< Masalimo 130 >

1 Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama; 2 Ambuye imvani mawu anga. Makutu anu akhale tcheru kumva kupempha chifundo kwanga. 3 Inu Yehova, mukanamawerengera machimo, Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu? 4 Koma kwa Inu kuli chikhululukiro; nʼchifukwa chake mumaopedwa. 5 Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera, ndipo ndimakhulupirira mawu ake. 6 Moyo wanga umayembekezera Ambuye, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa, inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa, 7 Yembekeza Yehova, iwe Israeli, pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka. 8 Iye mwini adzawombola Israeli ku machimo ake onse.

< Masalimo 130 >