< Galatians 1 >

1 Paul, an apostle—not from men, nor through man, but through Jesus Christ, and God the Father, who raised him from the dead—
Paulo mtumwi, osati wosankhidwa ndi anthu kapena kutumidwa ndi munthu ayi, koma Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate amene anamuukitsa Yesuyo kwa akufa,
2 and all the brothers who are with me, to the assemblies of Galatia:
pamodzi ndi abale onse amene ali nane, Kulembera mipingo ya ku Galatiya:
3 Grace to you and peace from God the Father and our Lord Jesus Christ,
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.
4 who gave himself for our sins, that he might deliver us out of this present evil age (aiōn g165), according to the will of our God and Father—
Yesuyo anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu kuti atipulumutse ku njira za moyo woyipa uno, molingana ndi chifuniro cha Mulungu ndi Atate athu. (aiōn g165)
5 to whom be the glory for the ages (aiōn g165) of the ages (aiōn g165). Amen.
Ulemerero ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ameni. (aiōn g165)
6 I marvel that you are so quickly deserting him who called you in the grace of Christ to a different “good news”,
Ine ndikudabwa kuti mukusiya mwamsangamsanga chotere Mulungu amene anakuyitanani mwachisomo cha Khristu ndipo mwatembenuka ndi kutsatira uthenga wina wosiyana,
7 but there is not another “good news.” Only there are some who trouble you and want to pervert the Good News of Christ.
umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu.
8 But even though we, or an angel from heaven, should preach to you any “good news” other than that which we preached to you, let him be cursed.
Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa!
9 As we have said before, so I now say again: if any man preaches to you any “good news” other than that which you received, let him be cursed.
Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.”
10 For am I now seeking the favor of men, or of God? Or am I striving to please men? For if I were still pleasing men, I would not be a servant of Christ.
Kodi tsopano ndikufuna kukopa anthu kuti andivomereze, kapena Mulungu? Kapena ndikufuna kukondweretsa anthu? Ngati ine ndikanakhala kuti ndikufunabe kukondweretsa anthu, sindikanakhala mtumiki wa Khristu.
11 But I make known to you, brothers, concerning the Good News which was preached by me, that it is not according to man.
Abale, ine ndikufuna kuti mudziwe, kuti Uthenga Wabwino umene ndinalalikira si ochokera kwa munthu ayi.
12 For I did not receive it from man, nor was I taught it, but it came to me through revelation of Jesus Christ.
Ine sindinawulandire kuchokera kwa munthu aliyense, kapena kuphunzitsidwa; koma ndinawulandira mwa vumbulutso lochokera kwa Khristu.
13 For you have heard of my way of living in time past in the Jews’ religion, how that beyond measure I persecuted the assembly of God and ravaged it.
Pakuti inu munamva za moyo wanga wakale mʼChiyuda, mmene ndinkazunzira mpingo wa Mulungu koopsa ndi kuyesetsa kuwuwononga.
14 I advanced in the Jews’ religion beyond many of my own age among my countrymen, being more exceedingly zealous for the traditions of my fathers.
Ine ndinkapambana Ayuda ambiri a msinkhu wanga pochita za Chiyuda, ndipo ndinali wachangu koposa pa miyambo ya makolo athu.
15 But when it was the good pleasure of God, who separated me from my mother’s womb and called me through his grace,
Koma Mulungu, amene anandipatula ine ndisanabadwe, ndi kundiyitana mwachisomo chake, atakondweretsedwa
16 to reveal his Son in me, that I might preach him among the Gentiles, I did not immediately confer with flesh and blood,
kuvumbulutsa Mwana wake mwa ine, kuti ndikalalikire Khristuyo pakati pa anthu a mitundu ina, ine sindinapemphe nzeru kwa munthu aliyense.
17 nor did I go up to Jerusalem to those who were apostles before me, but I went away into Arabia. Then I returned to Damascus.
Ine sindinapite ku Yerusalemu kukaonana ndi amene anali atumwi ine ndisanakhale mtumwi. Mʼmalo mwake nthawi yomweyo ndinapita ku Arabiya ndi kubwereranso ku Damasiko.
18 Then after three years I went up to Jerusalem to visit Peter, and stayed with him fifteen days.
Pambuyo pake, patatha zaka zitatu, ndinapita ku Yerusalemu kukaonana ndi Petro ndikukhala naye masiku khumi ndi asanu.
19 But of the other apostles I saw no one except James, the Lord’s brother.
Ine sindinaonane ndi atumwi enawo koma Yakobo yekha, mʼbale wa Ambuye.
20 Now about the things which I write to you, behold, before God, I am not lying.
Ine ndikutsimikizira inu pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulemberani si zonama ayi.
21 Then I came to the regions of Syria and Cilicia.
Pambuyo pake ndinapita ku Siriya ndi ku Kilikiya.
22 I was still unknown by face to the assemblies of Judea which were in Christ,
Koma sindimadziwika ndi nkhope ku mipingo ya ku Yudeya imene ili mwa Khristu.
23 but they only heard, “He who once persecuted us now preaches the faith that he once tried to destroy.”
Iwo anangomva mbiri yokha yakuti, “Munthu amene poyamba anatizunza ife, tsopano akulalikira chikhulupiriro chimene iyeyo nthawi ina anafuna kuchiwononga.”
24 So they glorified God in me.
Ndipo iwo anayamika Mulungu chifukwa cha ine.

< Galatians 1 >