< Danieli 5 >

1 Tsiku lina mfumu Belisazara anakonza phwando lalikulu la akalonga ake 1,000 ndipo anamwa vinyo pamodzi ndi iwo.
Belshazzar the king made a great feast for a thousand of his lords, and drank wine before the thousand.
2 Pamene Belisazara ankamwa vinyo, analamula kuti ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara abambo ake anakatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu zikatengedwe kuti mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi amweremo.
Belshazzar, while he tasted the wine, commanded to bring the golden and silver vessels which Nebuchadnezzar his father had taken out of the temple which was in Jerusalem, that the king and his lords, his wives and his concubines, might drink from there.
3 Choncho anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga mʼNyumba ya Mulungu; ndipo mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi ake anamweramo.
Then they brought the golden vessels that were taken out of the temple of the house of God which was at Jerusalem. And the king and his lords, his wives and his concubines, drank from them.
4 Akumwa vinyo, anatamanda milungu yagolide ndi siliva, yamkuwa, chitsulo, yamtengo ndi mwala.
They drank wine, and praised the gods of gold, and of silver, of brass, of iron, of wood, and of stone.
5 Mwadzidzidzi zala za dzanja la munthu zinaonekera ndi kulemba pa khoma, pafupi ndi choyikapo nyale mʼnyumba yaufumu. Mfumu inapenyetsetsa dzanjalo pamene limalemba.
In the same hour the fingers of a man's hand came forth, and wrote opposite the lampstand upon the plaster of the wall of the king's palace. And the king saw the part of the hand that wrote.
6 Nkhope yake inasandulika ndipo inachita mantha, nkhongono zii, mawondo gwedegwede.
Then the king's countenance was changed in him, and his thoughts troubled him. And the joints of his loins were loosed, and his knees smote one against another.
7 Mfumu inafuwula kuyitana owombeza, alawuli ndi amawula kuti abwere. Ndipo anawawuza anthu anzeru a ku Babuloni kuti, “Aliyense amene awerenge malembawa ndi kundiwuza tanthauzo lake adzavekedwa chovala cha pepo ndi mkanda wa golide udzavekedwa mʼkhosi mwake, ndipo adzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”
The king cried aloud to bring in the enchanters, the Chaldeans, and the soothsayers. The king spoke and said to the wise men of Babylon, Whoever shall read this writing, and show me the interpretation of it, shall be clothed with purple, and have a chain of gold about his neck, and shall be the third ruler in the kingdom.
8 Pamenepo anzeru onse a mfumu anabwera, koma sanakwanitse kuwerenga malembawo kapena kumutanthauzira mfumu.
Then all the king's wise men came in, but they could not read the writing, nor make known to the king the interpretation.
9 Choncho mfumu Belisazara anachita mantha koposa ndipo nkhope yake inapitirira kusinthika. Akalonga ake anathedwa nzeru.
Then king Belshazzar was greatly troubled, and his countenance was changed in him, and his lords were perplexed.
10 Mfumukazi, pakumva mawu a mfumu ndi akalonga ake, analowa mʼchipinda cha phwando ndipo anati, “Mfumu mukhale ndi moyo wautali! Musavutike! Nkhope yanu isasinthike!
Now the queen came into the banquet house because of the words of the king and his lords. The queen spoke and said, O king, live forever. Let not thy thoughts trouble thee, nor let thy countenance be changed.
11 Pali munthu wina mu ufumu wanu uno amene mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera. Pa nthawi ya ulamuliro wa abambo anu iye anapezeka kuti ali ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zonga za milungu. Mfumu Nebukadinezara, abambo anu, Ine ndikukuwuzani anamusankha iye kukhala mkulu wa amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula.
There is a man in thy kingdom, in whom is the spirit of the holy gods. And in the days of thy father light and understanding and wisdom, like the wisdom of the gods, were found in him. And the king Nebuchadnezzar thy father, the king, I say, thy father, made him master of the magicians, enchanters, Chaldeans, and soothsayers,
12 Munthu ameneyu dzina lake ndi Danieli, koma mfumu inamutcha Belitesezara ndipo ali ndi nzeru zapadera, ndi wodziwa ndi kuzindikira zinthu, ndiponso luso lakutanthauzira maloto, kufotokozera miyambi ndi kuthetsa mavuto osautsa. Muyitaneni Danieli, ndipo adzakuwuzani chomwe mawuwa akutanthauza.”
inasmuch as an excellent spirit, and knowledge, and understanding, interpreting of dreams, and showing of dark sentences, and dissolving of doubts, were found in the same Daniel, whom the king named Belteshazzar. Now let Daniel be called, and he will show the interpretation.
13 Choncho anabwera naye Danieli pamaso pa mfumu ndipo inati kwa iye, “Kodi ndiwe Danieli, mmodzi mwa akapolo omwe abambo anga mfumu anabwera nawo kuchoka ku Yuda?
Then Daniel was brought in before the king. The king spoke and said to Daniel, Are thou that Daniel, who are of the sons of the captivity of Judah, whom my father the king brought out of Judah?
14 Ndamva kuti mzimu wa milungu uli mwa iwe ndi kuti uli ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zapadera.
I have heard of thee, that the spirit of the gods is in thee, and that light and understanding and excellent wisdom are found in thee.
15 Anzeru ndi owombeza anabwera pamaso panga kuti awerenge zolembedwazi ndi kundiwuza tanthauzo lake koma sanakwanitse kundifotokozera.
And now the wise men, the enchanters, have been brought in before me, that they should read this writing, and make known to me the interpretation of it, but they could not show the interpretation of the thing.
16 Tsopano ndamva kuti iwe ukhoza kupereka matanthauzo ndi kuthetsa mavuto. Ngati ungawerenge zolembedwazi ndi kundiwuza tanthauzo lake, udzavekedwa chovala cha pepo ndi kuyikidwa mkanda wa golide mʼkhosi mwako, ndipo udzakhala wolamulira wachitatu mu ufumu uno.”
But I have heard of thee, that thou can give interpretations, and dissolve doubts. Now if thou can read the writing, and make known to me the interpretation of it, thou shall be clothed with purple, and have a chain of gold about thy neck, and shall be the third ruler in the kingdom.
17 Pamenepo Danieli anayankha mfumu kuti, “Inu musunge mphatso zanuzo kwa inu nokha ndipo mupereke mphothoyo kwa wina aliyense. Komabe ine ndi kuwerengerani malembawa mfumu; ndikukuwuzani tanthauzo lake.
Then Daniel answered and said before the king, Let thy gifts be to thyself, and give thy rewards to another. Nevertheless I will read the writing to the king, and make known to him the interpretation.
18 “Inu mfumu, Mulungu Wammwambamwamba anapatsa abambo anu Nebukadinezara mphamvu ndi ukulu ndi ulemerero ndi ufumu.
O thou king, the Most High God gave Nebuchadnezzar thy father the kingdom and greatness and glory and majesty.
19 Chifukwa cha udindo waukulu umene anapatsidwanso, anthu onse ndi mitundu ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana ankanjenjemera ndikumuopa iye. Amene mfumu inafuna anawaphadi; amene inafuna kuwasunga, inawasunga; amene inafuna kuwakweza, inawakweza; ndipo amene inafuna kuwatsitsa, inawatsitsa.
And because of the greatness that he gave him, all the peoples, nations, and languages trembled and feared before him. Whom he wanted, he killed, and whom he wanted, he kept alive, and whom he wanted, he raised up, and whom he wanted, he put down.
20 Koma pamene inayamba kudzitama ndi kuwumitsa mtima wake ndi kuyamba kunyada, inachotsedwa pa mpando wake waufumu ndi kulandidwa ulemerero wake.
But when his heart was lifted up, and his spirit was hardened so that he dealt proudly, he was deposed from his kingly throne. And they took his glory from him,
21 Iyo inachotsedwa pakati pa anthu ndi kupatsidwa mtima ngati wa nyama; inakhala pamodzi ndi abulu akutchire ndi kudya udzu ngati ngʼombe; ndipo thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anavomereza kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye wolamulira maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene Iye wafuna.
and he was driven from the sons of men. And his heart was made like the beasts, and his dwelling was with the wild donkeys. He was fed with grass like oxen, and his body was wet with the dew of heaven, until he knew that the Most High God rules in the kingdom of men, and that he sets up over it whomever he will.
22 “Koma inu mwana wake, Belisazara, simunadzichepetse, ngakhale kuti mumadziwa zonsezi.
And thou his son, O Belshazzar, have not humbled thy heart, though thou knew all this,
23 Mʼmalo mwake, mwadzikweza nokha kutsutsana ndi Ambuye wakumwamba. Inu mwatenga ziwiya za mʼNyumba mwake, ndipo inu ndi akalonga anu, akazi anu ndi azikazi anu mwamwera vinyo mu zimenezi. Inu munatamanda milungu yasiliva ndi golide, yamkuwa, chitsulo, mtengo ndi mwala, imene singaone kapena kumva kapena kuzindikira. Koma simunamupatse ulemu Mulungu amene asunga mʼmanja mwake moyo wanu ndi njira zanu zonse.
but have lifted up thyself against the Lord of heaven. And they have brought the vessels of his house before thee, and thou and thy lords, thy wives and thy concubines, have drunk wine from them. And thou have praised the gods of silver and gold, of brass, iron, wood, and stone, which neither see, nor hear, nor know. And the God in whose hand thy breath is, and whose are all thy ways, thou have not glorified.
24 Choncho Iye watumiza dzanja limene lalemba mawu amenewa.
Then the part of the hand was sent from before him, and this writing was inscribed.
25 “Mawu amene analembedwa ndi awa: MENE, MENE, TEKELI, PARASINI.
And this is the writing that was inscribed: MENE, MENE, TEKEL, UPHARSIN.
26 “Zimene mawuwa akutanthauza ndi izi:
This is the interpretation of the thing: MENE, God has numbered thy kingdom, and brought it to an end.
27 Tekeli: Inu mwayesedwa pa sikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera.
TEKEL, thou are weighed in the balances, and are found wanting.
28 Parasini: Ufumu wanu wagawidwa ndi kupatsidwa kwa Amedi ndi Aperezi.”
PERES, thy kingdom is divided, and given to the Medes and Persians.
29 Mwa lamulo la Belisazara, Danieli anavekedwa chovala cha pepo, mkanda wagolide unayikidwa mʼkhosi mwake, ndipo analengeza kuti anali wachitatu mu ulamuliro mu ufumuwo.
Then Belshazzar commanded, and they clothed Daniel with purple, and put a chain of gold about his neck, and made proclamation concerning him, that he should be the third ruler in the kingdom.
30 Usiku womwewo Belisazara, mfumu ya anthu a ku Babuloni, inaphedwa,
In that night Belshazzar the Chaldean King was slain.
31 ndipo Dariyo Mmedi analanda ufumuwo ali ndi zaka 62.
And Darius the Mede received the kingdom, being about sixty-two years old.

< Danieli 5 >