< Ezekiel 40 >

1 In the five and twentieth year of our captivity, in the beginning of the year, in the tenth day of the month, in the fourteenth year after that the city was struck, in the same day, the hand of the LORD was on me, and he brought me there.
Kumayambiriro a chaka cha 25, cha ukapolo wathu, tsiku la khumi lamwezi, patapita zaka khumi ndi zinayi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, pa tsiku lomwelo dzanja la Yehova linali pa ine ndipo Iye anapita nane ku Yerusalemu.
2 In the visions of God brought he me into the land of Israel, and set me down on a very high mountain, whereon was as it were the frame of a city on the south.
Mʼmasomphenyawo Yehova ananditenga ndi kupita nane ku dziko la Israeli ndipo anandiyika pa phiri lalitali kwambiri, moti ndinaona ngati mzinda.
3 He brought me there; and, look, there was a man, whose appearance was like the appearance of bronze, with a line of flax in his hand, and a measuring reed; and he stood in the gate.
Atandifikitsa kumeneko ndinaona munthu wonyezimira ngati mkuwa. Iye anali atayima pa chipata ndipo mʼdzanja lake munali chingwe cha nsalu yabafuta ndi ndodo yoyezera.
4 The man said to me, "Son of man, see with your eyes, and hear with your ears, and set your heart on all that I shall show you; for, to the intent that I may show them to you, you are brought here: declare all that you see to the house of Israel."
Munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetse bwinobwino. Uyikepo mtima wako pa zonse zimene ndikukuonetsa pakuti anakubweretsa kuno kuti uwone zimenezi. Tsono ukawawuze Aisraeli zonse zimene uzione.”
5 Look, a wall on the outside of the house all around, and in the man's hand a measuring reed ten feet four inches (based on a standard eighteen inches plus three inches). So he measured the thickness of the building ten feet four inches, and the height ten feet four inches.
Ine ndinaona khoma litazungulira mbali zonse za Nyumba ya Mulungu. Mʼdzanja la munthuyo munali bango lopimira limene kutalika kwake kunali kwa mamita atatu. Atayeza chipupacho anapeza kuti kuchindikira kwake kunali mamita atatu, ndiponso kutalika kwake kunalinso mamita atatu.
6 Then came he to the gate which looks toward the east, and went up its steps: and he measured the threshold of the gate, ten feet four inches broad; and the other threshold, ten feet four inches broad.
Anapita ku chipata chakummawa. Anakwera pa makwerero a nyumbayo, nayeza chiwundo choyamba cha chipatacho; kutalika kwake kunali mamita atatu.
7 Every side-room was ten feet four inches long, and one reed broad; and the space between the side-rooms was eight feet seven inches; and the threshold of the gate by the porch of the gate at the inner end was ten feet four inches.
Kudutsa chiwundo choyambachi, panali zipinda za alonda zisanu ndi chimodzi, zitatu kudzanja lamanja, zitatu kudzanja lamanzere. Chilichonse chinali cha mamita atatu mulitali mwake, chimodzimodzinso mulifupi mwake. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita awiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pa chipata pafupi ndi khonde lapachipata, chinali mamita atatu.
8 He measured also the porch of the gate toward the house, ten feet four inches.
Ndipo iye anayeza khonde la chipata ndipo chinali cha mamita atatu.
9 Then measured he the porch of the gate, thirteen feet nine inches; and its jambs, three feet five inches; and the porch of the gate was toward the inner end.
Anayeza khonde ndipo linali mamita anayi. Mphuthu zake zinali mita imodzi kuchindikira kwake. Khonde lamʼkati lapachipata linali kumapeto kwenikweni pafupi ndi Nyumba ya Mulungu.
10 The side-rooms of the gate eastward were three on this side, and three on that side; they three were of one measure: and the jambs had the same measurement.
Mʼkati mwa chipata chakummawa munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zofanana, ndipo khonde la pakati pa zipindazo linali lofanana.
11 He measured the breadth of the opening of the gate, seventeen feet three inches; and the length of the gate, twenty-two feet five inches;
Kenaka anayeza chipata cholowera; mulifupi mwake munali mamita asanu ndipo mulitali mwake munali mamita asanu ndi limodzi ndi theka.
12 and a barrier in front of the side-rooms, twenty-one inches, and a barrier on the other side, twenty-one inches; and the side-rooms were ten feet four inches square.
Kutsogolo kwa chipinda chilichonse cha alonda kunali khoma lalifupi lotalika theka la mita, ndipo mbali iliyonse ya zipinda za alondazo inali yotalika mamita atatu.
13 He measured the gate from the ceiling of the one side-room to the ceiling of the other, a breadth of fourty-three feet one inch; the openings being opposite each other.
Ndipo anayeza kutalika kwa mulifupi mwa chipata cholowera, kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china; kuchokera ku chitseko mpaka ku chitseko china. Kutalika kwake kunali mamita khumi ndi awiri ndi theka.
14 He also measured the porch, one hundred three feet four inches; and to the jamb of the courtyard was the gateway all around.
Anayezanso khonde lamʼkati ndipo linali la mamita makumi atatu. Ndipo mozungulira khondelo munali bwalo. Muyesowu sukuphatikiza khonde loyangʼanana ndi bwalo.
15 From the forefront of the gate at the entrance to the forefront of the inner porch of the gate were eighty-six feet one inch.
Kuchokera pa chipata cholowera mpaka ku mapeto a khonde la chipata, kutalika kwake kunali mamita 27.
16 There were closed windows to the side-rooms, and toward their jambs within the gate all around, and likewise to the porches; and windows were around the inside; and on each jamb were palm trees.
Makoma a zipinda ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lamʼkati linalinso ndi mazenera mʼkati mwake. Pa makoma onsewo anajambulapo zithunzi za kanjedza.
17 Then he brought me into the outer court; and look, there were rooms and a pavement, made for the court all around: thirty rooms faced the pavement.
Kenaka munthuyo anandilowetsa mʼbwalo lakunja, ndipo ndinaona zipinda zina ndi msewu wa miyala wozungulira bwalo lonse. Zipinda zonse zinali makumi atatu ndipo zinkayangʼana msewuwo.
18 The pavement was by the side of the gates, corresponding to the length of the gates; this was the lower pavement.
Utali wa mulifupi mwa msewuwo unkayenda mamita 27 kufanana ndi utali wa chipata cholowera. Uwu unali msewu wa mʼmunsi.
19 Then he measured the breadth from the forefront of the lower gate to the forefront of the inner court outside, one hundred seventy-two feet three inches, both on the east and on the north.
Tsono, anayeza kutalika kwa bwalo kuyambira chipata cholowera choyamba mpaka polowera pa chipata chakunja cha bwalo la mʼkati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
20 And the gate of the outer court which faced toward the north, he measured its length and its breadth.
Kenaka munthuyo anayeza mulitali ndi mulifupi mwa chipata chimene chimayangʼana kumpoto, chotulukira kunja.
21 And its side-rooms were three on either side, and its jambs and its porches had the same measurement as the first gate; its length was eighty-six feet one inch, and the breadth fourty-three feet one inch.
Zipinda za alonda zimene zinalipo zitatu mbali iliyonse, makoma ake ndi khonde zinali ndi muyeso wofanana ndi wachipata choyamba chija. Kutalika kwake kunali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
22 And its windows, and its porches, and the palm trees of it had the same measurement as the gate that faced toward the east. And they went up to it by seven steps; and its porch was in front of them.
Mipata yake, khonde lake ndi zojambula za kanjedza zinali ndi miyeso yofanana ndi za chipata chakummawa. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndipo kotsirizira kwa chipatacho kunali khonde.
23 And there was a gate to the inner court across the gate to the north and the east; and he measured from gate to gate one hundred seventy-two feet three inches.
Panalinso chipata cholowera ku bwalo lamʼkati chofanana ndi chakummawa chimene chimayangʼanana ndi chipata chakumpoto, chofanana ndi cha mbali ya kummawa. Anachiyeza kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
24 He led me toward the south; and look, a gate toward the south. And he measured its jambs and its porches; they were the same size as the others.
Ndipo munthuyo anapita nane ku mbali yakummwera ndipo ndinaona chipata chakummwera. Iye anayeza mphuthu zake ndi khonde ndipo zinali ndi miyeso yofanana ndi ya zina zija.
25 There were windows in it and in its porches all around, like those windows; the length was eighty-six feet one inch, and the breadth fourty-three feet one inch.
Mʼzipinda za chipata cholowera chimenechi ndi mʼkhonde lake munali mipata yofanana ndi ya mʼzipinda zina. Mulitali mwake munali mamita 27, mulifupi mwake munali mamita 13.
26 There were seven steps to go up to it, and its porches were in front of them; and it had palm trees on its jambs, one on either side.
Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndi khonde kotsirizira kwake. Chipindacho chinali ndi zojambula za kanjedza ku mbali zonse za makoma.
27 There was a gate to the inner court toward the south. And he measured from gate to gate toward the south one hundred seventy-two feet three inches.
Bwalo lamʼkati linalinso ndi chipata kummwera. Munthuyo analiyeza kuchokera ku chipata chimenechi mpaka ku chipata chakunja. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
28 Then he brought me to the inner court by the south gate, and it had the same dimensions as the others.
Ndipo munthu uja anandilowetsa mʼbwalo lamʼkati kudzera ku chipata chakummwera. Anayeza chipatachi ndipo chinali chofanana ndi zinzake zija.
29 And its side-rooms, and its jambs, and its porches were of the same size as the others. And there were windows in it and in its porches all around; it was eighty-six feet one inch long, and fourty-three feet one inch broad.
Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake zinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi munali mamita 13.
30 And there were porches all around, fourty-three feet one inch long, and eight feet seven inches broad.
(Khonde lililonse la makonde atatu a zipata zolowera bwalo lamʼkati aja linali la mamita ozungulira mʼbwalo lamʼkati anali mamita 13 mulitali mwake, mamita awiri ndi theka mulifupi mwake).
31 And the porches of it faced the outer court, and palm trees were on its jambs, and its stairway had eight steps.
Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
32 And he brought me to the inner court toward the east, and he measured the gate as being the same size;
Kenaka munthuyo anapita nane ku bwalo la mʼkati mbali ya kummawa, ndipo anayeza chipata cholowera; chinali chofanana ndi zinzake zina zija.
33 and its side-rooms, and its jambs, and its porches were the same size as the others, and there were windows in it and in its porches all around. It was eighty-six feet one inch long, and fourty-three feet one inch broad.
Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake chinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
34 The porches of it faced the outer court; and palm trees were on its jambs, on either side, and its stairway had eight steps.
Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
35 He brought me to the north gate, and he measured it; and it had the same dimensions as the others;
Kenaka anapita nane ku chipata chakumpoto ndipo anachiyeza. Chinali chofanana ndi zina zija.
36 its side-rooms, its jambs, and its porches. And there were windows in it all around; the length was eighty-six feet one inch, and the breadth fourty-three feet one inch.
Zipinda zake za alonda, makoma ake ndiponso khonde lake zinali zofanana ndi zina zija, ndipo chinalinso ndi mipata mbali zonse ziwiri. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
37 And its porch faced the outer court; and palm trees were on its jambs, on either side, and its stairway had eight steps.
Khonde lake limayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu zake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
38 And a chamber with its door was by the porch of the gate; there they washed the burnt offering.
Panali chipinda ndipo khomo lake linali pafupi ndi khonde la chipata cholowera chamʼkati. Mʼchipinda mʼmenemo ankatsukira nyama ya nsembe yopsereza.
39 And in the porch of the gate were two tables on either side, and two tables on that side, on which to slaughter the burnt offering and the sin offering and guilt offering.
Pa khonde la chipatacho panali matebulo awiri, lina kuno lina uko. Ankapherapo nsembe zopsereza, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula.
40 On the one side outside, as one goes up to the entrance of the north gate, were two tables; and on the other side of the porch of the gate were two tables.
Panali matebulo anayi, awiri a iwo anali kunja kwa khoma la khonde pafupi ndi makwerero olowera pa chipata chakumpoto ndi awiri enawo anali mbali inayo ya makwerero.
41 Four tables were on either side of the gate, eight tables on which they slaughtered the sacrifices.
Choncho ku mbali imodzi ya chipata kunali matebulo anayi, ndiponso ku mbali inayo kunali matebulo anayi. Onse pamodzi anali matebulo asanu ndi atatu. Pa matebulopo ankapherapo nyama za nsembe zopsereza.
42 There were four tables of carved stone for the burnt offering, two feet seven inches long, and two feet seven inches broad, and twenty-one inches high; on which they laid the instruments with which they slaughtered the burnt offering and the sacrifice.
Matebulo anayiwa anali a miyala yosema. Lililonse mulitali mwake linali la masentimita 75, mulifupi mwake linali la masentimita 75, ndipo msinkhu wake unali wa masentimita makumi asanu. Pa matebulopo amayikapo zipangizo zophera nsembe zopsereza ndi nsembe zina.
43 The hooks, three inches long, were fastened all around within, and on the tables was the flesh of the offering.
Choncho pa matebulopo ankayikapo nyama za nsembe zopsereza. Mbedza zitatu zazitali ngati chikhatho amazikoleka pa makoma pozungulira ponse.
44 And from the outside of the inner gate were two chambers in the inner court, one which was at the side of the north gate facing toward the south; and one at the side of the south gate facing toward the north.
Munthu uja anapita nane mʼkati mwa bwalo ndipo ndinaona zipinda ziwiri. Chimodzi chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyangʼana kummwera ndi china chinali pafupi ndi chipata chakummwera kuyangʼana kumpoto.
45 He said to me, "This room that faces toward the south, is for the priests, the keepers of the duty of the house;
Munthuyo anandiwuza kuti, “Chipinda chimene chikuyangʼana kummwera ndi cha ansembe amene amayangʼanira Nyumba ya Mulungu,
46 and the room that faces toward the north is for the priests, the keepers of the duty of the altar: these are the sons of Zadok, who from among the sons of Levi come near to the LORD to minister to him."
ndipo chipinda chimene chikuyangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amayangʼanira guwa lansembe. Amenewa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene ayenera kutumikira pamaso pa Yehova mʼNyumba ya Mulungu.”
47 He measured the court, one hundred seventy-two feet three inches long, and one hundred seventy-two feet three inches broad, a square; and the altar was in front of the house.
Kenaka munthuyo anayeza bwalo; linali lofanana mbali zonse kutalika kwake, mulitali mwake munali mamita 53, ndipo mulifupi mwake munali mamita 53. Ndipo guwa lansembe linali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
48 Then he brought me to the porch of the house, and measured the jambs of the porch, eight feet seven inches on each side. And the breadth of the gate was twenty-four feet one inch, and the sides of the gate were five feet two inches on each side.
Munthuyo anapita nane pa khonde la Nyumba ya Mulunguyo. Anayeza mphuthu za khondelo ndipo zinali mamita awiri ndi theka mbali zonse. Mulifupi mwa chipatacho munali mamita asanu ndi awiri ndipo mulifupi mwa makoma ake munali mamita awiri mbali zonse.
49 The length of the porch was thirty-four feet five inches, and the breadth twenty feet eight inches. And they went up to it by ten steps; and there were pillars by the jambs on either side.
Mulitali mwa khonde munali mamita khumi, mulifupi mwake munali mamita asanu ndi limodzi kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. Panali makwerero khumi, ndipo mbali zonse kunali nsanamira.

< Ezekiel 40 >