< Isaiah 31 >

1 Woe to those who go down to Egypt for help, and rely on horses, and trust in chariots because they are many, and in horsemen because they are very strong, but they don’t look to the Holy One of Israel, and they don’t seek the LORD!
Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo, amene amadalira akavalo, nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo, koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli, kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.
2 Yet he also is wise, and will bring disaster, and will not call back his words, but will arise against the house of the evildoers, and against the help of those who work iniquity.
Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga, ndipo sasintha chimene wanena. Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa, komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
3 Now the Egyptians are men, and not God; and their horses flesh, and not spirit. When the LORD stretches out his hand, both he who helps shall stumble, and he who is helped shall fall, and they all shall be consumed together.
Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu; akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu. Yehova akangotambasula dzanja lake, amene amapereka chithandizo adzapunthwa, amene amalandira chithandizocho adzagwa; onsewo adzathera limodzi.
4 For the LORD says to me, “As the lion and the young lion growling over his prey, if a multitude of shepherds is called together against him, will not be dismayed at their voice, nor abase himself for their noise, so the LORD of Hosts will come down to fight on Mount Zion and on its heights.
Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi: “Monga mkango kapena msona wamkango umabangula ukagwira nyama yake, ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo, momwemonso palibe chingaletse Yehova Wamphamvuzonse kubwera kudzatchinjiriza phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
5 As birds hovering, so the LORD of Hosts will protect Jerusalem. He will protect and deliver it. He will pass over and preserve it.”
Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake, Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu; ndi kumupulumutsa, iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”
6 Return to him from whom you have deeply revolted, children of Israel.
Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu.
7 For in that day everyone shall cast away his idols of silver and his idols of gold—sin which your own hands have made for you.
Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
8 “The Assyrian will fall by the sword, not of man; and the sword, not of mankind, shall devour him. He will flee from the sword, and his young men will become subject to forced labor.
“Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu. Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga. Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo adzagwira ntchito yathangata.
9 His rock will pass away by reason of terror, and his princes will be afraid of the banner,” says the LORD, whose fire is in Zion, and his furnace in Jerusalem.
Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha, ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.” Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni, ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.

< Isaiah 31 >