< איוב 8 >

ויען בלדד השוחי ויאמר 1
Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
עד-אן תמלל-אלה ורוח כביר אמרי-פיך 2
“Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti? Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho.
האל יעות משפט ואם-שדי יעות-צדק 3
Kodi Mulungu amapotoza chiweruzo cholungama? Kodi Wamphamvuzonse amalephera kuchita zachilungamo?
אם-בניך חטאו-לו וישלחם ביד-פשעם 4
Pamene ana ako anamuchimwira Mulungu, Iye anawapereka kuti alangidwe chifukwa cha tchimo lawo.
אם-אתה תשחר אל-אל ואל-שדי תתחנן 5
Koma utayangʼana kwa Mulungu, ndi kudandaulira Wamphamvuzonse,
אם-זך וישר אתה כי-עתה יעיר עליך ושלם נות צדקך 6
ngati uli wangwiro ndi wolungama mtima ngakhale tsopano Iye adzachitapo kanthu mʼmalo mwako ndipo adzakubwezeretsa pa malo ako oyenera.
והיה ראשיתך מצער ואחריתך ישגה מאד 7
Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa koma chimaliziro chako chidzakhala chopambana.
כי-שאל-נא לדר רישון וכונן לחקר אבותם 8
“Funsa kwa anthu amvulazakale ndipo upeze zimene makolo awo anaziphunzira
כי-תמול אנחנו ולא נדע כי צל ימינו עלי-ארץ 9
pakuti ife ndife ana adzulodzuloli ndipo sitidziwa chilichonse, ndipo moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi.
הלא-הם יורוך יאמרו לך ומלבם יוצאו מלים 10
Kodi iwo sadzakulangiza ndi kukufotokozera? Kodi sadzakuwuza mawu ochokera pa zimene amazidziwa?
היגאה-גמא בלא בצה ישגה-אחו בלי-מים 11
Kodi bango nʼkumera pa nthaka yopanda chinyontho? Nanga mawango nʼkukula bwino popanda madzi?
עדנו באבו לא יקטף ולפני כל-חציר ייבש 12
Popanda madzi, zimenezi zimafota zikanali zaziwisi ndi zosadula; zimawuma msangamsanga kuposa bango.
כן--ארחות כל-שכחי אל ותקות חנף תאבד 13
Ndimo mmene amachitira anthu onse amene amayiwala Mulungu; ndi mmene chiyembekezo cha munthu wosapembedza Mulungu chimathera.
אשר-יקוט כסלו ובית עכביש מבטחו 14
Kulimba mtima kwake kumafowoka; zimene iye amadalira zili ngati ukonde wa kangawude.
ישען על-ביתו ולא יעמד יחזיק בו ולא יקום 15
Iye amatsamira ukonde wake, koma umaduka; amawugwiritsitsa koma sulimba.
רטב הוא לפני-שמש ועל גנתו ינקתו תצא 16
Munthu woyipayo ali ngati chomera chothiriridwa bwino chimene chili pa dzuwa, nthambi zake zimatambalala pa munda wake;
על-גל שרשיו יסבכו בית אבנים יחזה 17
mizu yake imayanga pa mulu wa miyala ndi kufunafuna malo woti izikike pa miyalapo.
אם-יבלענו ממקמו וכחש בו לא ראיתיך 18
Koma pamene yachotsedwa pamalo pakepo, pamalopo pamakana chomeracho ndi kuti, ‘Ine sindinakuonepo.’
הן-הוא משוש דרכו ומעפר אחר יצמחו 19
Ndithudi chomeracho chimafota, ndipo pa nthakapo pamatuluka zomera zina.
הן-אל לא ימאס-תם ולא-יחזיק ביד-מרעים 20
“Ndithudi, Mulungu sakana munthu amene alibe cholakwa kapena kulimbikitsa anthu ochita zoyipa.
עד-ימלה שחוק פיך ושפתיך תרועה 21
Iye adzadzaza mʼkamwa mwako ndi phwete ndipo milomo yako idzafuwula ndi chimwemwe.
שנאיך ילבשו-בשת ואהל רשעים איננו 22
Adani ako adzachita manyazi, ndipo malo okhalamo anthu oyipa sadzaonekanso.”

< איוב 8 >