< Eksodo 10 >

1 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao, pakuti Ine ndawumitsa mtima wake ndi mitima ya nduna zake kuti ndichite zizindikiro zozizwitsa pakati pawo
And Jehovah said to Moses, Go in to Pharaoh, for I have hardened his heart, and the heart of his servants, that I may show these my signs in the midst of them,
2 kuti inu mudzawuze ana ndi zidzukulu zanu za mmene ndinawakhawulitsira Aigupto ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinachita pakati pawo ndiponso kuti inu mudziwe kuti ine ndine Yehova.”
and that thou may tell in the ears of thy son, and of thy son's son, what things I have wrought upon Egypt, and my signs which I have done among them, that ye may know that I am Jehovah.
3 Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze.
And Moses and Aaron went in to Pharaoh, and said to him, Thus says Jehovah, the God of the Hebrews, How long will thou refuse to humble thyself before me? Let my people go, that they may serve me.
4 Ngati ukana kuwalola, ndigwetsa dzombe mʼdziko lako lino mawa.
Else, if thou refuse to let my people go, behold, tomorrow I will bring locusts into thy border.
5 Dzombeli lidzakuta nthaka yonse moti sidzaoneka konse. Lidzadya kalikonse kakangʼono kamene sikanawonongedwe ndi matalala aja, kuphatikizapo mitengo yonse imene ikumera mʼminda yanu.
And they shall cover the face of the earth, so that no man is able to see the ground. And they shall eat the residue of that which is escaped, which remains to you from the hail, and shall eat every tree which grows for you out of the field.
6 Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao.
And thy houses shall be filled, and the houses of all thy servants, and the houses of all the Egyptians, as neither thy fathers nor thy fathers' fathers have seen, since the day that they were upon the earth to this day. And he turned, and went out from Pharaoh.
7 Nduna za Farao zinamufunsa kuti, “Kodi munthu uyu adzativutitsa mpaka liti? Aloleni anthuwa apite, kuti akapembedze Yehova Mulungu wawo. Kodi simukuona kuti dziko la Igupto lawonongeka?”
And Pharaoh's servants said to him, How long shall this man be a snare to us? Let the men go, that they may serve Jehovah their God. Do thou not yet know that Egypt is destroyed?
8 Choncho Mose ndi Aaroni anayitanidwanso kwa Farao ndipo anati, “Pitani kapembedzeni Yehova Mulungu wanu. Koma ndani amene adzapite?”
And Moses and Aaron were brought again to Pharaoh. And he said to them, Go, serve Jehovah your God, but who are those who shall go?
9 Mose anayankha kuti, “Ife tidzapita tonse pamodzi; angʼonoangʼono ndi akuluakulu, ana athu aamuna ndi aakazi, ndiponso ziweto zathu ndi ngʼombe chifukwa tikakhala ndi chikondwerero cha kwa Yehova.”
And Moses said, We will go with our young and with our old, with our sons and with our daughters, with our flocks and with our herds will we go, for we must hold a feast to Jehovah.
10 Farao anati, “Yehova akhale ndi inu ngati ndingakuloleni kupita pamodzi ndi akazi ndi ana anu! Zikuoneka kuti mwakonzeka kuchita choyipa.
And he said to them, So be Jehovah with you, as I will let you go, and your little ones. Look, evil is before you.
11 Ndakana! Amuna okha ndiwo apite ndi kukapembedza Yehova pakuti izi ndi zimene mwakhala mukupempha.” Kenaka Mose ndi Aaroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao.
Not so. Go ye now who are men, and serve Jehovah, for that is what ye desire. And they were driven out from Pharaoh's presence.
12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Igupto kuti dzombe lidze pa dziko la Igupto ndi kuwononga chilichonse chimene chikumera mʼminda ndi chilichonse chimene chinatsala pa nthawi ya matalala.”
And Jehovah said to Moses, Stretch out thy hand over the land of Egypt for the locusts, that they may come up upon the land of Egypt, and eat every herb of the land, even all that the hail has left.
13 Kotero Mose anakweza ndodo yake pa dziko la Igupto, ndipo Yehova anawutsa mphepo ya kummawa imene inawomba pa dziko usana ndi usiku wonse. Mmene kumacha nʼkuti mphepoyo itabweretsa dzombe.
And Moses stretched forth his rod over the land of Egypt, and Jehovah brought an east wind upon the land all that day, and all the night, and when it was morning, the east wind brought the locusts.
14 Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo.
And the locusts went up over all the land of Egypt, and rested in all the borders of Egypt, very grievous were they, before them there were no such locusts as they, neither after them shall be such.
15 Dzombelo linaphimba nthaka yonse mpaka kuoneka kuti bii. Linadya zonse zimene zinatsala nthawi ya matalala, zomera za mʼmunda ndi zipatso. Panalibe chobiriwira chilichonse chimene chinatsala pa mtengo kapena pa chomera chilichonse mʼdziko lonse la Igupto.
For they covered the face of the whole ground, so that the land was darkened, and they ate every herb of the land, and all the fruit of the trees which the hail had left. And there remained not any green thing, either tree nor herb of the field, through all the land of Egypt.
16 Mwamsangamsanga, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Ine ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso inu.
Then Pharaoh called for Moses and Aaron in haste, and he said, I have sinned against Jehovah your God, and against you.
17 Tsopano ndikhululukirenso tchimo langa kano konkha ndipo pempherani kwa Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wosakazawu.”
Now therefore forgive, I pray thee, my sin only this once, and entreat Jehovah your God, that he may only take away from me this death.
18 Mose anachoka kwa Farao nakapemphera kwa Yehova.
And he went out from Pharaoh, and entreated Jehovah.
19 Ndipo Yehova anasintha mphepo ija kuti ikhale ya mphamvu yochokera ku madzulo, ndipo inanyamula dzombe lija nʼkulikankhira mʼNyanja Yofiira. Panalibe dzombe ndi limodzi lomwe limene linatsala mu Igupto.
And Jehovah turned an exceedingly strong west wind, which took up the locusts, and drove them into the Red Sea. There remained not one locust in all the border of Egypt.
20 Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli apite.
But Jehovah hardened Pharaoh's heart, and he did not let the sons of Israel go.
21 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasulira dzanja lako kumwamba kuti kukhale mdima umene udzaphimba dziko lonse la Igupto, mdima wandiweyani.”
And Jehovah said to Moses, Stretch out thy hand toward heaven, that there may be darkness over the land of Egypt, even darkness which may be felt.
22 Choncho Mose anakweza dzanja lake kumwamba ndipo mdima wandiweyani unaphimba dziko lonse la Igupto kwa masiku atatu.
And Moses stretched forth his hand toward heaven, and there was a thick darkness in all the land of Egypt three days,
23 Palibe amene anatha kuona mnzake kapena kuchoka pa khomo pake kwa masiku atatu. Koma kumalo kumene kumakhala Aisraeli kunali kowala.
they did not see each other, neither did anyone rise from his place for three days, but all the sons of Israel had light in their dwellings.
24 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kapembedzeni Yehova. Ngakhale akazi ndi ana anu apite pamodzi ndi inu. Koma musatenge ziweto zanu ndi ngʼombe zanu.”
And Pharaoh called to Moses, and said, Go ye, serve Jehovah, only let your flocks and your herds stay. Let your little ones also go with you.
25 Koma Mose anati, “Ndiye inu mutipatse nsembe zopsereza zoti tikapereke kwa Yehova Mulungu wathu.
And Moses said, Thou must also give into our hand sacrifices and burnt offerings, that we may sacrifice to Jehovah our God.
26 Koma ayi, ife tipita ndi ziweto zathu. Palibe chiweto chilichonse chimene chitatsale kuno, popeza tikasankha komweko ziweto zokapembedzera Yehova. Sitingadziwe zimene tikagwiritse ntchito popembedza Yehova mpaka titakafika kumeneko.”
Our cattle shall also go with us, there shall not a hoof be left behind, for we must take of it to serve Jehovah our God, and we do not know with what we must serve Jehovah, until we come there.
27 Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo sanafune kuwalola kuti apite.
But Jehovah hardened Pharaoh's heart, and he would not let them go.
28 Farao anati kwa Mose, “Choka pamaso panga! Uwonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga! Tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.”
And Pharaoh said to him, Get thee from me. Take heed to thyself, see my face no more, for in the day thou see my face thou shall die.
29 Mose anayankha kuti, “Monga momwe mwaneneramu, Ine sindidzaonekeranso pamaso panu.”
And Moses said, Thou have spoken well. I will see thy face again no more.

< Eksodo 10 >