Preface
Read
+
Publisher
Nainoia, Inc.
PO Box 462, Bellefonte, PA 16823
(814) 470-8028
Nainoia Inc, Publisher
LinkedIn/NAINOIA-INC
Third Party Publisher Resources
Request Custom Formatted Verses
Please contact us below
Submit your proposed corrections
I understand that the Aionian Bible republishes public domain and Creative Commons Bible texts and that volunteers may be needed to present the original text accurately. I also understand that apocryphal text is removed and most variant verse numbering is mapped to the English standard. I have entered my corrections under the verse(s) below. Proposed corrections to the Chichewa Bible, Hosea Chapter 8 https://www.AionianBible.org/Bibles/Chichewa---Chichewa-Bible/Hosea/8 1) “Ika lipenga pakamwa pako. Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova chifukwa anthu aphwanya pangano langa ndiponso agalukira lamulo langa. 2) Israeli akulirira kwa Ine kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’ 3) Koma Israeli wakana zabwino; mdani adzamuthamangitsa. 4) Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amasankha akalonga popanda chilolezo changa. Amadzipangira mafano asiliva ndi agolide koma adzawonongeka nawo. 5) Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe! Mkwiyo wanga wayakira anthuwo. Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima? 6) Mafanowa ndi ochokera ku Israeli! Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso; si Mulungu amene anamupanga. Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa, mwana wangʼombe wa ku Samariya. 7) “Aisraeli amadzala mphepo ndipo amakolola kamvuluvulu. Tirigu alibe ngala; sadzabala chakudya. Akanabala chakudya alendo akanadya chakudyacho. 8) Israeli wamezedwa, tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina ngati chinthu cha chabechabe. 9) Pakuti iwo anapita ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha. Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake. 10) Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu, Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi. Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu. 11) “Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo, maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo. 12) Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga, koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo. 13) Amapereka nsembe za nyama kwa Ine ndipo iwo amadya nyamayo, koma Yehova sakondwera nazo. Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo: iwowo adzabwerera ku Igupto. 14) Israeli wayiwala Mlengi wake ndipo wamanga nyumba zaufumu; Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga. Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo, moto umene udzatenthe malinga awo.” Additional comments?
Refresh Captcha
The world's first Holy Bible un-translation!