< Masalimo 148 >

1 Tamandani Yehova. Tamandani Yehova, inu a kumwamba, mutamandeni Iye, inu a mlengalenga. 2 Mutamandeni, inu angelo ake onse, mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba. 3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi, mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala. 4 Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba ndi inu madzi a pamwamba pa thambo. 5 Zonse zitamande dzina la Yehova pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa. 6 Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi; analamula ndipo sizidzatha. 7 Tamandani Yehova pa dziko lapansi, inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya, 8 inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo, mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake, 9 inu mapiri ndi zitunda zonse, inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse, 10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse, inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka. 11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi. 12 Inu anyamata ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe. 13 Onsewo atamande dzina la Yehova pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka; ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe. 14 Iye wakwezera nyanga anthu ake, matamando a anthu ake onse oyera mtima, Aisraeli, anthu a pamtima pake. Tamandani Yehova.

< Masalimo 148 >