< К Евреям 1 >

1 Бог, многократно и многообразно говоривший издревле отцам в пророках,
Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri.
2 В последние дни сии говорил нам в Сыне, Которого поставил наследником всего, чрез Которого и веки сотворил. (aiōn g165)
Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. (aiōn g165)
3 Сей, будучи сияние славы и образ ипостаси Его и держа все словом силы Своей, совершив собою очищение грехов наших, воссел одесную (престола) величия на высоте,
Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
4 Будучи столько превосходнее Ангелов, сколько славнейшее пред ними наследовал имя.
Mwanayu ndi wamkulu koposa angelo, monga momwe dzina limene analandira limaposa dzina la angelo.
5 Ибо кому когда из Ангелов сказал Бог: “Ты сын мой, Я ныне родил Тебя?” И еще: “Я буду Ему Отцом, и Он будет Мне Сыном”?
Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati, “Iwe ndiwe mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.” Kapena kunenanso kuti, “Ine ndidzakhala abambo ake; iye adzakhala mwana wanga.”
6 Также, когда вводит Первородного во вселенную, говорит: “и да поклонятся Ему все Ангелы Божии”.
Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati, “Angelo onse a Mulungu amupembedze Iye.”
7 Об Ангелах сказано: “Ты творишь Ангелами Своими духов и служителями Своими пламенеющий огонь”.
Iye ponena za angelo akuti, “Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo, amasandutsa atumiki ake malawi amoto.”
8 А о Сыне: “Престол Твой Боже, в век века; жезл царствия Твоего - жезл правоты. (aiōn g165)
Koma za Mwana wake akuti, “Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya, ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu. (aiōn g165)
9 Ты возлюбил правду и возненавидел беззакония; посему помазав Тебя, Боже, Бог твой елеем радости более соучастников твоих”.
Mwakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa; Nʼchifukwa chake, Mulungu wanu wakukwezani kuposa anzanu pokudzozani mafuta osonyeza chimwemwe.”
10 И: “В начале Ты, Господи, основал землю, и небеса - дело рук Твоих;
Mulungu akutinso, “Ambuye, pachiyambi Inu munayika maziko a dziko lapansi; ndipo zakumwambako ndi ntchito za manja anu.
11 Они погибнут, а ты пребываешь; и все обветшают как риза,
Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu wachikhalire. Izo zidzatha ngati zovala.
12 И как одежду свернешь их, и изменятся; но Ты тот же, и лета Твои не кончатся”.
Mudzazipindapinda ngati chofunda; ndipo zidzasinthidwa ngati chovala. Koma Inu simudzasintha, ndipo zaka zanu sizidzatha.”
13 Кому когда из Ангелов сказал Бог: “Седи одесную Меня, доколе положу врагов Твоих в подножие ног Твоих”?
Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti, “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditapanga adani ako kukhale chopondapo mapazi ako.”
14 Не все ли они суть служебные духи, посылаемые на служение для тех, которые имеют наследовать спасение?
Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?

< К Евреям 1 >