< Ester 2 >

1 Bu olaylardan sonra öfkesi dinen Kral Ahaşveroş, Vaşti'yi, yaptıklarını ve ona karşı alınan kararı anımsadı.
Pambuyo pake mtima wa Ahasiwero utatsika, Ahasiwero anakumbukira Vasiti ndi zimene anachita Vasitiyo. Anakumbukiranso lamulo lomukhudza limene anasindikiza.
2 Kralın özel hizmetkârları, “Kral için genç, güzel, el değmemiş kızlar aransın” dediler,
Tsono anyamata a mfumu amene ankamutumikira anati, “Mfumu, akufunireni anamwali okongola.
3 “Kral, egemen olduğu bütün illerde görevliler atasın. Bu görevliler bütün genç, güzel, el değmemiş kızları toplayıp Sus Kalesi'ndeki hareme getirsinler, kralın kızlardan sorumlu haremağası Hegay'a teslim etsinler. Güzelleşmeleri için ne gerekiyorsa verilsin.
Mfumu isankhe oyangʼanira pa chigawo chilichonse cha ufumu wake kuti abwere nawo pamodzi anamwali onse okongola ku nyumba yosungira akazi ku Susa. Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene amayangʼanira amayi, akhale wosamalira anamwaliwa ndipo aziwapatsa mafuta odzola.
4 Sonunda kralın hoşuna giden kız, Vaşti'nin yerine kraliçe olsun.” Kral bu öneriyi beğendi ve söyleneni yaptı.
Ndipo namwali amene mfumu yakondwera naye akhale mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.” Mfumu inakondwera ndi uphunguwu, ndipo inachita momwemo.
5 Sus Kalesi'nde Mordekay adında bir Yahudi vardı. Benyamin oymağından olan Mordekay, Kiş oğlu Şimi oğlu Yair'in oğluydu.
Myuda wina wa fuko la Benjamini, dzina lake Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi, anali mu mzinda wa Susa.
6 Kiş, Babil Kralı Nebukadnessar'ın Yahuda Kralı Yehoyakin ile birlikte Yeruşalim'den sürgün ettiği kişilerden biriydi.
Iyeyu anali mmodzi mwa anthu amene anatengedwa ukapolo ndi Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda.
7 Mordekay'ın Hadassa adında bir amca kızı vardı. Annesiyle babasını yitiren Hadassa'yı Mordekay evlat edinip büyütmüştü. Hadassa'nın öbür adı Ester'di; endamı ve yüzü güzeldi.
Mordekai nʼkuti atalera Hadasa, amene ankatchedwanso Estere, mwana wamkazi wa amalume ake chifukwa analibe abambo kapena amayi. Mtsikanayu anali wokongola ndi wooneka bwino ndipo Mordekai ankamutenga ngati mwana wake weniweni pamene abambo ndi amayi ake anamwalira.
8 Kralın buyruğu ve fermanı yayınlandıktan sonra çok sayıda genç kız Sus Kalesi'ne getirilip harem sorumlusu Hegay'a teslim edildi. Saraya getirilen kızlar arasında Ester de vardı.
Lamulo la mfumu atalilengeza ndi kubwera nawo pamodzi anamwali ambiri ku mzinda wa Susa kuti akasamalidwe ndi Hegai, Estere nayenso anatengedwa kupita naye ku nyumba ya mfumu kuti akasamalidwe ndi Hegai woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi uja.
9 Hegay Ester'i beğendi ve ona ayrıcalık tanıdı. En iyi biçimde beslenip güzelleşmesi için ne gerekiyorsa hemen sağladı; ayrıca kralın sarayından seçilen yedi hizmetçiyi buyruğuna verdi. Sonra onu hizmetçileriyle birlikte haremin en güzel bölümüne yerleştirdi.
Hegai anasangalatsidwa naye namwaliyo ndipo anamukomera mtima. Mosataya nthawi anamupatsa mafuta ake odzola ndi chakudya chapadera. Anamusankhiranso anamwali asanu ndi awiri a ku nyumba ya mfumu kuti azimutumikira, ndipo iye pamodzi ndi anamwali omutumikira aja anawapatsa malo abwino koposa mʼnyumba yosungira akazi.
10 Ester halkını da, soyunu da açıklamadı. Çünkü Mordekay bunları açıklamasını yasaklamıştı.
Estere sanawulule mtundu wake ndi abale ake chifukwa Mordekai anamuletsa kutero.
11 Mordekay, Ester'in nasıl olduğunu ve ona nasıl davranıldığını öğrenmek için her gün haremin avlusunun önünde gezinip dururdu.
Tsiku ndi tsiku Mordekai ankayendayenda pafupi ndi bwalo la nyumba yosungiramo akazi ija kuti adziwe za moyo wa Estere ndi kuti zinthu zikumuyendera bwanji.
12 Her genç kız sırası geldiğinde Kral Ahaşveroş'un huzuruna çıkacaktı. Ama kızlarla ilgili kurallar uyarınca, önce on iki ay süren güzellik bakımını tamamlaması gerekiyordu. Altı ay süreyle her kıza mür yağı sürülüyor, altı ay da kremler, losyonlar uygulanıyordu.
Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa.
13 Kralın yanına girme sırası gelen genç kız, haremden her istediğini alıp birlikte saraya götürürdü.
Ndipo namwali ankapita kwa mfumu motere: Ankaloledwa kutenga chilichonse angafune mʼnyumba yosungiramo akazi kupita nacho ku nyumba ya mfumu.
14 Akşam kralın yanına giren kız, ertesi sabah ikinci hareme, cariyelerden sorumlu haremağası Şaaşgaz'ın yönetimindeki hareme dönerdi. Yalnız kralın beğendiği, adıyla çağırdığı kız yeniden onun yanına girebilirdi.
Ankalowa madzulo kwa mfumu ndi kutuluka mmawa kupita ku nyumba ina yosungira akazi yomwe ankayangʼanira ndi Saasigazi, mdindo wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi a mfumu. Namwali sankabwerera kwa mfumu pokhapokha amukomere mtima ndi kumuyitana potchula dzina lake.
15 Kralın yanına girme sırası Mordekay'ın evlat edindiği Ester'e –Mordekay'ın amcası Avihayil'in kızına– gelince, Ester, kralın kızlardan sorumlu haremağası Hegay'ın kendisine önerdiklerinden başka bir şey istemedi. Kendisini gören herkesin beğenisini kazandı.
Tsono inafika nthawi kuti Estere, mwana wamkazi wa Abihaili amenenso analeredwa ndi Mordekai amalume ake, alowe kwa mfumu. Iye sanapemphe kanthu kalikonse, koma anatenga zokhazo zimene ananena Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi. Ndipo aliyense amene anamuona Estere, anasangalatsidwa naye.
16 Ahaşveroş'un krallığının yedinci yılında, Tevet diye adlandırılan onuncu ayda, Ester saraya, kralın yanına götürüldü.
Anapita naye kwa mfumu Ahasiwero ku nyumba ya ufumu pa mwezi wa khumi, mwezi wa Tebete, chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.
17 Kral Ester'i öbür kızlardan daha çok sevdi, en çok ondan hoşlandı, en çok ona ayrıcalık tanıdı. Kraliçelik tacını ona giydirip Vaşti'nin yerine kraliçe yaptı.
Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.
18 Ardından Ester'in onuruna büyük bir şölen verdi. Bu şölende bütün önderler ve görevliler hazır bulundu. Kral bütün illerde bayram ilan etti ve krallara yaraşır cömertlikle armağanlar dağıttı.
Ndipo mfumu inakonza phwando lalikulu, phwando la Estere, kukonzera anthu olemekezeka ndi nduna zake zonse. Analamuliranso kuti anthu mʼzigawo zonse asapereke msonkho ndipo anapereka mphatso monga mwakukoma mtima kwa mfumu.
19 Kızlar ikinci kez toplandıklarında Mordekay, kralın kapı görevlilerinden biri olmuştu.
Anamwali atasonkhanitsidwa pamodzi, Mordekai anakhala pansi pa chipata cha mfumu.
20 Ester, Mordekay'ın verdiği buyruk uyarınca, soyunu ve halkını henüz açıklamamıştı; kendisini büyüttüğü günlerde olduğu gibi, Mordekay'ın sözünü dinlemeye devam etti.
Koma Estere anali asanawululebe za mtundu wake ndi anthu a pa banja lake monga momwe analamulira Mordekai, chifukwa anapitirira kutsata malangizo a Mordekai monga ankachitira pamene ankamulera.
21 Mordekay kralın kapı görevlisiyken, kapı nöbetçilerinden ikisi, Bigtan ve Tereş, Kral Ahaşveroş'a öfkelendiler; onu öldürmek için fırsat kollamaya başladılar.
Pa nthawi imene Mordekai ankalondera pa chipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa amfumu, olondera pa khomo la nyumba yake, anayipidwa mtima ndipo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero.
22 Durumu öğrenen Mordekay bunu Kraliçe Ester'e iletti; o da Mordekay adına krala bildirdi.
Koma Mordekai atazindikira za chiwembuchi anawuza mfumukazi Estere ndipo iye anakawuza mfumu mʼmalo mwa Mordekai.
23 Durum araştırıldı; doğru olduğu anlaşılınca da iki adam darağacına asıldı ve olay kralın önünde tarih kayıtlarına geçirildi.
Ndipo pamene anafufuza za chiwembuchi kuti zinali zoona, adindo awiriwa anaphedwa monyongedwa. Zinthu izi zinalembedwa mʼbuku la Mbiri ndi kusungidwa ndi Mfumu.

< Ester 2 >