< 1-е Тимофею 3 >

1 Верно слово: если кто епископства желает, доброго дела желает.
Mawu woona ndi awa: Ngati munthu akufunitsitsa atakhala woyangʼanira, ndiye kuti akufuna ntchito yabwino.
2 Но епископ должен быть непорочен, одной жены муж, трезв, целомудрен, благочинен, честен, страннолюбив, учителен,
Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa.
3 не пьяница, не бийца, не сварлив, не корыстолюбив, но тих, миролюбив, не сребролюбив,
Asakhale chidakwa, asakhale wandewu, koma wofatsa, asakhale wokonda mikangano, kapena wokonda ndalama.
4 хорошо управляющий домом своим, детей содержащий в послушании со всякою честностью;
Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni.
5 ибо, кто не умеет управлять собственным домом, тот будет ли пещись о Церкви Божией?
(Ngati munthu sadziwa kusamala banja lake lomwe, angathe bwanji kusamala mpingo wa Mulungu?)
6 Не должен быть из новообращенных, чтобы не возгордился и не подпал осуждению с диаволом.
Asakhale wongotembenuka mtima kumene kuopa kuti angadzitukumule napezeka pa chilango monga Satana.
7 Надлежит ему также иметь доброе свидетельство от внешних, чтобы не впасть в нарекание и сеть диавольскую.
Ayeneranso kukhala munthu wambiri yabwino ndi akunja, kuti anthu asamutonze nagwa mu msampha wa Satana.
8 Диаконы также должны быть честны, не двоязычны, не пристрастны к вину, не корыстолюбивы,
Momwemonso atumiki, akhale anthu oyenera ulemu, woona mtima, osakhala okonda zoledzeretsa, osakonda kupeza zinthu mwachinyengo.
9 хранящие таинство веры в чистой совести.
Ayenera kugwiritsa mozama choonadi cha chikhulupiriro ndi kukhala ndi chikumbumtima chabwino.
10 И таких надобно прежде испытывать, потом, если беспорочны, допускать до служения.
Ayambe ayesedwa kaye, ndipo ngati palibe kanthu kowatsutsa, aloleni akhale atumiki.
11 Равно и жены их должны быть честны, не клеветницы, трезвы, верны во всем.
Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse.
12 Диакон должен быть муж одной жены, хорошо управляющий детьми и домом своим.
Mtumiki akhale wokhulupirika kwa mkazi wake ndipo ayenera kukhala wosamalira bwino ana ake ndi onse a pa khomo pake.
13 Ибо хорошо служившие приготовляют себе высшую степень и великое дерзновение в вере во Христа Иисуса.
Iwo amene atumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndipo amakhala chitsimikizo chachikulu cha chikhulupiriro chawo mwa Khristu Yesu.
14 Сие пишу тебе, надеясь вскоре придти к тебе,
Ngakhale ndili ndi chiyembekezo choti ndifika komweko posachedwapa, ndikukulemberani malangizo awa.
15 чтобы, если замедлю, ты знал, как должно поступать в доме Божием, который есть Церковь Бога живаго, столп и утверждение истины.
Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi.
16 И беспрекословно - великая благочестия тайна: Бог явился во плоти, оправдал Себя в Духе, показал Себя Ангелам, проповедан в народах, принят верою в мире, вознесся во славе.
Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu: Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu anamuchitira umboni, angelo anamuona, analalikidwa pakati pa mitundu yonse, dziko lapansi linamukhulupirira, anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero.

< 1-е Тимофею 3 >