< Genesis 7 >

1 Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu.
And Jehovah said to Noah, Come, thou and all thy house into the ark, for I have seen thee righteous before me in this generation.
2 Pa mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya utengepo zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi zazikazi zisanu ndi ziwirinso. Koma pa mtundu wa nyama iliyonse yosati nʼkudya utengepo zazimuna ziwiri ndi zazikazi ziwirinso.
Of every clean beast thou shall take to thee by sevens, the male and his female. And of the beasts that are not clean two, the male and his female.
3 Chimodzimodzinso mbalame, utenge zisanu ndi ziwiri zazimuna ndi zisanu ndi ziwiri zazikazi za mtundu uliwonse kuti mitundu yawo isungike ndi moyo pa dziko lonse lapansi.
Also of the birds of the heavens by sevens, male and female, to keep seed alive upon the face of all the earth.
4 Pakapita masiku asanu ndi awiri ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku ndipo ndidzawononga cha moyo chilichonse chimene ndinachipanga pa dziko lapansi.”
For yet seven days, and I will cause it to rain upon the earth forty days and forty nights, and every living thing that I have made I will destroy from off the face of the ground.
5 Ndipo Nowa anachita zonse zimene Yehova anamulamulira.
And Noah did according to all that Jehovah commanded him.
6 Pamene chigumula chinabwera pa dziko lapansi Nowa anali ndi zaka 600.
And Noah was six hundred years old when the flood of waters was upon the earth.
7 Ndipo Nowa, ana ake aamuna, mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aakazi analowa mu chombo chija kuthawa madzi a chigumula.
And Noah went in, and his sons, and his wife, and his sons' wives with him, into the ark, because of the waters of the flood.
8 Nyama zoti nʼkudya ndi nyama zosadyedwa, mbalame, pamodzi ndi nyama zokwawa zonse zinadza kwa Nowa ziwiriziwiri ndi kulowa mʼchombomo.
Of clean beasts, and of beasts that are not clean, and of birds, and of everything that creeps upon the ground,
9 Ndipo Nowa anatenga ziwiriziwiri, yayimuna ndi yayikazi monga anamulamulira Mulungu.
there went in two by two to Noah into the ark, male and female, as God commanded Noah.
10 Patapita masiku asanu ndi awiri chigumula chinabwera pa dziko lapansi.
And it came to pass after the seven days, that the waters of the flood were upon the earth.
11 Pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri, Nowa ali ndi zaka 600, akasupe onse akuya kwambiri anasefuka ndiponso zitseko za madzi akumwamba zinatsekuka.
In the six hundredth year of Noah's life, in the second month, on the seventeenth day of the month, on the same day all the fountains of the great deep were broken up, and the windows of heaven were opened.
12 Ndipo mvula inagwa pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku.
And the rain was upon the earth forty days and forty nights.
13 Linali tsiku lomwelo pamene Nowa ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, pamodzi ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake atatu aja analowa mu chombo.
In the selfsame day Noah, and Shem, and Ham, and Japheth, the sons of Noah, and Noah's wife, and the three wives of his sons with them, entered into the ark,
14 Iwowa analowa mʼchombomo pamodzi ndi nyama iliyonse ya kutchire monga mwa mtundu wake, ziweto zonse monga mwa mitundu yawo, nyama yokwawa iliyonse monga mwa mtundu wake ndi mbalame iliyonse monga mwa mtundu wake.
they, and every beast according to its kind, and all the cattle according to their kind, and every creeping thing that creeps upon the earth according to its kind, and every bird according to its kind, every bird of every sort.
15 Nowa analowa mu chombo muja pamodzi ndi zamoyo zonse.
And they went in to Noah into the ark, two by two of all flesh in which is the breath of life.
16 Iye analowa nazo zazimuna ndi zazikazi monga mmene Mulungu anamulamulira. Kenaka Yehova anatseka pa khomo.
And those that went in, went in male and female of all flesh, as God commanded him. And Jehovah shut him in.
17 Chigumula chinagwa pa dziko la pansi kwa masiku makumi anayi. Madzi anayamba kuchuluka ndipo ananyamula chombo chija ndi kuchiyandamitsa pamwamba pa dziko.
And the flood was forty days upon the earth. And the waters increased, and bore up the ark, and it was lifted up above the earth.
18 Madzi anafika mwamphamvu ndipo anachulukirachulukira pa dziko lapansi moti chombo chinayandama pamwamba pa madziwo.
And the waters prevailed, and increased greatly upon the earth, and the ark went upon the face of the waters.
19 Madzi a chigumula anabwerabe molimbika motero kuti mapiri ataliatali onse a pa dziko anamizidwa.
And the waters prevailed exceedingly upon the earth, and all the high mountains that were under the whole heaven were covered,
20 Madzi anakwera namiza mapiri kwa mamita pafupifupi asanu ndi awiri.
fifteen cubits upward. The waters prevailed, and the mountains were covered.
21 Chamoyo chilichonse choyenda pa dziko lapansi chinafa: mbalame, ziweto, nyama zakuthengo, miyandamiyanda ya zonse zolengedwa za pa dziko lapansi pamodzi ndi anthu.
And all flesh died that moved upon the earth, from birds, to cattle, to beasts, and every creeping thing that creeps upon the earth, and every man.
22 Chilichonse chamoyo, chokhala pa mtunda chinafa.
All in whose nostrils was the breath of the spirit of life, of all that was on the dry land, died.
23 Chamoyo chilichonse pa dziko lapansi chinawonongedwa, kuyambira munthu, nyama, zokwawa ndi mbalame. Nowa yekha ndiye anatsala pamodzi ndi onse amene anali naye.
And every living thing was destroyed that was upon the face of the ground, from man, to cattle, to creeping things, and birds of the heavens, and they were destroyed from the earth. And only Noah was left, and those who were with him in the ark.
24 Madziwo anadzaza dziko lonse lapansi kwa masiku 150.
And the waters prevailed upon the earth a hundred and fifty days.

< Genesis 7 >

The Great Flood
The Great Flood