< Yeremiya 42 >

1 Atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya ndi Azariya mwana wa Hosayia, ndiponso anthu onse, ana ndi akuluakulu omwe, anapita
Then all the captains of the forces, and Johanan the son of Kareah, and Jezaniah the son of Hoshaiah, and all the people from the least even to the greatest, came near,
2 kwa mneneri Yeremiya ndipo anamuwuza kuti, “Chonde imvani dandawulo lathu ndipo mutipempherere anthu otsalafe kwa Yehova Mulungu wanu. Pakuti monga tsopano mukuona, ngakhale kuti kale tinalipo ambiri, koma tsopano ochepa okha ndiye amene atsala.
and said to Jeremiah the prophet, Let, we pray thee, our supplication be presented before thee, and pray for us to Jehovah thy God, even for all this remnant, for we are left but a few of many, as thine eyes do behold us,
3 Mupemphere kuti Yehova Mulungu wanu atiwuze kumene tiyenera kupita ndi chimene tiyenera kuchita.”
that Jehovah thy God may show us the way in which we should walk, and the thing that we should do.
4 Mneneri Yeremiya anawayankha kuti, “Ndamva zimene mwanenazi. Ndithu ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga momwe mwandipemphera. Ndidzakuwuzani chilichonse chimene Yehova anene ndipo sindidzakubisirani kanthu kalikonse.”
Then Jeremiah the prophet said to them, I have heard you. Behold, I will pray to Jehovah your God according to your words, and it shall come to pass that whatever thing Jehovah shall answer you, I will declare it to you. I will keep nothing back from you.
5 Ndipo iwo anawuza Yeremiya kuti, “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ife ngati sitichita mogwirizana ndi chilichonse chimene Yehova Mulungu adzakutumani kuti mutiwuze.
Then they said to Jeremiah, Jehovah be a true and faithful witness amongst us, if we do not according to all the word with which Jehovah thy God shall send thee to us.
6 Kaya ndi zotikomera kapena zosatikomera, ife tidzamvera Yehova Mulungu wathu, amene takutumaniko. Tidzamvera Yehova Mulungu wathu kuti zinthu zidzatiyendere bwino.”
Whether it be good, or whether it be evil, we will obey the voice of Jehovah our God, to whom we send thee, that it may be well with us when we obey the voice of Jehovah our God.
7 Patapita masiku khumi, Yehova anayankhula ndi Yeremiya.
And it came to pass after ten days, that the word of Jehovah came to Jeremiah.
8 Choncho Yeremiya anayitana Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye ndiponso anthu onse, ana ndi akulu omwe.
Then he called Johanan the son of Kareah, and all the captains of the forces who were with him, and all the people from the least even to the greatest,
9 Yehova, Mulungu wa Israeli amene munanditumako kuti ndikapereke madandawulo mʼdzina lanu akuti,
and said to them, Thus says Jehovah, the God of Israel, to whom ye sent me to present your supplication before him:
10 “Ngati mukhala mʼdziko muno, ndiye kuti ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani. Inde ndidzakudzalani osakuchotsani pakuti ndi kumva chisoni kwambiri chifukwa cha mavuto amene ndabweretsa pa inu.
If ye will still abide in this land, then I will build you, and not pull you down, and I will plant you, and not pluck you up, for I relent of the evil that I have done to you.
11 Musayiope mfumu ya ku Babuloni, imene mukuyiopa tsopano. Musachite nayo mantha, akutero Yehova, pakuti Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani ndi kukulanditsani mʼmanja mwake.
Be not afraid of the king of Babylon, of whom ye are afraid. Be not afraid of him, says Jehovah, for I am with you to save you, and to deliver you from his hand.
12 Ndidzakuchitirani chifundo, ndipo mfumuyonso idzakuchitirani chifundo ndi kukulolani kuti mukhale mʼdziko mwanumwanu.
And I will grant you mercy, that he may have mercy upon you, and cause you to return to your own land.
13 “Koma mwina simudzamvera Yehova Mulungu wanu nʼkumanena kuti, ‘Ayi ife sitidzakhala mʼdziko muno,
But if ye say, We will not dwell in this land, so that ye do not obey the voice of Jehovah your God,
14 ndipo ngati mukunena kuti, ‘Ayi, koma tidzapita ku Igupto kumene sitidzaonako nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga kapenanso kusowa chakudya.’
saying, No, but we will go into the land of Egypt, where we shall see no war, nor hear the sound of the trumpet, nor have hunger of bread, and we will dwell there-
15 Tsono, inu otsala a ku Yuda, imvani mawu a Yehova. Iye akuti, ngati mutsimikiza zopita ku Igupto, nʼkupitadi kukakhala kumeneko,
Now therefore hear ye the word of Jehovah, O remnant of Judah. Thus says Jehovah of hosts, the God of Israel: If ye indeed set your faces to enter into Egypt, and go to sojourn there,
16 ndiye nkhondo imene mukuyiopayo idzakugonjetsani ku Igupto komweko. Njala imene mukuyiopayo idzakupezani ku Igupto komweko ndipo mudzafera kumeneko.
then it shall come to pass, that the sword, which ye fear, shall overtake you there in the land of Egypt, and the famine, of which ye are afraid, shall follow hard after you there in Egypt, and there ye shall die.
17 Kunena zoona, onse amene atsimikiza zopita ku Igupto kuti akakhale kumeneko adzafa ndi nkhondo njala ndi mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumuke kapena kuthawa mavuto amene ndidzawagwetsera.’
So shall it be with all the men who set their faces to go into Egypt to sojourn there. They shall die by the sword, by the famine, and by the pestilence, and none of them shall remain or escape from the evil that I will bring upon them.
18 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Momwe ndinawakwiyira mwaukali anthu okhala mu Yerusalemu, koteronso ndidzakukwiyirani mukapita ku Igupto. Mudzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, choseketsa ndi chonyozeka. Malo ano simudzawaonanso.’
For thus says Jehovah of hosts, the God of Israel: As my anger and my wrath has been poured forth upon the inhabitants of Jerusalem, so shall my wrath be poured forth upon you when ye shall enter into Egypt. And ye shall be an execration, and an astonishment, and a curse, and a reproach. And ye shall see this place no more.
19 “Inu otsala a ku Yuda, Yehova wakuwuzani kuti, ‘Musapite ku Igupto.’ Dziwani chinthu ichi: Ine lero ndikukuchenjezani
Jehovah has spoken concerning you, O remnant of Judah, Go ye not into Egypt. Know certainly that I have testified to you this day.
20 kuti munalakwitsa kwambiri. Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu nʼkumati ‘Mukatipempherere kwa Yehova Mulungu wathu, nʼkudzatiwuza chimene afuna kuti tichite, ndipo ife tidzachita.’
For ye have dealt deceitfully against your own souls. For ye sent me to Jehovah your God, saying, Pray for us to Jehovah our God, and according to all that Jehovah our God shall say, so declare to us, and we will do it.
21 Ine lero ndakuwuzani, koma inu simukumverabe zonse zimene Yehova Mulungu anandituma kuti ndikuwuzeni.
And I have this day declared it to you. But ye have not obeyed the voice of Jehovah your God in anything for which he has sent me to you.
22 Tsono dziwani ichi: mudzafadi ndi nkhondo, njala ndi mliri kumalo kumene mukufuna mukakhaleko.”
Now therefore know certainly that ye shall die by the sword, by the famine, and by the pestilence, in the place where ye desire to go to sojourn there.

< Yeremiya 42 >