< Masalimo 129 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli;
Mnogo mi dosaðivaše od mladosti moje, neka reèe Izrailj,
2 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane.
Mnogo mi dosaðivaše od mladosti moje, ali me ne svladaše.
3 Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali:
Na leðima mojim oraše oraèi, i vodiše duge brazde svoje.
4 Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”
Gospod je pravedan; isijeèe konopce bezbožnièke.
5 Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi.
Postidjeæe se, odbiæe se svi koji nenavide Sion.
6 Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule;
Biæe kao trava na krovovima, koja se sasušuje prije nego se poèupa,
7 sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo.
Od koje neæe žetelac napuniti ruke svoje, niti naruèja svojega vezilac;
8 Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”
I koji prolaze neæe reæi: “Blagoslov Gospodnji na vama! blagosiljamo vas imenom Gospodnjim.”

< Masalimo 129 >