< 1 Mbiri 24 >

1 Magulu a ana a Aaroni anali awa: Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
These were the divisions of the sons of Aaron. The sons of Aaron: Nadab, Abihu, Eleazar, and Ithamar.
2 Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe.
But Nadab and Abihu died before their father, and had no children; therefore Eleazar and Ithamar served as priests.
3 Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira.
David, with Zadok of the sons of Eleazar and Ahimelech of the sons of Ithamar, divided them according to their ordering in their service.
4 Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara.
There were more chief men found of the sons of Eleazar than of the sons of Ithamar; and they were divided like this: of the sons of Eleazar there were sixteen, heads of fathers’ houses; and of the sons of Ithamar, according to their fathers’ houses, eight.
5 Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.
Thus they were divided impartially by drawing lots; for there were princes of the sanctuary and princes of God, both of the sons of Eleazar, and of the sons of Ithamar.
6 Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.
Shemaiah the son of Nethanel the scribe, who was of the Levites, wrote them in the presence of the king, the princes, Zadok the priest, Ahimelech the son of Abiathar, and the heads of the fathers’ households of the priests and of the Levites; one fathers’ house being taken for Eleazar, and one taken for Ithamar.
7 Maere woyamba anagwera Yehoyaribu, achiwiri anagwera Yedaya,
Now the first lot came out to Jehoiarib, the second to Jedaiah,
8 achitatu anagwera Harimu, achinayi anagwera Seorimu,
the third to Harim, the fourth to Seorim,
9 achisanu anagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini,
the fifth to Malchijah, the sixth to Mijamin,
10 achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu anagwera Abiya,
the seventh to Hakkoz, the eighth to Abijah,
11 achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa, a khumi anagwera Sekaniya,
the ninth to Jeshua, the tenth to Shecaniah,
12 a 11 anagwera Eliyasibu, a 12 anagwera Yakimu,
the eleventh to Eliashib, the twelfth to Jakim,
13 a 13 anagwera Hupa, a 14 anagwera Yesebeabu,
the thirteenth to Huppah, the fourteenth to Jeshebeab,
14 a 15 anagwera Biliga, a 16 anagwera Imeri,
the fifteenth to Bilgah, the sixteenth to Immer,
15 a 17 anagwera Heziri, a 18 anagwera Hapizezi,
the seventeenth to Hezir, the eighteenth to Happizzez,
16 a 19 anagwera Petahiya, a 20 anagwera Ezekieli,
the nineteenth to Pethahiah, the twentieth to Jehezkel,
17 a 21 anagwera Yakini, a 22 anagwera Gamuli,
the twenty-first to Jachin, the twenty-second to Gamul,
18 a 23 anagwera Delaya, ndipo a 24 anagwera Maaziya.
the twenty-third to Delaiah, and the twenty-fourth to Maaziah.
19 Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.
This was their ordering in their service, to come into the LORD’s house according to the ordinance given to them by Aaron their father, as the LORD, the God of Israel, had commanded him.
20 Za zidzukulu zina zonse za Levi: Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli; kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya.
Of the rest of the sons of Levi: of the sons of Amram, Shubael; of the sons of Shubael, Jehdeiah.
21 Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake: Mtsogoleri anali Isiya.
Of Rehabiah: of the sons of Rehabiah, Isshiah the chief.
22 Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti; kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati.
Of the Izharites, Shelomoth; of the sons of Shelomoth, Jahath.
23 Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.
The sons of Hebron: Jeriah, Amariah the second, Jahaziel the third, and Jekameam the fourth.
24 Mwana wa Uzieli: Mika; kuchokera kwa ana a Mika: Samiri.
The sons of Uzziel: Micah; of the sons of Micah, Shamir.
25 Mʼbale wa Mika: Isiya; kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya.
The brother of Micah: Isshiah; of the sons of Isshiah, Zechariah.
26 Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Mwana wa Yaaziya: Beno.
The sons of Merari: Mahli and Mushi. The son of Jaaziah: Beno.
27 Ana a Merari: Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.
The sons of Merari by Jaaziah: Beno, Shoham, Zaccur, and Ibri.
28 Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.
Of Mahli: Eleazar, who had no sons.
29 Kuchokera kwa Kisi: Mwana wa Kisi: Yerahimeeli.
Of Kish, the son of Kish: Jerahmeel.
30 Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti. Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo.
The sons of Mushi: Mahli, Eder, and Jerimoth. These were the sons of the Levites after their fathers’ houses.
31 Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.
These likewise cast lots even as their brothers the sons of Aaron in the presence of David the king, Zadok, Ahimelech, and the heads of the fathers’ households of the priests and of the Levites, the fathers’ households of the chief even as those of his younger brother.

< 1 Mbiri 24 >