< Masalimo 112 >

1 Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.
הַ֥לְלוּ יָ֨הּ ׀ אַשְׁרֵי־אִ֭ישׁ יָרֵ֣א אֶת־יְהוָ֑ה בְּ֝מִצְוֹתָ֗יו חָפֵ֥ץ מְאֹֽד׃
2 Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.
גִּבֹּ֣ור בָּ֭אָרֶץ יִהְיֶ֣ה זַרְעֹ֑ו דֹּ֭ור יְשָׁרִ֣ים יְבֹרָֽךְ׃
3 Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
הֹון־וָעֹ֥שֶׁר בְּבֵיתֹ֑ו וְ֝צִדְקָתֹ֗ו עֹמֶ֥דֶת לָעַֽד׃
4 Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima; wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.
זָ֘רַ֤ח בַּחֹ֣שֶׁךְ אֹ֖ור לַיְשָׁרִ֑ים חַנּ֖וּן וְרַח֣וּם וְצַדִּֽיק׃
5 Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo.
טֹֽוב־אִ֭ישׁ חֹונֵ֣ן וּמַלְוֶ֑ה יְכַלְכֵּ֖ל דְּבָרָ֣יו בְּמִשְׁפָּֽט׃
6 Ndithu sadzagwedezeka; munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.
כִּֽי־לְעֹולָ֥ם לֹא־יִמֹּ֑וט לְזֵ֥כֶר עֹ֝ולָ֗ם יִהְיֶ֥ה צַדִּֽיק׃
7 Saopa akamva zoyipa zimene zachitika; mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.
מִשְּׁמוּעָ֣ה רָ֭עָה לֹ֣א יִירָ֑א נָכֹ֥ון לִ֝בֹּ֗ו בָּטֻ֥חַ בַּיהוָֽה׃
8 Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha; potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.
סָמ֣וּךְ לִ֭בֹּו לֹ֣א יִירָ֑א עַ֖ד אֲשֶׁר־יִרְאֶ֣ה בְצָרָֽיו׃
9 Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.
פִּזַּ֤ר ׀ נָ֘תַ֤ן לָאֶבְיֹונִ֗ים צִ֭דְקָתֹו עֹמֶ֣דֶת לָעַ֑ד קַ֝רְנֹ֗ו תָּר֥וּם בְּכָבֹֽוד׃
10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.
רָ֘שָׁ֤ע יִרְאֶ֨ה ׀ וְכָעָ֗ס שִׁנָּ֣יו יַחֲרֹ֣ק וְנָמָ֑ס תַּאֲוַ֖ת רְשָׁעִ֣ים תֹּאבֵֽד׃

< Masalimo 112 >