< Иакова 4 >

1 Откуда у вас вражды и распри? Не отсюда ли, от вожделений ваших, воюющих в членах ваших?
Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu?
2 Желаете - и не имеете; убиваете и завидуете - и не можете достигнуть; препираетесь и враждуете - и не имеете, потому что не просите.
Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.
3 Просите и не получаете, потому что просите не на добро, а чтобы употребить для ваших вожделений.
Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.
4 Прелюбодеи и прелюбодейцы! Не знаете ли, что дружба с миром есть вражда против Бога? Итак, кто хочет быть другом миру, тот становится врагом Богу.
Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu.
5 Или вы думаете, что напрасно говорит Писание: “До ревности любит дух, живущий в нас”?
Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife?
6 Но тем большую дает благодать; посему и сказано: Бог гордым противится, а смиренным дает благодать.
Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”
7 Итак покоритесь Богу; противостаньте диаволу, и убежит от вас.
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.
8 Приблизьтесь к Богу, и приблизится к вам; очистите руки, грешники, исправьте сердца, двоедушные.
Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.
9 Сокрушайтесь, плачьте и рыдайте; смех ваш да обратится в плач и радость - в печаль.
Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni.
10 Смиритесь пред Господом, и вознесет вас.
Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.
11 Не злословьте друг друга, братия: кто злословит брата или судит брата своего, того злословит закон и судит закон; а если ты судишь закон, то ты не исполнитель закона, но судья.
Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza.
12 Един Законодатель и Судия, могущий спасти и погубить; а ты кто, который судишь другого?
Pali mmodzi yekha Wopereka Malamulo ndi Woweruza. Ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga. Kodi ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?
13 Теперь послушайте вы, говорящие: “Сегодня или завтра отправимся в такой-то город, и проживем там один год, и будем торговать и получать прибыль”;
Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.”
14 вы, которые не знаете, что случится завтра: ибо что такое жизнь ваша? пар, являющийся на малое время, а потом исчезающий.
Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira.
15 Вместо того, чтобы вам говорить: если угодно будет Господу и живы будем, то сделаем то или другое, -
Koma inuyo muyenera kunena kuti, “Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti.”
16 вы, по своей надменности, тщеславитесь: всякое такое тщеславие есть зло.
Koma mmene zililimu mumangodzitama ndi kudzikuza. Kudzitama konse kotereku ndi koyipa.
17 Итак, кто разумеет делать добро и не делает, тому грех.
Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.

< Иакова 4 >