< Від Матвія 15 >

1 Тоді до Ісуса прийшли фарисеї та книжники з Єрусалиму н сказали:
Pamenepo Afarisi ena ndi aphunzitsi amalamulo anabwera kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu ndipo anamufunsa kuti,
2 „Чого Твої учні ламають переда́ння старших? Бо не миють вони своїх рук, коли хліб споживають“.
“Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!”
3 А Він відповів і промовив до них: „А чого й ви порушуєте Божу заповідь ради переда́ння вашого?
Yesu anayankha kuti, “Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu?
4 Бо Бог заповів: „Шануй ба́тька та матір“, та: „Хто злорі́чить на ба́тька чи матір, — хай смертю помре“.
Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’
5 А ви кажете: Коли скаже хто ба́тьку чи матері: „Те, чим би ви скористатись від мене хотіли, то дар Богові “,
Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’
6 то може вже й не шанувати той ба́тька свого або матір свою. Так ви ради переда́ння вашого зні́вечили Боже Слово.
iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu.
7 Лицеміри! Про вас добре Ісая пророкував, говорячи:
Inu anthu achiphamaso, Yesaya ananenera za inu kuti,
8 „Оці люди уста́ми шанують Мене, серце ж їхнє дале́ко від Мене!
“‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
9 Та однак надаре́мне шанують Мене, бо навчають наук — лю́дських за́повідей“.
Amandilambira Ine kwachabe ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’”
10 І Він покликав наро́д, і промовив до нього: „Послухайте та зрозумійте!
Yesu anayitana gulu la anthu nati, “Mverani ndipo zindikirani.
11 Не те, що вхо́дить до уст, люди́ну скверни́ть, але те, що виходить із уст, те люди́ну скверни́ть“.
Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”
12 Тоді учні Його приступили й сказали Йому: „Чи Ти знаєш, що фарисеї, почуши це слово, спокуси́лися?“
Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?”
13 А Він відповів і сказав: „Усяка росли́на, яку насадив не Отець Мій Небесний, буде вирвана з коренем.
Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe.
14 Залишіть ви їх: це сліпі повода́тарі для сліпих. А коли сліпий водить сліпого, — обо́є до ями впаду́ть“.
Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”
15 А Петро відповів і до Нього сказав: „Поясни нам цю при́тчу“.
Petro anati, “Timasulireni fanizoli.”
16 А Він відказав: „Чи ж і ви розумі́ння не маєте?
Yesu anawafunsa kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa?
17 Чи ж ви не розумієте, що все те, що́ входить до уст, вступає в живіт, та й назовні виходить?
Kodi inu simudziwa kuti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi?
18 Що ж виходить із уст, те походить із серця, — і воно опога́нює люди́ну.
Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa.
19 Бо з серця виходять лихі думки́, душогубства, пере́люби, розпуста, крадіж, неправдиві засвідчення, богознева́ги.
Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe.
20 Оце те, що люди́ну опога́нює. А їсти руками невмитими, — не опога́нює це люди́ни!“
Izi ndi zimene zimachititsa munthu kukhala woyipa; koma kudya ndi mʼmanja mosasamba sikumuchititsa munthu kukhala woyipa.”
21 І, вийшовши звідти, Ісус відійшов у землі ти́рські й сидо́нські.
Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni.
22 І ось жінка одна ханане́янка, із тих околиць прийшовши, заголосила до Нього й сказала: „Змилуйся надо мною, Господи, Сину Давидів, — де́мон тяжко дочку́ мою мучить!“
Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”
23 А Він їй не казав ані слова. Тоді учні Його, підійшовши, благали Його та казали: „Відпусти її, бо кричить услід за нами!“
Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, “Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu.”
24 А Він відповів і сказав: „Я по́сланий тільки до овечок загинулих дому Ізраїлевого“.
Iye anayankha kuti, “Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha.”
25 А вона, підійшовши, уклонилась Йому та й сказала: „Господи, допоможи мені!“
Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!”
26 А Він відповів і сказав: „Не годи́ться взяти хліб у дітей, і кинути щеня́там“.
Iye anayankha kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.”
27 Вона ж відказала: „Так, Господи! Але ж і щеня́та їдять ті кришки́, що спадають зо сто́лу їхніх панів“.
Mayiyo anati, “Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo.”
28 Тоді відповів і сказав їй Ісус: „О жінко, твоя віра велика, — нехай буде тобі, я́к ти хочеш“! І тієї години дочка́ її ви́дужала.
Pomwepo Yesu anayankha kuti, “Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka.” Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.
29 І, відійшовши звідти, Ісус прибув до Галіле́йського моря, і, зійшовши на го́ру, сів там.
Yesu anachoka kumeneko napita mʼmbali mwa nyanja ya Galileya. Ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi.
30 І приступило до Нього багато наро́ду, що мали з собою кривих, калік, сліпих, німих і інших багато, і клали їх до Ісусових ніг. І Він уздоро́влював їх.
Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye ndi anthu olumala, osaona, ofa ziwalo, osayankhula ndi ena ambiri nawagoneka pa mapazi ake ndipo Iye anawachiritsa.
31 А наро́д не вихо́див із дива, бо бачив, що говорять німі, каліки стаю́ть здорові, криві ходять, і бачать сліпі, — і сла́вив він Бога Ізраїлевого!
Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.
32 А Ісус Своїх у́чнів покликав і сказав: „Жаль Мені цих людей, що вже три́ дні зо Мною знахо́дяться, але їсти не мають чого́; відпустити їх без їжі не хо́чу, щоб вони не ослабли в дорозі“.
Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira.”
33 А учні Йому відказали: „Де́ нам узяти стільки хліба в пустині, щоб нагодувати стільки наро́ду?“
Ophunzira anayankha kuti, “Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?”
34 А Ісус запитав їх: „Скільки маєте хліба?“Вони ж відказали: „Семеро, та трохи рибок“.
Yesu anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?” Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono.”
35 І Він ізвелів на землі посідати наро́дові.
Iye anawuza gululo kuti likhale pansi.
36 І, взявши сім хлібів і риби, віддавши Богу подяку, поламав і дав у́чням Своїм, а учні наро́дові.
Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo.
37 І всі їли й наси́тилися, а з позосталих кусків назбирали сім ко́шиків по́вних...
Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri.
38 Їдців же було чотири тисячі мужа, окрім жінок та дітей.
Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana.
39 І, відпустивши наро́д, усів Він до чо́вна, і прибув до землі Магдали́нської.
Yesu atatha kuwuza gululo kuti lipite kwawo, analowa mʼbwato ndipo anapita kudera la Magadala.

< Від Матвія 15 >