< Masalimo 119 >

1 Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa, amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.
行为完全、遵行耶和华律法的, 这人便为有福!
2 Odala ndi amene amasunga malamulo ake, amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.
遵守他的法度、一心寻求他的, 这人便为有福!
3 Sachita cholakwa chilichonse; amayenda mʼnjira zake.
这人不做非义的事, 但遵行他的道。
4 Inu mwapereka malangizo ndipo ayenera kutsatidwa kwathunthu.
耶和华啊,你曾将你的训词吩咐我们, 为要我们殷勤遵守。
5 Aa! Ndikanakonda njira zanga zikanakhala zokhazikika pa kumvera zophunzitsa zanu!
但愿我行事坚定, 得以遵守你的律例。
6 Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi, poganizira malamulo anu onse.
我看重你的一切命令, 就不至于羞愧。
7 Ndidzakutamandani ndi mtima wolungama, pamene ndikuphunzira malamulo anu olungama.
我学了你公义的判语, 就要以正直的心称谢你。
8 Ndidzamvera zophunzitsa zanu; musanditaye kwathunthu.
我必守你的律例; 求你总不要丢弃我!
9 Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake? Akawasamala potsata mawu anu.
少年人用什么洁净他的行为呢? 是要遵行你的话!
10 Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse; musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.
我一心寻求了你; 求你不要叫我偏离你的命令。
11 Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.
我将你的话藏在心里, 免得我得罪你。
12 Mutamandike Inu Yehova; phunzitseni malamulo anu.
耶和华啊,你是应当称颂的! 求你将你的律例教训我!
13 Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse amene amachokera pakamwa panu.
我用嘴唇传扬你口中的一切典章。
14 Ndimakondwera potsatira malamulo anu monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.
我喜悦你的法度, 如同喜悦一切的财物。
15 Ndimalingalira malangizo anu ndipo ndimaganizira njira zanu.
我要默想你的训词, 看重你的道路。
16 Ndimakondwera ndi malamulo anu; sindidzayiwala konse mawu anu.
我要在你的律例中自乐; 我不忘记你的话。
17 Chitirani zokoma mtumiki wanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo; kuti tsono ndisunge mawu anu.
求你用厚恩待你的仆人,使我存活, 我就遵守你的话。
18 Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.
求你开我的眼睛, 使我看出你律法中的奇妙。
19 Ine ndine mlendo pa dziko lapansi; musandibisire malamulo anu.
我是在地上作寄居的; 求你不要向我隐瞒你的命令!
20 Moyo wanga wafowoka polakalaka malamulo anu nthawi zonse.
我时常切慕你的典章, 甚至心碎。
21 Inu mumadzudzula onyada, otembereredwa, amene achoka pa malamulo anu.
受咒诅、偏离你命令的骄傲人, 你已经责备他们。
22 Mundichotsere chitonzo ndi mnyozo pakuti ndimasunga malamulo anu.
求你除掉我所受的羞辱和藐视, 因我遵守你的法度。
23 Ngakhale mafumu akhale pamodzi kundinyoza, mtumiki wanu adzalingalirabe zophunzitsa zanu.
虽有首领坐着妄论我, 你仆人却思想你的律例。
24 Malamulo anu amandikondweretsa; ndiwo amene amandilangiza.
你的法度是我所喜乐的, 是我的谋士。
25 Moyo wanga wakangamira fumbi; tsitsimutseni molingana ndi mawu anu.
我的性命几乎归于尘土; 求你照你的话将我救活!
26 Ndinafotokoza njira zanga ndipo Inu munandiyankha; phunzitseni malamulo anu.
我述说我所行的,你应允了我; 求你将你的律例教训我!
27 Mundidziwitse chiphunzitso cha malangizo anu; pamenepo ndidzalingalira zodabwitsa zanu.
求你使我明白你的训词, 我就思想你的奇事。
28 Moyo wanga wafowoka ndi chisoni; limbikitseni monga mwa mawu anu.
我的心因愁苦而消化; 求你照你的话使我坚立!
29 Mundichotse mʼnjira zachinyengo; mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.
求你使我离开奸诈的道, 开恩将你的律法赐给我!
30 Ndasankha njira ya choonadi; ndayika malamulo anu pa mtima panga.
我拣选了忠信的道, 将你的典章摆在我面前。
31 Ndagwiritsitsa umboni wanu, Inu Yehova; musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
我持守你的法度; 耶和华啊,求你不要叫我羞愧!
32 Ndimathamanga mʼnjira ya malamulo anu, pakuti Inu mwamasula mtima wanga.
你开广我心的时候, 我就往你命令的道上直奔。
33 Yehova, phunzitseni kutsatira zophunzitsa zanu; ndipo ndidzazisunga mpaka kumapeto.
耶和华啊,求你将你的律例指教我, 我必遵守到底!
34 Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.
求你赐我悟性,我便遵守你的律法, 且要一心遵守。
35 Munditsogolere mʼnjira ya malamulo anu, pakuti mʼmenemo ndimapezamo chikondwerero changa.
求你叫我遵行你的命令, 因为这是我所喜乐的。
36 Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma.
求你使我的心趋向你的法度, 不趋向非义之财。
37 Tembenuzani maso anga kuchoka ku zinthu zachabechabe; sungani moyo wanga monga mwa mawu anu.
求你叫我转眼不看虚假, 又叫我在你的道中生活。
38 Kwaniritsani lonjezo lanu kwa mtumiki wanu, kuti Inu muopedwe.
你向敬畏你的人所应许的话, 求你向仆人坚定!
39 Mundichotsere chipongwe chimene ndikuchiopa, pakuti malamulo anu ndi abwino.
求你使我所怕的羞辱远离我, 因你的典章本为美。
40 Taonani, ndimalakalakatu malangizo anu! Sungani moyo wanga mʼchilungamo chanu.
我羡慕你的训词; 求你使我在你的公义上生活!
41 Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova, chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;
耶和华啊,愿你照你的话,使你的慈爱, 就是你的救恩,临到我身上,
42 ndipo ndidzayankha amene amandinyoza, popeza ndimadalira mawu anu.
我就有话回答那羞辱我的, 因我倚靠你的话。
43 Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga, pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.
求你叫真理的话总不离开我口, 因我仰望你的典章。
44 Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse, ku nthawi za nthawi.
我要常守你的律法, 直到永永远远。
45 Ndidzayendayenda mwaufulu, chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.
我要自由而行, 因我素来考究你的训词。
46 Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu ndipo sindidzachititsidwa manyazi,
我也要在君王面前论说你的法度, 并不至于羞愧。
47 popeza ndimakondwera ndi malamulo anu chifukwa ndimawakonda.
我要在你的命令中自乐; 这命令素来是我所爱的。
48 Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda, ndipo ndimalingalira malangizo anu.
我又要遵行你的命令, 这命令素来是我所爱的; 我也要思想你的律例。
49 Kumbukirani mawu anu kwa mtumiki wanu, popeza mwandipatsa chiyembekezo.
求你记念向你仆人所应许的话, 叫我有盼望。
50 Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi: lonjezo lanu limasunga moyo wanga.
这话将我救活了; 我在患难中,因此得安慰。
51 Odzikuza amandinyoza popanda chowaletsa, koma sindichoka pa malamulo anu.
骄傲的人甚侮慢我, 我却未曾偏离你的律法。
52 Ndimakumbukira malamulo anu Yehova akalekale, ndipo mwa iwo ndimapeza chitonthozo.
耶和华啊,我记念你从古以来的典章, 就得了安慰。
53 Ndayipidwa kwambiri chifukwa cha oyipa amene ataya malamulo anu.
我见恶人离弃你的律法, 就怒气发作,犹如火烧。
54 Zophunzitsa zanu ndi mitu ya nyimbo yanga kulikonse kumene ndigonako.
我在世寄居, 素来以你的律例为诗歌。
55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu Yehova, ndipo ndidzasunga malamulo anu.
耶和华啊,我夜间记念你的名, 遵守你的律法。
56 Ichi ndicho ndakhala ndikuchita: ndimasunga malangizo anu.
我所以如此, 是因我守你的训词。
57 Yehova, Inu ndiye gawo langa; ndalonjeza kumvera mawu anu.
耶和华是我的福分; 我曾说,我要遵守你的言语。
58 Ndimafunafuna nkhope yanu ndi mtima wanga wonse; mundikomere mtima monga mwa lonjezo lanu.
我一心求过你的恩; 愿你照你的话怜悯我!
59 Ndinalingalira za njira zanga ndipo ndatembenuza mayendedwe anga kutsatira umboni wanu.
我思想我所行的道, 就转步归向你的法度。
60 Ndidzafulumira ndipo sindidzazengereza kumvera malamulo anu.
我急忙遵守你的命令, 并不迟延。
61 Ngakhale oyipa andimange ndi zingwe, sindidzayiwala lamulo lanu.
恶人的绳索缠绕我, 我却没有忘记你的律法。
62 Ndimadzuka pakati pa usiku kuyamika Inu chifukwa cha malamulo anu olungama.
我因你公义的典章, 半夜必起来称谢你。
63 Ine ndine bwenzi la onse amene amakukondani, kwa onse amene amatsatira malangizo anu.
凡敬畏你、守你训词的人, 我都与他作伴。
64 Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chanu chosasinthika, phunzitseni malamulo anu.
耶和华啊,你的慈爱遍满大地; 求你将你的律例教训我!
65 Inu Yehova, chitirani chabwino mtumiki wanu molingana ndi mawu anu.
耶和华啊,你向来是照你的话善待仆人。
66 Phunzitseni nzeru ndi chiweruzo chabwino, pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.
求你将精明和知识赐给我, 因我信了你的命令。
67 Ndisanayambe kuzunzika ndinasochera, koma tsopano ndimamvera mawu anu.
我未受苦以先走迷了路, 现在却遵守你的话。
68 Inu ndinu abwino ndipo zimene mumachita ndi zabwino; phunzitseni malamulo anu.
你本为善,所行的也善; 求你将你的律例教训我!
69 Ngakhale odzikuza andipaka mabodza, ine ndimasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
骄傲人编造谎言攻击我, 我却要一心守你的训词。
70 Mitima yawo ndi yowuma ndi yosakhudzidwa, koma ine ndimakondwera ndi malamulo anu.
他们心蒙脂油, 我却喜爱你的律法。
71 Ndi bwino kuti ndinasautsidwa kuti ndithe kuphunzira malamulo anu.
我受苦是与我有益, 为要使我学习你的律例。
72 Lamulo lochokera mʼkamwa mwanu limandikomera kwambiri kuposa ndalama zambirimbiri za siliva ndi golide.
你口中的训言与我有益, 胜于千万的金银。
73 Manja anu anandilenga ndi kundiwumba; patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ndiphunzire malamulo anu.
你的手制造我,建立我; 求你赐我悟性,可以学习你的命令!
74 Iwo amene amakuopani akondwere akandiona, chifukwa chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
敬畏你的人见我就要欢喜, 因我仰望你的话。
75 Ine ndikudziwa, Inu Yehova, kuti malamulo anu ndi olungama ndipo mwandizunza chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
耶和华啊,我知道你的判语是公义的; 你使我受苦是以诚实待我。
76 Chikondi chanu chosasinthika chikhale chitonthozo changa, molingana ndi lonjezo lanu kwa mtumiki wanu.
求你照着应许仆人的话, 以慈爱安慰我。
77 Chifundo chanu chindifikire kuti ndikhale ndi moyo, popeza malamulo anu ndiye chikondwerero changa.
愿你的慈悲临到我,使我存活, 因你的律法是我所喜爱的。
78 Odzikuza achititsidwe manyazi chifukwa cha kundilakwira popanda chifukwa; koma ine ndidzalingalira malangizo anu.
愿骄傲人蒙羞,因为他们无理地倾覆我; 但我要思想你的训词。
79 Iwo amene amakuopani atembenukire kwa ine, iwo amene amamvetsetsa umboni wanu.
愿敬畏你的人归向我, 他们就知道你的法度。
80 Mtima wanga ukhale wopanda cholakwa pa chiphunzitso chanu kuti ndisachititsidwe manyazi.
愿我的心在你的律例上完全, 使我不致蒙羞。
81 Moyo wanga wafowoka ndi kufunafuna chipulumutso chanu, koma chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
我心渴想你的救恩, 仰望你的应许。
82 Maso anga alefuka pofunafuna lonjezo lanu; Ine ndikuti, “Kodi mudzanditonthoza liti?”
我因盼望你的应许眼睛失明,说: 你何时安慰我?
83 Ngakhale ndili ngati thumba lachikopa la vinyo pa utsi sindiyiwala zophunzitsa zanu.
我好像烟薰的皮袋, 却不忘记你的律例。
84 Kodi mtumiki wanu ayenera kudikira mpaka liti? Kodi mudzawalanga liti amene amandizunza?
你仆人的年日有多少呢? 你几时向逼迫我的人施行审判呢?
85 Anthu osalabadira za Mulungu, odzikuza amandikumbira dzenje motsutsana ndi malamulo anu.
不从你律法的骄傲人为我掘了坑。
86 Malamulo anu onse ndi odalirika; thandizeni, pakuti anthu akundizunza popanda chifukwa.
你的命令尽都诚实; 他们无理地逼迫我,求你帮助我!
87 Iwo anatsala pangʼono kundichotsa pa dziko lapansi koma sindinataye malangizo anu.
他们几乎把我从世上灭绝, 但我没有离弃你的训词。
88 Sungani moyo wanga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika, ndipo ndidzamvera umboni wa pakamwa panu.
求你照你的慈爱将我救活, 我就遵守你口中的法度。
89 Mawu anu Yehova ndi amuyaya; akhazikika kumwambako.
耶和华啊,你的话安定在天, 直到永远。
90 Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka ku mibado yonse; Inu munakhazikitsa dziko lapansi ndipo lilipobe.
你的诚实存到万代; 你坚定了地,地就长存。
91 Malamulo anu alipobe mpaka lero lino, pakuti zinthu zonse zimatumikira Inu.
天地照你的安排存到今日; 万物都是你的仆役。
92 Malamulo anu akanapanda kukhala chikondwerero changa, ndikanawonongeka mʼmasautso anga.
我若不是喜爱你的律法, 早就在苦难中灭绝了!
93 Ine sindidzayiwala konse malangizo anu, pakuti ndi malangizo anuwo munasunga moyo wanga.
我永不忘记你的训词, 因你用这训词将我救活了。
94 Ndine wanu, ndipulumutseni; pakuti ndasamala malangizo anu.
我是属你的,求你救我, 因我寻求了你的训词。
95 Anthu oyipa akudikira kuti andiwononge, koma ndidzalingalira umboni wanu.
恶人等待我,要灭绝我, 我却要揣摩你的法度。
96 Ndadziwa kuti zinthu zonse zili ndi malire, koma malamulo anu alibe malire konse.
我看万事尽都有限, 惟有你的命令极其宽广。
97 Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu! Ndimalingaliramo tsiku lonse.
我何等爱慕你的律法, 终日不住地思想。
98 Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga, popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.
你的命令常存在我心里, 使我比仇敌有智慧。
99 Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse popeza ndimalingalira umboni wanu.
我比我的师傅更通达, 因我思想你的法度。
100 Ndili ndi nzeru zochuluka zomvetsera zinthu kuposa anthu okalamba, popeza ndimamvera malangizo anu.
我比年老的更明白, 因我守了你的训词。
101 Ndimaletsa miyendo yanga kuyenda mʼnjira iliyonse yoyipa kuti ndithe kumvera mawu anu.
我禁止我脚走一切的邪路, 为要遵守你的话。
102 Sindinapatuke kuchoka pa malamulo anu, pakuti Inu mwini munandiphunzitsa.
我没有偏离你的典章, 因为你教训了我。
103 Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa, otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!
你的言语在我上膛何等甘美, 在我口中比蜜更甜!
104 Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu; kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.
我借着你的训词得以明白, 所以我恨一切的假道。
105 Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga ndi kuwunika kwa pa njira yanga.
你的话是我脚前的灯, 是我路上的光。
106 Ndalumbira ndipo ndatsimikiza, kuti ndidzatsatira malamulo anu olungama.
你公义的典章,我曾起誓遵守, 我必按誓而行。
107 Ndazunzika kwambiri; Inu Yehova, sungani moyo wanga molingana ndi mawu anu.
我甚是受苦; 耶和华啊,求你照你的话将我救活!
108 Inu Yehova, landirani matamando aufulu ochokera pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.
耶和华啊,求你悦纳我口中的赞美为供物, 又将你的典章教训我!
109 Ngakhale moyo wanga umakhala mʼzoopsa nthawi ndi nthawi, sindidzayiwala malamulo anu.
我的性命常在危险之中, 我却不忘记你的律法。
110 Anthu oyipa anditchera msampha, koma sindinasochere kuchoka pa malangizo anu.
恶人为我设下网罗, 我却没有偏离你的训词。
111 Umboni wanu ndiye cholowa changa kwamuyaya; Iwo ndiye chimwemwe cha mtima wanga.
我以你的法度为永远的产业, 因这是我心中所喜爱的。
112 Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu mpaka kumapeto kwenikweni.
我的心专向你的律例, 永远遵行,一直到底。
113 Ndimadana ndi anthu apawiripawiri, koma ndimakonda malamulo anu.
心怀二意的人为我所恨; 但你的律法为我所爱。
114 Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa; chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
你是我藏身之处,又是我的盾牌; 我甚仰望你的话语。
115 Chokani kwa ine, inu anthu ochita zoyipa, kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga!
作恶的人哪,你们离开我吧! 我好遵守我 神的命令。
116 Mundichirikize molingana ndi lonjezo lanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo; musalole kuti chiyembekezo changa chipite pachabe.
求你照你的话扶持我,使我存活, 也不叫我因失望而害羞。
117 Gwirizizeni, ndipo ndidzapulumutsidwa; nthawi zonse ndidzasamalira zophunzitsa zanu.
求你扶持我,我便得救, 时常看重你的律例。
118 Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu, pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.
凡偏离你律例的人,你都轻弃他们, 因为他们的诡诈必归虚空。
119 Anthu onse oyipa a pa dziko lapansi mumawayesa ngati zinthu zakudzala; nʼchifukwa chake ndimakonda umboni wanu.
凡地上的恶人,你除掉他,好像除掉渣滓; 因此我爱你的法度。
120 Thupi langa limanjenjemera chifukwa cha kuopa Inu; ndimachita mantha ndi malamulo anu.
我因惧怕你,肉就发抖; 我也怕你的判语。
121 Ndachita zolungama ndi zabwino; musandisiye mʼmanja mwa ondizunza.
我行过公平和公义, 求你不要撇下我给欺压我的人!
122 Onetsetsani kuti mtumiki wanu akukhala bwino, musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.
求你为仆人作保,使我得好处, 不容骄傲人欺压我!
123 Maso anga alefuka, kufunafuna chipulumutso chanu, kufunafuna lonjezo lanu lolungama.
我因盼望你的救恩 和你公义的话眼睛失明。
124 Muchite naye mtumiki wanu molingana ndi chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
求你照你的慈爱待仆人, 将你的律例教训我。
125 Ine ndine mtumiki wanu; patseni mzimu wondizindikiritsa, kuti ndimvetsetse umboni wanu.
我是你的仆人,求你赐我悟性, 使我得知你的法度。
126 Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu; malamulo anu akuswedwa.
这是耶和华降罚的时候, 因人废了你的律法。
127 Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino,
所以,我爱你的命令胜于金子, 更胜于精金。
128 ndiponso chifukwa choti ndimaona kuti malangizo anu onse ndi wowongoka, ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.
你一切的训词,在万事上我都以为正直; 我却恨恶一切假道。
129 Maumboni anu ndi odabwitsa nʼchifukwa chake ndimawamvera.
你的法度奇妙, 所以我一心谨守。
130 Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika; ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.
你的言语一解开就发出亮光, 使愚人通达。
131 Ndimatsekula pakamwa panga ndi kupuma wefuwefu, kufunafuna malamulo anu.
我张口而气喘, 因我切慕你的命令。
132 Tembenukirani kwa ine ndipo mundichitire chifundo, monga mumachitira nthawi zonse kwa iwo amene amakonda dzina lanu.
求你转向我,怜悯我, 好像你素常待那些爱你名的人。
133 Tsogolerani mayendedwe anga molingana ndi mawu anu; musalole kuti tchimo lizindilamulira.
求你用你的话使我脚步稳当, 不许什么罪孽辖制我。
134 Ndiwomboleni mʼdzanja la anthu ondizunza, kuti ndithe kumvera malangizo anu.
求你救我脱离人的欺压, 我要遵守你的训词。
135 Nkhope yanu iwalire mtumiki wanu ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
求你用脸光照仆人, 又将你的律例教训我。
136 Mitsinje ya misozi ikuyenda kuchoka mʼmaso mwanga, chifukwa anthu sakumvera malamulo anu.
我的眼泪下流成河, 因为他们不守你的律法。
137 Yehova ndinu wolungama, ndipo malamulo anu ndi abwino.
耶和华啊,你是公义的; 你的判语也是正直的!
138 Maumboni amene munatipatsa ndi olungama; ndi odalirika ndithu.
你所命定的法度是凭公义和至诚。
139 Ndikusautsidwa kwambiri mʼkati mwanga chifukwa adani anu amanyalanyaza mawu anu.
我心焦急,如同火烧, 因我敌人忘记你的言语。
140 Mawu anu ndi woyera kwambiri nʼchifukwa chake mtumiki wanune ndimawakonda.
你的话极其精炼, 所以你的仆人喜爱。
141 Ngakhale ndili wamngʼono ndi wonyozeka, sindiyiwala malangizo anu.
我微小,被人藐视, 却不忘记你的训词。
142 Chilungamo chanu nʼchamuyaya, ndipo malamulo anu nʼchoona.
你的公义永远长存; 你的律法尽都真实。
143 Mavuto ndi masautso zandigwera, koma ndimakondwera ndi malamulo anu.
我遭遇患难愁苦, 你的命令却是我所喜爱的。
144 Umboni wanu ndi wabwino nthawi zonse; patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ine ndikhale ndi moyo.
你的法度永远是公义的; 求你赐我悟性,我就活了。
145 Ndimayitana ndi mtima wanga wonse; ndiyankheni Inu Yehova, ndipo ndidzamvera zophunzitsa zanu.
耶和华啊,我一心呼吁你; 求你应允我,我必谨守你的律例!
146 Ndikuyitana kwa Inu; pulumutseni ndipo ndidzasunga umboni wanu.
我向你呼吁,求你救我! 我要遵守你的法度。
147 Ndimadzuka tambala asanalire kuti ndipemphe thandizo; chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
我趁天未亮呼求; 我仰望了你的言语。
148 Maso anga amakhala chipenyere nthawi yonse ya usiku, kuti ndithe kulingalira malonjezo anu.
我趁夜更未换将眼睁开, 为要思想你的话语。
149 Imvani mawu anga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; Yehova sungani moyo wanga, molingana ndi malamulo anu.
求你照你的慈爱听我的声音; 耶和华啊,求你照你的典章将我救活!
150 Iwo amene amakonza njira zoyipa andiyandikira, koma ali kutali ndi malamulo anu.
追求奸恶的人临近了; 他们远离你的律法。
151 Koma Inu Yehova muli pafupi, malamulo anu onse ndi woona.
耶和华啊,你与我相近; 你一切的命令尽都真实!
152 Ndinaphunzira kalekale kuchokera mʼmaumboni anu kuti maumboni amene munakhazikitsawo ndi amuyaya.
我因学你的法度, 久已知道是你永远立定的。
153 Yangʼanani masautso anga ndipo mundipulumutse, pakuti sindinayiwale malamulo anu.
求你看顾我的苦难,搭救我, 因我不忘记你的律法。
154 Mundiyimirire pa mlandu wanga ndi kundiwombola; sungani moyo wanga molingana ndi lonjezo lanu.
求你为我辨屈,救赎我, 照你的话将我救活。
155 Chipulumutso chili kutali ndi anthu oyipa, pakuti iwowo safunafuna zophunzitsa zanu.
救恩远离恶人, 因为他们不寻求你的律例。
156 Chifundo chanu Yehova nʼchachikulu; sungani moyo wanga molingana ndi malamulo anu.
耶和华啊,你的慈悲本为大; 求你照你的典章将我救活。
157 Adani amene akundizunza ndi ambiri, koma ine sindinatembenuke kuchoka pa umboni wanu.
逼迫我的,抵挡我的,很多, 我却没有偏离你的法度。
158 Ndimawayangʼana monyansidwa anthu opanda chikhulupiriro, popeza samvera mawu anu.
我看见奸恶的人就甚憎恶, 因为他们不遵守你的话。
159 Onani momwe ndimakondera malangizo anu; sungani moyo wanga, Inu Yehova, molingana ndi chikondi chanu chosanthika.
你看我怎样爱你的训词! 耶和华啊,求你照你的慈爱将我救活!
160 Mawu anu onse ndi owona; malamulo anu onse olungama ndi amuyaya.
你话的总纲是真实; 你一切公义的典章是永远长存。
161 Olamulira amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umanjenjemera ndi mawu anu.
首领无故地逼迫我, 但我的心畏惧你的言语。
162 Ine ndimakondwa ndi lonjezo lanu, ngati munthu amene wapeza chuma chambiri.
我喜爱你的话, 好像人得了许多掳物。
163 Ndimadana ndi chinyengo, kwambiri ndimanyansidwa nacho, koma ndimakonda malamulo anu.
谎话是我所恨恶所憎嫌的; 惟你的律法是我所爱的。
164 Ndimakutamandani kasanu ndi kawiri pa tsiku pakuti malamulo anu ndi olungama.
我因你公义的典章一天七次赞美你。
165 Amene amakonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, ndipo palibe chimene chingawapunthwitse
爱你律法的人有大平安, 什么都不能使他们绊脚。
166 Ndikudikira chipulumutso chanu, Inu Yehova, ndipo ndimatsatira malamulo anu.
耶和华啊,我仰望了你的救恩, 遵行了你的命令。
167 Ndimamvera umboni wanu pakuti ndimawukonda kwambiri.
我心里守了你的法度; 这法度我甚喜爱。
168 Ndimamvera malangizo anu ndi umboni wanu, pakuti njira zanga zonse ndi zodziwika pamaso panu.
我遵守了你的训词和法度, 因我一切所行的都在你面前。
169 Kulira kwanga kufike pamaso panu Yehova; patseni nzeru zomvetsa zinthu molingana ndi mawu anu.
耶和华啊,愿我的呼吁达到你面前, 照你的话赐我悟性。
170 Kupempha kwanga kufike pamaso panu; pulumutseni molingana ndi lonjezo lanu.
愿我的恳求达到你面前, 照你的话搭救我。
171 Matamando asefukire pa milomo yanga, pakuti Inu mumandiphunzitsa malamulo anu.
愿我的嘴发出赞美的话, 因为你将律例教训我。
172 Lilime langa liyimbe mawu anu, popeza malamulo anu onse ndi olungama.
愿我的舌头歌唱你的话, 因你一切的命令尽都公义。
173 Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza pakuti ndasankha malangizo anu.
愿你用手帮助我, 因我拣选了你的训词。
174 Ndikufunitsitsa chipulumutso chanu Yehova, ndipo ndimakondwera ndi malamulo anu.
耶和华啊,我切慕你的救恩! 你的律法也是我所喜爱的。
175 Loleni kuti ndikhale ndi moyo kuti ndikutamandeni, ndipo malamulo anu andichirikize.
愿我的性命存活,得以赞美你! 愿你的典章帮助我!
176 Ndasochera ngati nkhosa yotayika, funafunani mtumiki wanu, pakuti sindinayiwale malamulo anu.
我如亡羊走迷了路,求你寻找仆人, 因我不忘记你的命令。

< Masalimo 119 >