< Yesaya 12 >

1 Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati: “Ndikukuyamikani, Inu Yehova; chifukwa ngakhale munandipsera mtima, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mwanditonthoza.
And in that day thou shall say, I will give thanks to thee, O Jehovah, for though thou were angry with me. Thine anger is turned away and thou comfort me.
2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga; ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa.”
Behold, God is my salvation. I will trust, and will not be afraid, for Jehovah, even Jehovah, is my strength and song, and he has become my salvation.
3 Mudzakondwera popeza Yehova ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.
Therefore with joy ye shall draw water out of the wells of salvation.
4 Tsiku limenelo mudzati: “Yamikani Yehova, tamandani dzina lake; mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
And in that day ye shall say, Give thanks to Jehovah. Call upon his name. Declare his doings among the peoples. Make mention that his name is exalted.
5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu; zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.
Sing to Jehovah, for he has done excellent things. Let this be known in all the earth.
6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni; pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”
Cry aloud and shout, thou inhabitant of Zion, for great in the midst of thee is the Holy One of Israel.

< Yesaya 12 >