< Masalimo 131 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Davide. Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza, maso anga siwonyada; sinditengeteka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa. 2 Koma moyo wanga ndawutontholetsa ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa, moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa. 3 Yembekeza Yehova, iwe Israeli, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

< Masalimo 131 >