< Lamentaciones 5 >

1 ACUÉRDATE, oh Jehová, de lo que nos ha sucedido: ve y mira nuestro oprobio.
Inu Yehova, kumbukirani zimene zinatichitikira; yangʼanani ndipo muone kunyozeka kwathu.
2 Nuestra heredad se ha vuelto á extraños, nuestras casas á forasteros.
Apereka cholowa chathu kwa obwera, nyumba zathu kwa alendo.
3 Huérfanos somos sin padre, nuestras madres como viudas.
Takhala amasiye ndi wopanda abambo, amayi athu ali ngati akazi amasiye.
4 Nuestra agua bebemos por dinero; nuestra leña por precio compramos.
Tiyenera kugula madzi amene timamwa, nkhuni zathunso nʼzogula.
5 Persecución padecemos sobre nuestra cerviz: nos cansamos, y no hay para nosotros reposo.
Otilondola atigwira pakhosi; tafowoka ndipo sakutilola kupumula.
6 Al Egipcio y al Asirio dimos la mano, para saciarnos de pan.
Tinadzipereka kwa Aigupto ndi kwa Asiriya kuti tipeze chakudya.
7 Nuestros padres pecaron, y son muertos; y nosotros llevamos sus castigos.
Makolo athu anachimwa ndipo anafa kale, koma chilango chawo chili pa ife.
8 Siervos se enseñorearon de nosotros; no hubo quien de su mano nos librase.
Akapolo akutilamulira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe angatimasule mʼdzanja lawo.
9 Con peligro de nuestras vidas traíamos nuestro pan delante del cuchillo del desierto.
Timapeza chakudya chathu poyika miyoyo yathu pa chiswe chifukwa cha lupanga mʼchipululu.
10 Nuestra piel se ennegreció como un horno á causa del ardor del hambre.
Khungu lathu latentha ngati uvuni mʼngʼanjo, chifukwa cha kuwawa kwa njala.
11 Violaron á las mujeres en Sión, á las vírgenes en las ciudades de Judá.
Amayi agwiriridwa mu Ziyoni, ndi anamwali mʼmizinda ya Yuda.
12 A los príncipes colgaron por su mano; no respetaron el rostro de los viejos.
Akalonga athu akuwapachika pomangirira manja awo, akuluakulu sakuwalemekeza.
13 Llevaron los mozos á moler, y los muchachos desfallecieron en la leña.
Achinyamata akukakamizidwa kupera tirigu; anyamata akudzandira ndi mitolo ya nkhuni.
14 Los ancianos cesaron de la puerta, los mancebos de sus canciones.
Akuluakulu anachokapo pa chipata cha mzinda; achinyamata aleka nyimbo zawo.
15 Cesó el gozo de nuestro corazón; nuestro corro se tornó en luto.
Chimwemwe chachoka mʼmitima yathu; kuvina kwathu kwasanduka maliro.
16 Cayó la corona de nuestra cabeza: ¡ay ahora de nosotros! porque pecamos.
Chipewa chathu chaufumu chagwa pamutu pathu. Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa!
17 Por esto fué entristecido nuestro corazón, por esto se entenebrecieron nuestros ojos:
Mitima yathu yakomoka chifukwa cha zimenezi, chifukwa cha zinthu zimenezi maso athu sakuona bwino,
18 Por el monte de Sión que está asolado; zorras andan en él.
pakuti phiri la Ziyoni, limene lasanduka bwinja, nkhandwe zikungoyendayendapo.
19 Mas tú, Jehová, permanecerás para siempre: tu trono de generación en generación.
Inu Yehova, lamulirani kwamuyaya; mpando wanu waufumu udzakhalabe ku mibadomibado.
20 ¿Por qué te olvidarás para siempre de nosotros, y nos dejarás por largos días?
Chifukwa chiyani mumatiyiwala nthawi zonse? Chifukwa chiyani mwatitaya nthawi yayitali chotere?
21 Vuélvenos, oh Jehová, á ti, y nos volveremos: renueva nuestros días como al principio.
Yehova mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere; mukonzenso masiku athu akhale monga akale,
22 Porque repeliendo nos has desechado; te has airado contra nosotros en gran manera.
pokhapokha ngati mwatitaya kotheratu, ndi kuti mwatikwiyira kobzola muyeso.

< Lamentaciones 5 >