< 2 Mbiri 22 >

1 Anthu a mu Yerusalemu anayika Ahaziya mwana wamngʼono kwambiri wa Yehoramu kukhala mfumu mʼmalo mwake, popeza gulu lankhondo limene linabwera ndi Aarabu ku misasa, linapha ana onse aakulu. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
And the inhabitants of Jerusalem made Ahaziah his youngest son king in his stead, for the band of men who came with the Arabians to the camp had slain all the eldest. So Ahaziah the son of Jehoram king of Judah reigned.
2 Ahaziya anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Dzina la amayi ake linali Ataliya, chidzukulu cha Omuri.
Ahaziah was twenty-two years old when he began to reign, and he reigned one year in Jerusalem. And his mother's name was Athaliah the daughter of Omri.
3 Nayenso anayenda mʼnjira ya banja la Ahabu, pakuti amayi ake anamulimbikitsa kuchita zolakwika.
He also walked in the ways of the house of Ahab. For his mother was his counselor to do wickedly.
4 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe banja la Ahabu linachitira, pakuti atamwalira abambo ake, iwo anakhala alangizi ake, kumene kunali kudziwononga kwake.
And he did that which was evil in the sight of Jehovah, as did the house of Ahab. For they were his counselors after the death of his father, to his destruction.
5 Iyeyo anatsatiranso uphungu wawo pamene anapita ndi Yehoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya Israeli kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yehoramu,
He walked also after their counsel, and went with Jehoram the son of Ahab king of Israel to war against Hazael king of Syria at Ramoth-gilead. And the Syrians wounded Joram.
6 kotero iye anabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene anamuvulaza ku Ramoti pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aaramu. Ndipo Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezireeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anavulazidwa.
And he returned to be healed in Jezreel of the wounds which they had given him at Ramah when he fought against Hazael king of Syria. And Azariah the son of Jehoram king of Judah went down to see Jehoram the son of Ahab in Jezreel because he was sick.
7 Mulungu anakonza kuti Ahaziya akaphedwe pa ulendo wake wokacheza. Ahaziya atafika, iye ndi Yoramu anapita kukakumana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamudzoza kuti akawononge banja la Ahabu.
Now the destruction of Ahaziah was of God, in that he went to Joram, for when he came he went out with Jehoram against Jehu the son of Nimshi, whom Jehovah had anointed to cut off the house of Ahab.
8 Pamene Yehu ankalanga banja la Ahabu anapeza atsogoleri a ku Yuda ndiponso ana aamuna a abale ake a Ahaziya amene amatumikira Ahaziya, ndipo anawapha.
And it came to pass, when Jehu was executing judgment upon the house of Ahab, that he found the rulers of Judah, and the sons of the brothers of Ahaziah, ministering to Ahaziah, and killed them.
9 Kenaka anapita kukafunafuna Ahaziya, ndipo anthu ake anagwira Ahaziya pamene amabisala mu Samariya. Anabwera naye kwa Yehu ndipo anaphedwa. Iwo anamuyika mʼmanda, pakuti anati, “Iyeyu anali mwana wa Yehosafati amene anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” Kotero panalibe wamphamvu mʼbanja la Ahaziya kuti nʼkukhala mfumu.
And he sought Ahaziah, and they caught him (now he was hiding in Samaria). And they brought him to Jehu, and killed him. And they buried him, for they said, He is the son of Jehoshaphat, who sought Jehovah with all his heart. And the house of Ahaziah had no power to hold the kingdom.
10 Ataliya, amayi ake a Ahaziya, ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakapha onse a banja laufumu la Yuda.
Now when Athaliah the mother of Ahaziah saw that her son was dead, she arose and destroyed all the royal seed of the house of Judah.
11 Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, momuba ndi kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene amati aphedwe ndipo anamuyika iye ndi mlezi wake mʼchipinda chogona. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa wansembe Yehoyada, yemwe anali mlongo wake wa Ahaziya anamubisa mwanayo kuti Ataliya asamuphe.
But Jehoshabeath, the daughter of the king, took Joash the son of Ahaziah, and stole him away from among the king's sons who were slain, and put him and his nurse in the bedchamber. So Jehoshabeath, the daughter of king Jehoram, the wife of Jehoiada the priest (for she was the sister of Ahaziah), hid him from Athaliah, so that she did not kill him.
12 Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi iwo mu Nyumba ya Mulungu kwa zaka zisanu ndi chimodzi muulamuliro wa Ataliya.
And he was with them hid in the house of God six years, and Athaliah reigned over the land.

< 2 Mbiri 22 >