< Ezekieli 13 >

1 Yehova anayankhulanso nane kuti,
And the word of Jehovah came to me, saying,
2 “Iwe mwana wa munthu unenere modzudzula aneneri a Israeli amene akunenera za kukhosi kwawo. Uwawuze iwowa kuti, ‘Imvani mawu a Yehova!’
Son of man, prophesy against the prophets of Israel who prophesy, and say thou to those who prophesy out of their own heart, Hear ye the word of Jehovah.
3 Ambuye Yehova akuti, ‘Tsoka kwa aneneri opusa amene amangonenera zopeka ngakhale kuti sanaone kanthu konse!’
Thus says the lord Jehovah: Woe to the foolish prophets, who follow their own spirit, and have seen nothing!
4 Iwe Israeli, aneneri ako ali ngati nkhandwe pa mabwinja.
O Israel, thy prophets have been like foxes in the waste places.
5 Simunakwere khoma kuti mukakonze mʼmene munagumuka, kuti Aisraeli adziteteze kolimba pa nkhondo pa tsiku la Yehova.
Ye have not gone up into the gaps, nor built up the wall for the house of Israel to stand in the battle in the day of Jehovah.
6 Masomphenya awo ndi achabe ndipo kuwombeza kwawo ndi kwabodza. Iwo amati, ‘Yehova akutero,’ pomwe Yehova sanawatume. Komabe iwo amayembekezera kuti zimene ayankhulazo zichitikadi.
They have seen falsehood and lying divination, who say, Jehovah says, but Jehovah has not sent them. And they have made men to hope that the word would be confirmed.
7 Koma Ine ndikuti masomphenya anu ngachabechabe ndi zimene mwawombedzazo nʼzabodza. Mumanena kuti, ‘Akutero Yehova,’ pamene sindinayankhule nʼkomwe.
Have ye not seen a false vision, and have ye not spoken a lying divination, in that ye say, Jehovah says, albeit I have not spoken?
8 “Tsono Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndikukutsutsani chifukwa cha zoyankhula zanu zonama ndi masomphenya anu abodzawo. Ndikutero Ine Yehova.
Therefore thus says the lord Jehovah: Because ye have spoken falsehood, and seen lies, therefore, behold, I am against you, says the lord Jehovah.
9 Ndidzalanga aneneri amene amanenera zabodza za zinthu zimene amati anaziona mʼmasomphenya. Sadzakhala nawo mʼbwalo la anthu anga ndipo mayina awo sadzalembedwa mu kawundula wa nzika za Israeli. Sadzalowa nawo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
And my hand shall be against the prophets who see false visions, and who divine lies. They shall not be in the council of my people, nor shall they be written in the writing of the house of Israel, neither shall they enter into the land of Israel. And ye shall know that I am the lord Jehovah.
10 “Popeza kuti aneneri asocheretsa anthu anga pomanena kuti, ‘Kuli mtendere’ pamene mtendere palibe; ndiponso anthu akamanga khoma iwo nʼkumalipaka njereza,
Because, even because they have seduced my people, saying, Peace, and there is no peace, and when a man builds up a wall, behold, they daub it with untempered mortar,
11 choncho ufotokozere amene alipaka njerezawo kuti khomalo lidzagwa. Mvula idzagwa mwamphamvu, kudzagwa matalala akuluakulu, ndipo kudzawomba mphepo yamkuntho.
say to those who daub it with untempered mortar, that it shall fall. There shall be an overflowing shower, and ye, O great hailstones, shall fall, and a stormy wind shall rend it.
12 Pamene khomalo lagwa, kodi anthu sadzakufunsani kuti, ‘Kodi njereza yemwe munapaka uja ali kuti?’
Lo, when the wall has fallen, shall it not be said to you, Where is the daubing with which ye have daubed it?
13 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Mwa ukali ndidzakunthitsa mphepo ya mkuntho. Ndidzagwetsa matalala akuluakulu ndili ndi ukali ndipo ndidzavumbwitsa mvula yamphamvu ndi mkwiyo mpaka khomalo litawonongeka kotheratu.
Therefore thus says the lord Jehovah: I will even rend it with a stormy wind in my wrath, and there shall be an overflowing shower in my anger, and great hailstones in wrath to consume it.
14 Ndidzagwetsa khoma limene munalipaka njerezalo. Ndidzaligumuliratu mpaka pansi kotero kuti maziko ake adzaoneka. Khomalo likadzagwa, inu mudzawonongekamo; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
So I will break down the wall that ye have daubed with untempered mortar, and bring it down to the ground, so that the foundation thereof shall be uncovered. And it shall fall, and ye shall be consumed in the midst of it. And ye shall know that I am Jehovah.
15 Kotero ndidzagwiritsa ntchito mkwiyo wanga pa khomali ndi pa amene analipaka njereza. Pambuyo pake ndidzakuwuzani kuti, ‘Khoma lagwa pamodzi ndi amene analipaka njereza.
Thus I will accomplish my wrath upon the wall, and upon those who have daubed it with untempered mortar. And I will say to you, The wall is no more, nor those who daubed it,
16 Agwanso aneneri a Yerusalemu amene ankalosa za Yerusalemu nʼkumati anaona mʼmasomphenya za mtendere wa Yerusalemu pamene mtendere kunalibe konse, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.’
namely, the prophets of Israel who prophesy concerning Jerusalem, and who see visions of peace for her, and there is no peace, says the lord Jehovah.
17 “Tsono iwe mwana wa munthu, yankhulapo pa nkhani za akazi amene ali pakati pa anthu ako. Iwo amanenera zopeka za mʼmutu mwawo. Tsono adzudzule.
And thou, son of man, set thy face against the daughters of thy people, who prophesy out of their own heart, and prophesy thou against them.
18 Uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu za kumutu za anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nʼkupulumutsa moyo wanu?
And say, Thus says the lord Jehovah: Woe to the women who sew pillows upon all elbows, and make headdresses for the head of every stature to hunt souls! Will ye hunt the souls of my people, and save souls alive for yourselves?
19 Ponamiza anthu anga amene amamva za mabodza anu, inu mwapha anthu amene sanayenera kufa ndipo mwasiya ndi moyo amene sanayenera kukhala ndi moyo.
And ye have profaned me among my people for handfuls of barley and for pieces of bread, to kill the souls who should not die, and to save the souls alive who should not live, by your lying to my people who listen to lies.
20 “‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikudana ndi zithumwa zanu zimene mumakokera nazo mitima ya anthu ngati mbalame. Ndidzazingʼamba kudzichotsa pa mikono yanu. Choncho ndidzapulumutsa miyoyo ya anthu amene munawakola ngati mbalame.
Therefore thus says the lord Jehovah: Behold, I am against your pillows, with which ye hunt the souls there to make fly, and I will tear them from your arms. And I will let the souls go, even the souls that ye hunt to make fly.
21 Ndidzangʼamba nsalu zanu za matsengazo ndi kupulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu, ndipo simudzakhalanso ndi mphamvu yowakolera. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
I will also tear your headdresses, and deliver my people out of your hand, and they shall no more be in your hand to be hunted. And ye shall know that I am Jehovah.
22 Popeza kuti munatayitsa mtima anthu olungama ngakhale sindinafune kuti ataye mtima; ndipo munalimbitsa anthu oyipa kuti asaleka machimo awo motero sakutha kupulumutsa moyo wawo,
Because with lies ye have grieved the heart of the righteous, whom I have not made sad, and strengthened the hands of the wicked, that he should not return from his wicked way, and be saved alive.
23 choncho inu simudzaonanso masomphenya abodza kapena kuwombeza. Ine ndidzapulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu. Ndipo pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’”
Therefore ye shall no more see false visions, nor divine divinations. And I will deliver my people out of your hand. And ye shall know that I am Jehovah.

< Ezekieli 13 >