+ Genesis 1 >

1 Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.
In the beginning God created the heavens and the earth.
2 Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.
And the earth was without form and void, and darkness was upon the face of the deep, and the Spirit of God moved upon the face of the waters.
3 Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi.
And God said, Let there be light, and there was light.
4 Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.
And God saw the light, that it was good. And God divided the light from the darkness.
5 Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.
And God called the light Day, and the darkness he called Night. And there was evening and there was morning, one day.
6 Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.”
And God said, Let there be a firmament in the midst of the waters, and let it divide the waters from the waters.
7 Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi.
And God made the firmament, and divided the waters which were under the firmament from the waters which were above the firmament. And it was so.
8 Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri.
And God called the firmament Heaven. And there was evening and there was morning, a second day.
9 Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi.
And God said, Let the waters under the heavens be gathered together to one place, and let the dry land appear. And it was so.
10 Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
And God called the dry land Earth, and he called the gathering together of the waters Seas. And God saw that it was good.
11 Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi.
And God said, Let the earth put forth grass, herbs yielding seed, and fruit trees bearing fruit according to their kind (in which is the seed of them) upon the earth. And it was so.
12 Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
And the earth brought forth grass, herbs yielding seed according to their kind, and trees bearing fruit in which is the seed of it, according to their kind. And God saw that it was good.
13 Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachitatu.
And there was evening and there was morning, a third day.
14 Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka;
And God said, Let there be lights in the firmament of heaven to divide the day from the night, and let them be for signs, and for seasons, and for days and years.
15 zikhale kuthambo kuti ziwunikire pa dziko lapansi. Ndipo zinachitikadi.”
And let them be for lights in the firmament of heaven to give light upon the earth. And it was so.
16 Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi.
And God made the two great lights, the greater light to rule the day, and the lesser light to rule the night, also the stars.
17 Mulungu anaziyika mlengalenga kuti ziziwunikira pa dziko lapansi,
And God set them in the firmament of heaven to give light upon the earth,
18 kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino.
and to rule over the day and over the night, and to divide the light from the darkness. And God saw that it was good.
19 Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachinayi.
And there was evening and there was morning, a fourth day.
20 Mulungu anati, “Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.”
And God said, Let the waters swarm with swarms of living creatures, and let birds fly above the earth in the open firmament of heaven.
21 Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino.
And God created the great sea creatures, and every living creature that moves, which the waters brought forth abundantly, according to their kind, and every winged bird according to its kind. And God saw that it was good.
22 Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.”
And God blessed them, saying, Be fruitful, and multiply, and fill the waters in the seas, and let birds multiply on the earth.
23 Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachisanu.
And there was evening and there was morning, a fifth day.
24 Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi.
And God said, Let the earth bring forth living creatures according to their kind, cattle, and creeping things, and beasts of the earth according to their kind. And it was so.
25 Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
And God made the beasts of the earth according to their kind, and the cattle according to their kind, and everything that creeps upon the ground according to its kind. And God saw that it was good.
26 Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”
And God said, Let us make mankind in our image-after our likeness-and let them have dominion over the fish of the sea, and over the birds of the heavens, and over the cattle, and over all the earth, and over every creeping thing that creeps upon the earth.
27 Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.
And God created mankind in his own image, in the image of God he created him, male and female he created them.
28 Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”
And God blessed them. And God said to them, Be fruitful, and multiply, and fill the earth, and have power over it, and have dominion over the fish of the sea, and over the birds of the heavens, and over every living thing that moves upon the earth.
29 Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu.
And God said, Behold, I have given you every herb yielding seed, which is upon the face of all the earth, and every tree, in which is the fruit of a tree yielding seed. To you it shall be for food,
30 Ndaperekanso msipu kwa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimakwawa, chilichonse chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinachitikadi.
and to every beast of the earth, and to every bird of the heavens, and to everything that creeps upon the earth in which there is life, for food-every green herb. And it was so.
31 Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
And God saw everything that he had made, and, behold, it was very good. And there was evening and there was morning, the sixth day.

+ Genesis 1 >