< 2 Samueli 14 >

1 Yowabu mwana wa Zeruya anadziwa kuti maganizo a mfumu ali pa Abisalomu.
Now Joab the son of Zeruiah perceived that the king's heart was toward Absalom.
2 Kotero Yowabu anatuma munthu wina kupita ku Tekowa ndi kukatengako mkazi wanzeru. Yowabu anati kwa mkaziyo, “Ukhale ngati namfedwa. Uvale zovala zaumasiye ndipo usadzole mafuta ena aliwonse. Ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira masiku ambiri.
And Joab sent to Tekoa, and fetched from there a wise woman, and said to her, I pray thee, feign thyself to be a mourner, and put on mourning apparel, I pray thee, and do not anoint thyself with oil, but be as a woman who has a long time mourned for the dead.
3 Kenaka upite kwa mfumu ndipo ukayankhule mawu awa.” Ndipo Yowabu anamuwuza mawu oti akanene.
And go in to the king, and speak on this manner to him. So Joab put the words in her mouth.
4 Mkazi wochokera ku Tekowa uja atapita kwa mfumu anadzigwetsa pansi, napereka ulemu kwa mfumu nati, “Thandizeni mfumu!”
And when the woman of Tekoa spoke to the king, she fell on her face to the ground, and did obeisance, and said, Help, O king.
5 Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi chikukusautsa iwe nʼchiyani?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira.
And the king said to her, What troubles thee? And she answered, Of a truth I am a widow, and my husband is dead.
6 Ine wantchito wanu ndinali ndi ana aamuna awiri. Iwo anayamba kumenyana mʼmunda, ndipo panalibe woti awaleretse. Wina anakantha mnzakeyo mpaka kumupha.
And thy handmaid had two sons, and they two strove together in the field, and there was none to part them, but the one smote the other, and killed him.
7 Tsono banja lonse landiwukira ine, wantchito wanu. Iwo akuti, ‘Utipatse mwana amene anakantha mʼbale wakeyo kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mʼbale wake amene anaphedwayo. Ife tidzaphanso mlowamʼmalo.’ Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.”
And, behold, the whole family is risen against thy handmaid, and they say, Deliver him who smote his brother that we may kill him for the life of his brother whom he killed, and so destroy the heir also. Thus they will quench my coal which is left, and will leave to my husband neither name nor remainder upon the face of the earth.
8 Mfumu inati kwa mkaziyo, “Pitani ku nyumba kwanu ndipo ine ndidzalamula mʼmalo mwanu.”
And the king said to the woman, Go to thy house, and I will give charge concerning thee.
9 Koma mkazi wochokera ku Tekowayo anati kwa mfumu, “Mbuye wanga mfumu, kulakwa kukhale pa ine ndi banja la abambo anga ndipo mfumu ndi mpando wanu waufumu mukhale osalakwa.”
And the woman of Tekoa said to the king, My lord, O king, the iniquity be on me, and on my father's house, and the king and his throne be guiltless.
10 Mfumu inayankha kuti, “Ngati wina aliyense anene kanthu kwa iwe, umubweretse kwa ine, ndipo sadzakuvutitsanso.”
And the king said, Whoever says anything to thee, bring him to me, and he shall not touch thee any more.
11 Mkaziyo anati, “Mfumu ipemphe kwa Yehova Mulungu wake kuti aletse wobwezera imfa asaphenso wina kuti mwana wanga asawonongedwe.” Mfumu inati, “Pali Yehova wamoyo ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pa mwana wako silidzathotholedwa.”
Then she said, I pray thee, let the king remember Jehovah thy God, that the avenger of blood not destroy any more, lest they destroy my son. And he said, As Jehovah lives, there shall not one hair of thy son fall to the earth.
12 Kenaka mkaziyo anati, “Lolani kuti wantchito wanu ayankhule mawu kwa inu mbuye wanga mfumu.” Iye anayankha kuti, “Yankhula.”
Then the woman said, Let thy handmaid, I pray thee, speak a word to my lord the king. And he said, Say on.
13 Mkaziyo anati, “Nʼchiyani tsono chimene mwaganiza kuchitira zimenezi anthu a Mulungu? Pamene mfumu yanena izi, kodi sikudzitsutsa yokha, pakuti mfumu sinayitanitse mwana amene anamupirikitsa?
And the woman said, Why then have thou devised such a thing against the people of God? For in speaking this word the king is as he who is guilty, in that the king does not fetch home again his banished one.
14 Koma poti madzi akatayika sawoleka, ndiye tonsefe tiyenera kufa ndithu. Koma Mulungu safuna kuti moyo wa munthu utayike kotero anakonza njira yakuti wopirikitsidwayo asakhale wotayikiratu.
For we must die, and are as water split on the ground, which cannot be gathered up again, neither does God take away life, but devises means that he who is banished be not an outcast from him.
15 “Tsopano ine ndabwera kudzanena izi kwa inu mbuye wanga mfumu chifukwa anthu andichititsa mantha. Mdzakazi wanu anaganiza kuti, ‘Ndikayankhula kwa mfumu, mwina adzachita zimene mdzakazi wake adzamupempha.
Now therefore seeing that I have come to speak this word to my lord the king, it is because the people have made me afraid. And thy handmaid said, I will now speak to the king. It may be that the king will perform the request of his servant.
16 Mwina mfumu idzavomereza kupulumutsa mdzakazi wake mʼdzanja la munthu amene akufuna kupha ine pamodzi ndi mwana wanga kutichotsa pa cholowa chimene Mulungu anatipatsa.’
For the king will hear to deliver his servant out of the hand of the man who would destroy me and my son together out of the inheritance of God.
17 “Ndipo tsopano mtumiki wanu akuti, ‘Lolani mawu a mbuye wanga mfumu abweretse mpumulo kwa ine, pakuti mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu pozindikira chabwino ndi choyipa. Yehova Mulungu wanu akhale nanu.’”
Then thy handmaid said, Let, I pray thee, the word of my lord the king be gracious, for as an agent of God, so is my lord the king to discern good and bad. And Jehovah thy God be with thee.
18 Kenaka mfumu inati kwa mkaziyo, “Usandibisire chilichonse pondiyankha chimene ndidzakufunsa.” Mkaziyo anati, “Mbuye wanga mfumu yankhulani.”
Then the king answered and said to the woman, Hide not from me, I pray thee, anything that I shall ask thee. And the woman said, Let my lord the king now speak.
19 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi zimenezi sukuchita motsogozedwa ndi Yowabu?” Mkaziyo anayankha kuti, “Pali inu wamoyo, mbuye wanga mfumu, palibe munthu angakhotere kumanja kapena kumanzere pa chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mwanena. Inde, ndi mtumiki wanu Yowabu amene wandilangiza ine kuchita zimenezi ndipo ndi amene anandipatsa mawu onsewa woti ine mtumiki wanu ndiyankhule.
And the king said, Is the hand of Joab with thee in all this? And the woman answered and said, As thy soul lives, my lord the king, none can turn to the right hand or to the left from anything that my lord the king has spoken, for thy servant Joab, he bade me, and he put all these words in the mouth of thy handmaid.
20 Mtumiki wanu Yowabu anachita zimenezi kuti asinthe mmene zinthu zilili lero. Mbuye wanga muli ndi nzeru ngati za mngelo wa Mulungu. Mumadziwa zonse zimene zikuchitika mʼdziko.”
Thy servant Joab has done this thing to change the face of the matter. And my lord is wise, according to the wisdom of an agent of God, to know all things that are on the earth.
21 Mfumu inati kwa Yowabu, “Chabwino, ine ndichita zimenezi. Pita kamutenge Abisalomuyo.”
And the king said to Joab, Behold now, I have done this thing. Go therefore, bring the young man Absalom back.
22 Yowabu anawerama pansi kupereka ulemu kwa mfumu. Yowabuyo anati, “Lero mtumiki wanu wadziwa kuti wapeza chifundo pamaso panu, mbuye wanga mfumu, chifukwa mwavomera pempho lakeli.”
And Joab fell to the ground on his face, and did obeisance, and blessed the king. And Joab said, Today thy servant knows that I have found favor in thy sight, my lord, O king, in that the king has performed the request of his servant.
23 Choncho Yowabu anapita ku Gesuri ndipo anamubweretsa Abisalomu ku Yerusalemu.
So Joab arose and went to Geshur, and brought Absalom to Jerusalem.
24 Koma mfumu inati, “Iye apite ku nyumba yake; asaone nkhope yanga.” Kotero Abisalomu anapita ku nyumba yake ndipo sanakumane ndi mfumu.
And the king said, Let him turn to his own house, but let him not see my face. So Absalom turned to his own house, and did not see the king's face.
25 Mʼdziko lonse la Israeli munalibe munthu amene anayamikidwa chifukwa cha maonekedwe ake wokongola ngati Abisalomu. Kuyambira kumutu mpaka ku mapazi ake, analibe chilema.
Now in all Israel there was none to be so much praised as Absalom for his beauty; from the sole of his foot even to the crown of his head there was no blemish in him.
26 Nthawi ina iliyonse akamameta tsitsi lake, ankameta pamene layamba kumulemera. Akatero amaliyeza, ndipo limalemera makilogalamu awiri pa sikelo yaufumu.
And when he cut the hair of his head (now it was at every year's end that he cut it, because it was heavy on him, therefore he cut it), he weighed the hair of his head at two hundred shekels, after the king's weight.
27 Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu ndi wamkazi mmodzi. Mwana wamkazi dzina lake linali Tamara, ndipo anali mkazi wokongola kwambiri.
And to Absalom there were born three sons, and one daughter whose name was Tamar. She was a woman of a fair countenance.
28 Abisalomu anakhala zaka ziwiri mu Yerusalemu osaonekera kwa mfumu.
And Absalom dwelt two full years in Jerusalem, and he did not see the king's face.
29 Kenaka Abisalomu anatumiza mawu kwa Yowabu, kumutuma kuti apite kwa mfumu, koma Yowabu anakana kubwera. Kotero anatumizanso mawu kachiwiri, koma Yowabu anakananso.
Then Absalom sent for Joab to send him to the king, but he would not come to him. And he sent again a second time, but he would not come.
30 Tsono Abisalomu anati kwa antchito ake, “Taonani, munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga ndipo muli barele mʼmenemo. Pitani mukawutenthe mundawo.” Ndipo antchito a Abisalomu anawutentha mundawo.
Therefore he said to his servants, See, Joab's field is near mine, and he has barley there. Go and set it on fire. And Absalom's servants set the field on fire.
31 Ndipo Yowabu anapita ku nyumba ya Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani antchito ako atentha munda wanga?”
Then Joab arose, and came to Absalom to his house, and said to him, Why have thy servants set my field on fire?
32 Abisalomu anati kwa Yowabu, “Taona, ine ndinatumiza mawu kwa iwe ndipo ndinati, ‘Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ine ndinabwera kuchokera ku Gesuri? Zikanakhala bwino ndikanakhala komweko!’ Tsono pano ndikufuna kuonana ndi mfumu, ndipo ngati ndili olakwa mfumuyo indiphe.’”
And Absalom answered Joab, Behold, I sent to thee, saying, Come here, that I may send thee to the king to say, Why have I come from Geshur? It were better for me to still be there. Now therefore let me see the king's face, and if there be iniquity in me, let him kill me.
33 Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anayiwuza zimenezi. Ndipo mfumu inamuyitanitsa Abisalomu, ndipo analowa nawerama kugunditsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu. Tsono mfumu inapsompsona Abisalomu.
So Joab came to the king, and told him. And when he had called for Absalom, he came to the king, and bowed himself on his face to the ground before the king. And the king kissed Absalom.

< 2 Samueli 14 >