< Yesaya 39 >

1 Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani mfumu ya ku Babuloni anatumiza nthumwi kwa Hezekiya nawapatsira makalata ndi mphatso, pakuti anamva za kudwala kwake ndi kuti anachira.
At that time Merodach-baladan the son of Baladan, king of Babylon, sent letters and a present to Hezekiah, for he heard that he had been sick, and was recovered.
2 Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse.
And Hezekiah was glad of them, and showed them the house of his precious things, the silver, and the gold, and the spices, and the precious oil, and all the house of his armor, and all that was found in his treasures. There was nothing in his house, nor in all his dominion, that Hezekiah did not show them.
3 Tsono mneneri Yesaya anapita kwa mfumu Hezekiya ndipo anamufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani chiyani, ndipo anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
Then Isaiah the prophet came to king Hezekiah, and said to him, What did these men say? And from where did they come to thee? And Hezekiah said, They have come from a far country to me, even from Babylon.
4 Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?” Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.”
Then he said, What have they seen in thy house? And Hezekiah answered, They have seen all that is in my house. There is nothing among my treasures that I have not shown them.
5 Pamenepo Yesaya anati kwa Hezekiya, “Imvani mawu a Yehova Wamphamvuzonse:
Then Isaiah said to Hezekiah, Hear the word of Jehovah of hosts:
6 Yehova akuti, nthawi idzafika ndithu pamene zonse za mʼnyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu anazisonkhanitsa mpaka lero lino, zidzatengedwa kupita nazo ku Babuloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe.
Behold, the days are coming, when all that is in thy house, and that which thy fathers have laid up in store until this day, shall be carried to Babylon. Nothing shall be left, says Jehovah.
7 Ndipo ena mwa ana anu, obala inu amene adzatengedwanso, ndipo adzawasandutsa adindo ofulidwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Babuloni.”
And of thy sons who shall issue from thee, whom thou shall beget, they shall take away, and they shall be eunuchs in the palace of the king of Babylon.
8 Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhula ndi abwino.” Ponena izi iye ankaganiza kuti, “Padzakhala mtendere ndi chitetezo masiku a moyo wanga onse.”
Then Hezekiah said to Isaiah, The word of Jehovah which thou have spoken is good. He said moreover, For there shall be peace and truth in my days.

< Yesaya 39 >