< До євреїв 4 >

1 Отже, біймося, коли зостається обітниця вхо́ду до Його́ відпочинку, щоб не виявилось, що хтось із вас опізни́вся.
Popeza lonjezo lakuti tidzalowe mu mpumulo umene anatilonjeza lilipobe, tiyeni tisamale kuti pasakhale wina aliyense mwa inu wodzalephera kulowamo.
2 Бо Єва́нгелія була звіщена нам, як і тим. Але не прине́сло пожитку їм слово почуте, бо воно не злучилося з вірою слухачів.
Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira.
3 Бо до Його́ відпочинку вхо́димо ми, що ввірували, як Він провістив: „Я присяг був у гніві Своїм, що до місця Мого відпочинку не вві́йдуть вони“, хоч діла Його були вчи́нені від закла́дин світу.
Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti, “Ndili wokwiya ndinalumbira kuti, ‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’” Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi.
4 Бо колись про день сьомий сказав Він отак: „І Бог відпочив сьомого дня від усієї праці Своєї“.
Pena pake wayankhula za tsiku lachisanu ndi chiwiri mʼmawu awa: “Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, Mulungu anapumula ku ntchito zake zonse.”
5 А ще тут: „До Мого відпочинку не вві́йдуть вони“!
Pa ndime inonso akunena za zomwezo pamene akuti, “Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.”
6 Коли ж залиша́ється ото, що деякі ввійдуть до нього, а ті, кому Єва́нгелія була перше зві́щена, не ввійшли за непо́слух,
Popeza kwatsalabe kuti ena adzalowe mu mpumulowo, koma aja anayamba kumva Uthenga Wabwino sanalowe chifukwa cha kusamvera kwawo.
7 то ще призначає Він деякий день, — „сьогодні“, бо через Давида говорить по такім довгім ча́сі, як вище вже сказано: „Сьогодні, як голос Його ви почуєте, не робіть затверді́лими ваших серде́ць“!
Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti, “Lero mukamva mawu ake, musawumitse mitima yanu.”
8 Бо коли б Ісус ( Навин ) дав їм відпочинок, то про інший день не казав би по цьо́му.
Ngati Yoswa akanalowetsa anthu mu mpumulo, Mulungu sakananena pambuyo pake za tsiku lina.
9 Отож, людові Божому залиша́ється субо́тство, спочи́нок.
Kotero tsono kwatsala mpumulo wa Sabata kwa anthu a Mulungu;
10 Хто бо ввійшов був у Його відпочинок, то й той відпочив від учинків своїх, як і Бог від Своїх.
Pakuti aliyense amene analowa mu mpumulo wa Mulungu anapuma pa ntchito zake, monga momwe Mulungu anachitira.
11 Отож, попильнуймо ввійти до того відпочинку, щоб ніхто не потра́пив у непо́слух за при́кладом тим.
Tiyeni tsono tiyesetse kulowa mu mpumulo, kuti pasapezeke wina aliyense wolephera potsatira chitsanzo chawo cha kusamvera.
12 Бо Боже Слово живе та дія́льне, гостріше від усякого меча обосічного, — прохо́дить воно аж до поділу душі й духа, сугло́бів та мо́зків, і спосібне судити думки́ та на́міри се́рця.
Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.
13 I немає створі́ння, щоб сховалось перед Ним, але́ все наге́ та відкрите перед очима Його, — Йому дамо звіт!
Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
14 Отож, мавши великого Первосвященика, що небо перейшов, Ісуса, Сина Божого, трима́ймося визнання нашого!
Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza.
15 Бо ми маємо не такого Первосвященика, що не міг би співчувати слабостям нашим, але ви́пробуваного в усьому, подібно до нас, окрім гріха.
Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.
16 Отож, приступаймо з відвагою до престолу благода́ті, щоб прийняти милість та для своєчасної допомо́ги знайти благода́ть.
Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.

< До євреїв 4 >