< Masalimo 149 >

1 Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima. 2 Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo. 3 Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe. 4 Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa. 5 Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo. 6 Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo, 7 kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse, 8 kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo, 9 kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova.

< Masalimo 149 >