< Actes 1 >

1 Nous avons rempli le premier traité, Théophile! de toutes les choses que Jésus a faites et enseignées;
Mʼbuku langa loyamba, ndinakulembera iwe Teofilo zonse zimene Yesu anayamba kuchita ndi kuphunzitsa,
2 Jusqu'au jour qu'il fut élevé [au ciel]; après avoir donné par le Saint-Esprit ses ordres aux Apôtres qu'il avait élus.
mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba, mwamphamvu ya Mzimu Woyera, atawalangiza atumwi amene anawasankha.
3 A qui aussi, après avoir souffert, il se présenta soi-même vivant, avec plusieurs preuves assurées, étant vu par eux durant quarante jours, et leur parlant des choses qui regardent le Royaume de Dieu.
Zitatha zowawa zake Yesu anadzionetsa kwa ophunzira ake, ndi kuonetsanso maumboni ambiri kuti anali wamoyo. Iye anadzionetsera kwa iwo ndi kuwaphunzitsa za ufumu wa Mulungu pa masiku makumi anayi.
4 Et les ayant assemblés, il leur commanda de ne partir point de Jérusalem, mais [d'y] attendre [l'effet de] la promesse du Père, laquelle, [dit-il], vous avez ouïe de moi.
Nthawi ina atasonkhana nawo pamodzi, Yesu analamulira ophunzira ake kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate anga analonjeza yomwe ndinakuwuzani.
5 Car Jean a baptisé d'eau, mais vous serez baptisés du Saint-Esprit, dans peu de jours.
Pakuti Yohane anakubatizani ndi madzi, koma posachedwapa inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”
6 Eux donc étant assemblés l'interrogèrent, disant: Seigneur, sera-ce en ce temps-ci que tu rétabliras le Royaume d'Israël?
Atumwi atasonkhana pamodzi, iwo anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi nthawi ino mubwezeretsa ufumu kwa Israeli?”
7 Mais il leur dit: ce n'est point à vous de connaître les temps ou les moments qui ne dépendent que de mon Père.
Yesu anawawuza kuti, “Sikofunika kuti mudziwe za nthawi kapena masiku amene Atate ayika mwa ulamuliro wawo.
8 Mais vous recevrez la vertu du Saint-Esprit qui viendra sur vous; et vous me serez témoins tant à Jérusalem qu'en toute la Judée, et dans la Samarie, et jusqu'au bout de la terre.
Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
9 Et quand il eut dit ces choses, il fut élevé [au ciel], eux le regardant, et une nuée le soutenant l'emporta de devant leurs yeux.
Atatha kuyankhula zimenezi, Yesu anatengedwa kupita kumwamba ophunzira ake akuona, ndipo anabisika mʼmitambo.
10 Et comme ils avaient les yeux arrêtés vers le ciel, à mesure qu'il s'en allait, voici, deux hommes en vêtements blancs se présentèrent devant eux;
Yesu akukwera kumwamba, ophunzira ake anayangʼanitsitsa ndi chidwi mʼmitambo. Mwadzidzidzi anaona anthu awiri ovala zoyera atayimirira pambali pawo.
11 Qui leur dirent: hommes Galiléens, pourquoi vous arrêtez-vous à regarder au ciel? Ce Jésus qui a été élevé d'avec vous au ciel en descendra de la même manière que vous l'avez contemplé montant au ciel.
Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”
12 Alors ils s'en retournèrent à Jérusalem de la montagne appelée [la montagne] des oliviers, qui est près de Jérusalem le chemin d'un Sabbat.
Pamenepo atumwi anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri la Olivi, mtunda wosakwana kilomita kuchokera mu mzindamo.
13 Et quand ils furent entrés [dans la ville], ils montèrent en une chambre haute; où demeuraient Pierre et Jacques, Jean et André, Philippe et Thomas, Barthélemy et Matthieu, Jacques [fils] d'Alphée, et Simon Zélotes, et Jude frère de Jacques.
Atafika mu mzindamo, analowa mʼchipinda chammwamba kumene amakhala. Amene analipo anali awa: Petro, Yohane, Yakobo ndi Andreya; Filipo ndi Tomasi, Bartumeyu ndi Mateyu; Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Simoni Zelote ndi Yuda mwana wa Yakobo.
14 Tous ceux-ci persévéraient unanimement en prières et en oraisons avec les femmes, et avec Marie mère de Jésus, et avec ses Frères.
Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
15 Et en ces jours-là Pierre se leva au milieu des Disciples, qui étaient là assemblés au nombre d'environ six-vingts personnes, et il leur dit:
Pa nthawi imeneyo Petro anayimirira pakati pa okhulupirira (gulu la anthu pafupifupi 120).
16 Hommes frères! il fallait que fût accompli ce qui a été écrit, [et] que le Saint-Esprit a prédit par la bouche de David touchant Judas, qui a été le guide de ceux qui ont pris Jésus.
Iye anati, “Abale anga, Malemba anayenera kukwaniritsidwa omwe Mzimu Woyera anayankhula kalekale kudzera mwa Davide za Yudasi, amene anatsogolera amene anamugwira Yesu.
17 Car il était de notre corps, et il avait reçu sa part de ce ministère.
Iye anali mmodzi wa gulu lathu ndipo anatumikira pamodzi ndi ife.”
18 Mais s'étant acquis un champ avec le salaire injuste qui lui avait été donné, et s'étant précipité, son corps s'est crevé par le milieu, et toutes ses entrailles ont été répandues.
(Yudasi anagula munda ndi ndalama zimene anazipeza pochita zoyipa zija; kumeneko, iye anagwa chamutu, naphulika pakati ndipo matumbo ake wonse anakhuthuka.
19 Ce qui a été connu de tous les habitants de Jérusalem; tellement que ce champ-là a été appelé en leur propre Langue, Haceldama, c'est-à-dire, le champ du sang.
Aliyense mu Yerusalemu anamva zimenezi, kotero anatcha mundawo mʼchiyankhulo chawo kuti Akeledama, kutanthauza, Munda wa Magazi).
20 Car il est écrit au Livre des Psaumes: que sa demeure soit déserte, et qu'il n'y ait personne qui y habite. Et, qu'un autre prenne son emploi.
Petro anati, “Pakuti kwalembedwa mʼbuku la Masalimo kuti, “Nyumba yake isanduke bwinja, ndipo pasakhale wogonamo. Ndiponso, “Wina atenge ntchito yake yautsogoleri.
21 Il faut donc que d'entre ces hommes qui se sont assemblés avec nous pendant tout le temps que le Seigneur Jésus a vécu entre nous,
Chifukwa chake ndi kofunika kusankha mmodzi wa anthu amene akhala nafe nthawi yonse imene Ambuye Yesu ankayenda nafe,
22 En commençant depuis le Baptême de Jean, jusqu'au jour qu'il a été enlevé d'avec nous, quelqu'un d'entre eux soit témoin avec nous de sa résurrection.
kuyambira pa nthawi ya ubatizo wa Yohane mpaka nthawi imene Yesu anatengedwa pakati pathu. Pakuti mmodzi wa anthu awa ayenera kukhala mboni pamodzi ndi ife zakuuka kwake.”
23 Et ils en présentèrent deux, [savoir] Joseph, appelé Barsabas, qui était surnommé Juste; et Matthias.
Pamenepo anasankha anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba (wodziwikanso kuti Yusto) ndi Matiyasi.
24 Et en priant ils dirent: toi, Seigneur, qui connais les cœurs de tous, montre lequel de ces deux tu as élu;
Kenaka iwo anapemphera nati, “Ambuye mukudziwa mtima wa aliyense. Tionetseni amene mwamusankha mwa awiri awa
25 Afin qu'il prenne [sa] part de ce ministère et de cet Apostolat, que Judas a abandonné, pour s'en aller en son lieu.
kuti atenge ntchito iyi ya utumwi, imene Yudasi anasiya napita kumalo womuyenera.”
26 Puis ils les tirèrent au sort; et le sort tomba sur Matthias, qui d'une commune voix fut mis au rang des onze Apôtres.
Tsono anachita maere, ndipo maerewo anagwera Matiyasi. Tsono iye anawonjezedwa pa gulu la atumwi khumi ndi mmodziwo.

< Actes 1 >