< Miyambo 16 >

1 Zolinga za mu mtima ndi za munthu, koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.
The plans of the heart belong to man, but the answer of the tongue is from Jehovah.
2 Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake, koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.
All the ways of a man are clean in his own eyes, but Jehovah weighs the spirits.
3 Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.
Commit thy works to Jehovah, and thy purposes shall be established.
4 Yehova amachita zonse ndi cholinga chake, ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.
Jehovah has made everything for its own end, yea, even the wicked for the day of evil.
5 Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova. Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.
Everyone who is proud in heart is an abomination to Jehovah. Hand in hand, he shall not be unpunished.
6 Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake; chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa.
By mercy and truth iniquity is atoned for, and by the fear of Jehovah men depart from evil.
7 Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova, ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere.
When a man's ways please Jehovah, he makes even his enemies to be at peace with him.
8 Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo, kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo.
Better is a little, with righteousness, than great revenues with injustice.
9 Mtima wa munthu umalingalira zochita, koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.
A man's heart devises his way, but Jehovah directs his steps.
10 Mawu a mfumu ali ngati mawu ochokera kwa Mulungu; ndipo pakamwa pake sipalakwa poweruza mlandu.
A divine sentence is in the lips of the king. His mouth shall not transgress in judgment.
11 Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova; miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova.
A just balance and scales are Jehovah's. All the weights of the bag are his work.
12 Kuchita zoyipa kumanyansa mafumu, pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wake.
It is an abomination to kings to commit wickedness, for the throne is established by righteousness.
13 Mawu owona amakondweretsa mfumu. Iyo imakonda munthu woyankhula choonadi.
Righteous lips are the delight of kings, and they love him who speaks right.
14 Ukali wa mfumu ndi mthenga wa imfa, koma munthu wanzeru amawupepesa ukaliwo.
The wrath of a king is messengers of death, but a wise man will pacify it.
15 Kuwala kwa nkhope ya mfumu kumapatsa moyo; ndipo kukoma mtima kwake kuli ngati mitambo ya mvula nthawi ya chilimwe.
In the light of the king's countenance is life, and his favor is as a cloud of the latter rain.
16 Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.
How much better it is to get wisdom than gold! Yea, to get understanding is rather to be chosen than silver.
17 Msewu wa munthu wowongoka mtima umapewa zoyipa; wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.
The highway of the upright is to depart from evil. He who keeps his way preserves his soul.
18 Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wodzikuza adzagwa.
Pride is before destruction, and a haughty spirit before a fall.
19 Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa, kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.
Better it is to be of a lowly spirit with the poor, than to divide the spoil with the proud.
20 Munthu womvera malangizo zinthu zimamuyendera bwino, ndipo wodala ndi amene amadalira Yehova.
He who gives heed to the word shall find good, and whoever trusts in Jehovah, happy is he.
21 A mtima wanzeru amatchedwa ozindikira zinthu, ndipo mawu ake okoma amawonjezera nzeru.
The wise in heart shall be called prudent, and the sweetness of the lips increases learning.
22 Kumvetsa zinthu ndi kasupe wa moyo kwa iwo amene ali nako, koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa zitsiru.
Understanding is a well-spring of life to him who has it, but the correction of fools is folly.
23 Mtima wanzeru umathandiza munthu kuyankhula mwa nzeru, ndipo mawu ake amawonjezera nzeru.
The heart of the wise instructs his mouth, and adds learning to his lips.
24 Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.
Pleasant words are a honeycomb: Sweet to the soul, and health to the bones.
25 Pali njira ina yooneka ngati yowongoka kwa munthu koma kumatsiriziro kwake ndi imfa.
There is a way which seems right to a man, but the end thereof are the ways of death.
26 Njala ya munthu wantchito imamuthandiza kulimbikira; njalayo imamukakamiza kuchitapo kanthu.
The appetite of the laboring man labors for him, for his mouth urges him.
27 Munthu wopanda pake amakonzekera kuchita zoyipa ndipo mawu ake ali ngati moto wopsereza.
A worthless man devises mischief, and in his lips there is as a scorching fire.
28 Munthu woyipa mtima amayambitsa mikangano, ndipo miseche imalekanitsa anthu okondana kwambiri.
A perverse man scatters abroad strife, and a whisperer separates chief friends.
29 Munthu wandewu amakopa mnansi wake, ndipo amamuyendetsa njira imene si yabwino.
A man of violence entices his neighbor, and leads him in a way that is not good.
30 Amene amatsinzinira maso ake amalingalira zinthu zokhota; amene amachita msunamo amakonzeka kuchita zoyipa.
He who shuts his eyes devises perverse things. He who moves his lips brings evil to pass.
31 Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero; munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.
The hoary head is a crown of glory. It shall be found in the way of righteousness.
32 Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo, munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.
He who is slow to anger is better than the mighty, and he who rules his spirit, than he who takes a city.
33 Maere amaponyedwa pa mfunga, koma ndiye Yehova amene amalongosola zonse.
The lot is cast into the lap, but the whole disposing thereof is of Jehovah.

< Miyambo 16 >