< 1 Mbiri 24 >

1 Magulu a ana a Aaroni anali awa: Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 2 Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe. 3 Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira. 4 Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara. 5 Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara. 6 Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara. 7 Maere woyamba anagwera Yehoyaribu, achiwiri anagwera Yedaya, 8 achitatu anagwera Harimu, achinayi anagwera Seorimu, 9 achisanu anagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini, 10 achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu anagwera Abiya, 11 achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa, a khumi anagwera Sekaniya, 12 a 11 anagwera Eliyasibu, a 12 anagwera Yakimu, 13 a 13 anagwera Hupa, a 14 anagwera Yesebeabu, 14 a 15 anagwera Biliga, a 16 anagwera Imeri, 15 a 17 anagwera Heziri, a 18 anagwera Hapizezi, 16 a 19 anagwera Petahiya, a 20 anagwera Ezekieli, 17 a 21 anagwera Yakini, a 22 anagwera Gamuli, 18 a 23 anagwera Delaya, ndipo a 24 anagwera Maaziya. 19 Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira. 20 Za zidzukulu zina zonse za Levi: Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli; kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya. 21 Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake: Mtsogoleri anali Isiya. 22 Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti; kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati. 23 Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi. 24 Mwana wa Uzieli: Mika; kuchokera kwa ana a Mika: Samiri. 25 Mʼbale wa Mika: Isiya; kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya. 26 Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Mwana wa Yaaziya: Beno. 27 Ana a Merari: Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri. 28 Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna. 29 Kuchokera kwa Kisi: Mwana wa Kisi: Yerahimeeli. 30 Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti. Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo. 31 Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.

< 1 Mbiri 24 >