< Obadiya 1 >

1 Masomphenya a Obadiya. Ambuye Yehova akunena kwa Edomu kuti, Tamva uthenga wochokera kwa Yehova: Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu kukanena kuti, “Konzekani, tiyeni tikachite nkhondo ndi Edomu.”
The vision of Obadiah. Thus says the lord Jehovah concerning Edom: We have heard tidings from Jehovah, and an ambassador is sent among the nations, saying, Arise ye, and let us rise up against her in battle.
2 “Taona, ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina; udzanyozedwa kwambiri.
Behold, I have made thee small among the nations. Thou are greatly despised.
3 Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali, iwe amene umanena mu mtima mwako kuti, ‘Ndani anganditsitse pansi?’
The pride of thy heart has deceived thee, O thou who dwell in the clefts of the rock, whose habitation is high, who says in his heart, Who shall bring me down to the ground?
4 Koma ngakhale umawuluka ngati chiwombankhanga ndi kumanga chisa chako pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.
Though thou mount on high as the eagle, and though thy nest be set among the stars, I will bring thee down from there, says Jehovah.
5 “Anthu akuba akanabwera kwa iwe, kapena anthu olanda zinthu akanafika usiku, aa, tsoka lanji limene likukudikira iwe! Kodi akanangotengako zimene akuzifuna zokha? Ngati anthu othyola mphesa akanafika, kodi akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?
If thieves came to thee, if robbers by night (how thou are cut off!), would they not steal only till they had enough? If grape gatherers came to thee, would they not leave some gleaning grapes?
6 Koma Esau adzalandidwa zinthu zonse, chuma chake chobisika chidzabedwa!
How are the things of Esau searched! How are his hidden treasures sought out!
7 Anthu onse ogwirizana nawo adzakupirikitsira kumalire; abwenzi ako adzakunyenga ndi kukugonjetsa; amene amadya chakudya chako adzakutchera msampha, koma iwe sudzazindikira zimenezi.”
All the men of thy confederacy have brought thee on thy way, even to the border. The men who were at peace with thee have deceived thee, and prevailed against thee. Those who eat thy bread lay a snare under thee. There is no understanding in him.
8 Yehova akunena kuti, “Tsiku limenelo, kodi sindidzawononga anthu onse anzeru a ku Edomu, anthu odziwa zinthu mʼmapiri a Esau?
Shall I not in that day, says Jehovah, destroy the wise men out of Edom, and understanding out of the mount of Esau?
9 Ankhondo ako, iwe Temani, adzachita mantha, ndipo aliyense amene ali mʼphiri la Esau adzaphedwa pa nkhondo.
And thy mighty men, O Teman, shall be dismayed, to the end that everyone may be cut off from the mount of Esau by slaughter.
10 Chifukwa cha nkhanza zimene unachitira mʼbale wako Yakobo, udzakhala wamanyazi; adzakuwononga mpaka muyaya.
Shame shall cover thee for the violence done to thy brother Jacob, and thou shall be cut off forever.
11 Pamene adani ankamulanda chuma chake pamene alendo analowa pa zipata zake ndi kuchita maere pa Yerusalemu, pa tsikulo iwe unali ngati mmodzi wa iwo.
In the day that thou stood on the other side, in the day that strangers carried away his substance, and foreigners entered into his gates, and cast lots upon Jerusalem, even thou were as one of them.
12 Iwe sunayenera kunyoza mʼbale wako pa nthawi ya tsoka lake, kapena kunyogodola Ayuda chifukwa cha chiwonongeko chawo, kapena kuwaseka pa nthawi ya mavuto awo.
But look not thou on the day of thy brother in the day of his disaster, and rejoice not over the sons of Judah in the day of their destruction, nor speak proudly in the day of distress.
13 Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu anga pa nthawi ya masautso awo, kapena kuwanyogodola pa tsiku la tsoka lawo, kapena kulanda chuma chawo pa nthawi ya masautso awo.
Enter not into the gate of my people in the day of their calamity. Yea, look not thou on their affliction in the day of their calamity, nor lay ye hands on their substance in the day of their calamity.
14 Sunayenera kudikirira pamphambano ya misewu kuti uphe Ayuda othawa, kapena kuwapereka kwa adani awo Ayuda opulumuka pa nthawi ya mavuto awo.”
And stand thou not in the crossway, to cut off those of his who escape, and deliver not up those of his who remain in the day of distress.
15 “Tsiku la Yehova layandikira limene adzaweruza mitundu yonse ya anthu. Adzakuchitira zomwe unawachitira ena; zochita zako zidzakubwerera wekha.
For the day of Jehovah is near upon all the nations. As thou have done, it shall be done to thee. Thy dealing shall return upon thine own head.
16 Iwe unamwa pa phiri langa loyera, koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza; iwo adzamwa ndi kudzandira ndipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi.
For as ye have drunk upon my holy mountain, so shall all the nations drink continually. Yea, they shall drink, and swallow down, and shall be as though they had not been.
17 Koma pa Phiri la Ziyoni padzakhala chipulumutso; phirilo lidzakhala lopatulika, ndipo nyumba ya Yakobo idzalandira cholowa chake.
But in mount Zion there shall be those who escape, and it shall be holy, and the house of Jacob shall possess their possessions.
18 Nyumba ya Yakobo idzasanduka moto ndipo nyumba ya Yosefe idzasanduka lawi la moto; nyumba ya Esau idzasanduka chiputu, ndipo adzayitenthe pa moto ndi kuyipsereza. Sipadzakhala anthu opulumuka kuchokera mʼnyumba ya Esau.” Yehova wayankhula.
And the house of Jacob shall be a fire, and the house of Joseph a flame, and the house of Esau for stubble. And they shall burn among them, and devour them, and there shall not be any remaining to the house of Esau, for Jehovah has spoken it.
19 Anthu ochokera ku Negevi adzakhala ku mapiri a Esau, ndipo anthu ochokera mʼmbali mwa mapiri adzatenga dziko la Afilisti. Adzakhala mʼminda ya Efereimu ndi Samariya, ndipo Benjamini adzatenga Giliyadi.
And those of the South shall possess the mount of Esau, and those of the lowland the Philistines. And they shall possess the field of Ephraim, and the field of Samaria, and Benjamin shall possess Gilead.
20 Aisraeli amene ali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati; a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda ya ku Negevi.
And the captives of this host of the sons of Israel, who are among the Canaanites, shall possess even to Zarephath. And the captives of Jerusalem who are in Sepharad shall possess the cities of the South.
21 Opulumukawo adzapita ku Phiri la Ziyoni ndipo adzalamulira mapiri a Esau. Koma ufumuwo udzakhala wa Yehova.
And saviors shall come up on mount Zion to judge the mount of Esau, and the kingdom shall be Jehovah's.

< Obadiya 1 >