< Salmos 51 >

1 Al Músico principal: Salmo de David, cuando después que entró á Bathsebah, vino á él Nathán el profeta. TEN piedad de mí, oh Dios, conforme á tu misericordia: conforme á la multitud de tus piedades borra mis rebeliones.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba. Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; molingana ndi chifundo chanu chachikulu mufafanize mphulupulu zanga.
2 Lávame más y más de mi maldad, y límpiame de mi pecado.
Munditsuke zolakwa zanga zonse ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.
3 Porque yo reconozco mis rebeliones; y mi pecado está siempre delante de mí.
Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.
4 A ti, á ti solo he pecado, y he hecho lo malo delante de tus ojos: porque seas reconocido justo en tu palabra, y tenido por puro en tu juicio.
Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa ndipo ndachita zoyipa pamaso panu, Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
5 He aquí, en maldad he sido formado, y en pecado me concibió mi madre.
Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa, wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
6 He aquí, tú amas la verdad en lo íntimo: y en lo secreto me has hecho comprender sabiduría.
Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga; mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.
7 Purifícame con hisopo, y seré limpio: lávame, y seré emblanquecido más que la nieve.
Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera, munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala
8 Hazme oir gozo y alegría; y se recrearán los huesos que has abatido.
Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo, mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.
9 Esconde tu rostro de mis pecados, y borra todas mis maldades.
Mufulatire machimo anga ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.
10 Crea en mí, oh Dios, un corazón limpio; y renueva un espíritu recto dentro de mí.
Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
11 No me eches de delante de ti; y no quites de mí tu santo espíritu.
Musandichotse pamaso panu kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
12 Vuélveme el gozo de tu salud; y el espíritu libre me sustente.
Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.
13 Enseñaré á los prevaricadores tus caminos; y los pecadores se convertirán á ti.
Pamenepo ndidzaphunzitsa anthu amphulupulu njira zanu kuti ochimwa adzabwerere kwa inu.
14 Líbrame de homicidios, oh Dios, Dios de mi salud: cantará mi lengua tu justicia.
Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu wa chipulumutso changa, ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.
15 Señor, abre mis labios; y publicará mi boca tu alabanza.
Inu Ambuye tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.
16 Porque no quieres tú sacrificio, que yo daría; no quieres holocausto.
Inu simusangalatsidwa ndi nsembe wamba. Ndikanapereka nsembe yopsereza, Inu simukondwera nayo.
17 Los sacrificios de Dios son el espíritu quebrantado: al corazón contrito y humillado no despreciarás tú, oh Dios.
Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka; mtima wosweka ndi wachisoni Inu Mulungu simudzawunyoza.
18 Haz bien con tu benevolencia á Sión: edifica los muros de Jerusalem.
Mwa kukoma mtima kwanu mupange Ziyoni kuti alemere; mumange makoma a Yerusalemu.
19 Entonces te agradarán los sacrificios de justicia, el holocausto ú ofrenda del todo quemada: entonces ofrecerán sobre tu altar becerros.
Kotero kudzakhala nsembe zachilungamo, nsembe yonse yopsereza yokondweretsa Inu; ndipo ngʼombe zazimuna zidzaperekedwa pa guwa lanu la nsembe.

< Salmos 51 >