulirira chithandizo. Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense.
From out of the populous city men groan, and the soul of the wounded cries out. Yet God does not regard the folly.
13 “Pali ena amene amakana kuwala, amene safuna kuyenda mʼkuwalako kapena kukhala mʼnjira zake.
These are of those who rebel against the light. They do not know the ways of it, nor abide in the paths of it.
14 Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka ndipo amakapha osauka ndi amphawi; nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.
The murderer rises with the light. He kills the poor and needy. And in the night he is as a thief.
15 Munthu wachigololo amadikira chisisira; iyeyo amaganiza kuti, ‘Palibe amene akundiona,’ ndipo amaphimba nkhope yake.
The eye also of the adulterer waits for the twilight, saying, No eye shall see me. And he disguises his face.
16 Mbala zimathyola nyumba usiku, koma masana zimadzitsekera; izo zimathawa kuwala.
In the dark they dig through houses. They shut themselves up in the daytime. They do not know the light.
17 Pakuti kwa onsewa mdima wandiweyani ndiye kuti kwawachera. Iwo amachita ubale ndi zoopsa za mdima.
For the morning is to all of them as thick darkness. For they know the terrors of the thick darkness.
18 “Komatu iwowo ndi thovu loyandama pa madzi; minda yawo ndi yotembereredwa pa dzikolo kotero kuti palibe amene amapita ku minda ya mpesa.
Swiftly they pass away upon the face of the waters. Their portion is cursed in the earth. They do not turn into the way of the vineyards.
19 Monga momwe kutentha ndi chilala zimasungunulira madzi owundana ndi momwemonso mmene manda amachotsera omwe achimwa. (Sheol h7585)
Drought and heat consume the snow waters, and Sheol those who have sinned. (Sheol h7585)
20 Mayi wowabereka amawayiwala, mphutsi zimasangalala powadya; anthu oyipa sakumbukiridwanso koma amathyoka ngati mtengo.
The womb shall forget him. The worm shall feed sweetly on him. He shall be no more remembered. And unrighteousness shall be broken as a tree.
21 Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana, ndipo sakomera mtima mkazi wamasiye.
He devours the barren who do not bear, and does no good to the widow.
22 Koma Mulungu amawononga munthu wamphamvu mwa mphamvu zake; ngakhale munthuyo atakhazikika, alibe chiyembekezo cha moyo wake.
Yet God preserves the mighty by his power. He rises up who has no assurance of life.
23 Mulungu atha kuwalola kuti akhale mosatekeseka, koma amakhala akupenyetsetsa njira zawo.
God gives them to be in security, and they rest in it. And his eyes are upon their ways.
24 Kwa kanthawi kochepa oyipa amakwezedwa ndipo kenaka saonekanso; amatsitsidwa ndipo amachotsedwa monga ena onse; amadulidwa ngati ngala za tirigu.
They are exalted. Yet a little while, and they are gone. Yea, they are brought low. They are taken out of the way as all others, and are cut off as the tops of the ears of grain.
25 “Ngati zimenezi sizoona, ndani angaonetse kuti ndine wabodza ndi kusandutsa mawu anga kukhala wopanda pake?”
And if it be not so now, who will prove me a liar, and make my speech worth nothing?

< Yobu 24 >