< Екклесиаст 9 >

1 На все это я обратил сердце мое для исследования, что праведные и мудрые и деяния их - в руке Божией, и что человек ни любви, ни ненависти не знает во всем том, что перед ним.
Ndinalingalira zonse ndanenazi ndipo ndinapeza kuti anthu olungama ndi anthu anzeru ali mʼmanja mwa Mulungu pamodzi ndi zimene amachita, koma palibe amene amadziwa zimene zikumudikira mʼtsogolo mwake, kaya chikondi kapena chidani.
2 Всему и всем - одно: одна участь праведнику и нечестивому, доброму и злому, чистому и нечистому, приносящему жертву и не приносящему жертвы; как добродетельному, так и грешнику; как клянущемуся, так и боящемуся клятвы.
Onsewa mathero awo ndi amodzi, anthu olungama ndi anthu oyipa, abwino ndi oyipa, oyera ndi odetsedwa, amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe. Zomwe zimachitikira munthu wabwino, zimachitikiranso munthu wochimwa, zomwe zimachitikira amene amalumbira, zimachitikiranso amene amaopa kulumbira.
3 Это-то и худо во всем, что делается под солнцем, что одна участь всем, и сердце сынов человеческих исполнено зла, и безумие в сердце их, в жизни их; а после того они отходят к умершим.
Choyipa chimene chili mʼzonse zochitika pansi ndi ichi: Mathero a zonse ndi amodzi. Ndithu, mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoyipa, ndipo mʼmitima mwawo muli zamisala pamene ali ndi moyo, potsiriza pake iwo amakakhala pamodzi ndi anthu akufa.
4 Кто находится между живыми, тому есть еще надежда, так как и псу живому лучше, нежели мертвому льву.
Aliyense amene ali ndi moyo amakhala ndi chiyembekezo, pajatu galu wamoyo aposa mkango wakufa!
5 Живые знают, что умрут, а мертвые ничего не знают, и уже нет им воздаяния, потому что и память о них предана забвению,
Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa kanthu; alibe mphotho ina yowonjezera, ndipo palibe amene amawakumbukira.
6 и любовь их и ненависть их и ревность их уже исчезли, и нет им более части во веки ни в чем, что делается под солнцем.
Chikondi chawo, chidani chawo ndiponso nsanje yawo, zonse zinatha kalekale; sadzakhalanso ndi gawo pa zonse zochitika pansi pano.
7 Итак иди, ешь с весельем хлеб твой, и пей в радости сердца вино твое, когда Бог благоволит к делам твоим.
Pita, kadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti tsopano Mulungu akukondwera ndi zochita zako.
8 Да будут во всякое время одежды твои светлы, и да не оскудевает елей на голове твоей.
Uzivala zovala zoyera nthawi zonse, uzidzola mafuta mʼmutu mwako nthawi zonse.
9 Наслаждайся жизнью с женою, которую любишь, во все дни суетной жизни твоей, и которую дал тебе Бог под солнцем на все суетные дни твои; потому что это - доля твоя в жизни и в трудах твоих, какими ты трудишься под солнцем.
Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano.
10 Все, что может рука твоя делать, по силам делай; потому что в могиле, куда ты пойдешь, нет ни работы, ни размышления, ни знания, ни мудрости. (Sheol h7585)
Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru. (Sheol h7585)
11 И обратился я, и видел под солнцем, что не проворным достается успешный бег, не храбрым - победа, не мудрым - хлеб, и не у разумных - богатство, и не искусным - благорасположение, но время и случай для всех их.
Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano: opambana pa kuthamanga si aliwiro, kapena opambana pa nkhondo si amphamvu, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru, kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri, kapena okomeredwa mtima si ophunzira; koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake.
12 Ибо человек не знает своего времени. Как рыбы попадаются в пагубную сеть, и как птицы запутываются в силках, так сыны человеческие уловляются в бедственное время, когда оно неожиданно находит на них.
Kungoti palibe munthu amene amadziwa kuti nthawi yake idzafika liti: monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde, kapena mmene mbalame zimakodwera mu msampha, chimodzimodzinso anthu amakodwa mu msampha pa nthawi yoyipa, pamene tsoka limawagwera mosayembekezera.
13 Вот еще какую мудрость видел я под солнцем, и она показалась мне важною:
Ine ndinaonanso pansi pano chitsanzo ichi cha nzeru chimene chinandikhudza kwambiri:
14 город небольшой, и людей в нем немного; к нему подступил великий царь и обложил его и произвел против него большие осадные работы;
Panali mzinda waungʼono umene unali ndi anthu owerengeka. Ndipo mfumu yamphamvu inabwera kudzawuthira nkhondo, inawuzungulira ndi kumanga mitumbira yankhondo.
15 но в нем нашелся мудрый бедняк, и он спас своею мудростью этот город; и однако же никто не вспоминал об этом бедном человеке.
Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo.
16 И сказал я: мудрость лучше силы, и однако же мудрость бедняка пренебрегается, и слов его не слушают.
Choncho ine ndinati, “Nzeru ndi yopambana mphamvu.” Koma nzeru ya munthu wosauka imanyozedwa, ndipo palibe amene amalabadirako za mawu ake.
17 Слова мудрых, высказанные спокойно, выслушиваются лучше, нежели крик властелина между глупыми.
Mawu oyankhula mofatsa a munthu wanzeru, anthu amawasamalira kwambiri kupambana kufuwula kwa mfumu ya zitsiru.
18 Мудрость лучше воинских орудий; но один погрешивший погубит много доброго.
Nzeru ndi yabwino kupambana zida zankhondo, koma wochimwa mmodzi amawononga zinthu zambiri zabwino.

< Екклесиаст 9 >