< Masalimo 111 >

1 Tamandani Yehova. Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.
הַ֥לְלוּ יָ֨הּ ׀ אֹודֶ֣ה יְ֭הוָה בְּכָל־לֵבָ֑ב בְּסֹ֖וד יְשָׁרִ֣ים וְעֵדָֽה׃
2 Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira.
גְּ֭דֹלִים מַעֲשֵׂ֣י יְהוָ֑ה דְּ֝רוּשִׁ֗ים לְכָל־חֶפְצֵיהֶֽם׃
3 Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
הֹוד־וְהָדָ֥ר פָּֽעֳלֹ֑ו וְ֝צִדְקָתֹ֗ו עֹמֶ֥דֶת לָעַֽד׃
4 Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike; Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.
זֵ֣כֶר עָ֭שָׂה לְנִפְלְאֹתָ֑יו חַנּ֖וּן וְרַח֣וּם יְהוָֽה׃
5 Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye; amakumbukira pangano lake kwamuyaya.
טֶ֭רֶף נָתַ֣ן לִֽירֵאָ֑יו יִזְכֹּ֖ר לְעֹולָ֣ם בְּרִיתֹֽו׃
6 Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake, kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.
כֹּ֣חַ מַ֭עֲשָׂיו הִגִּ֣יד לְעַמֹּ֑ו לָתֵ֥ת לָ֝הֶ֗ם נַחֲלַ֥ת גֹּויִֽם׃
7 Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama; malangizo ake onse ndi odalirika.
מַעֲשֵׂ֣י יָ֭דָיו אֱמֶ֣ת וּמִשְׁפָּ֑ט נֶ֝אֱמָנִ֗ים כָּל־פִּקּוּדָֽיו׃
8 Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi, ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.
סְמוּכִ֣ים לָעַ֣ד לְעֹולָ֑ם עֲ֝שׂוּיִ֗ם בֶּאֱמֶ֥ת וְיָשָֽׁר׃
9 Iyeyo amawombola anthu ake; anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya dzina lake ndi loyera ndi loopsa.
פְּד֤וּת ׀ שָׁ֘לַ֤ח לְעַמֹּ֗ו צִוָּֽה־לְעֹולָ֥ם בְּרִיתֹ֑ו קָדֹ֖ושׁ וְנֹורָ֣א שְׁמֹֽו׃
10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.
רֵ֘אשִׁ֤ית חָכְמָ֨ה ׀ יִרְאַ֬ת יְהוָ֗ה שֵׂ֣כֶל טֹ֖וב לְכָל־עֹשֵׂיהֶ֑ם תְּ֝הִלָּתֹ֗ו עֹמֶ֥דֶת לָעַֽד׃

< Masalimo 111 >