< 2 Samuel 3 >

1 Y HUBO larga guerra entre la casa de Saúl y la casa de David; mas David se iba fortificando, y la casa de Saúl iba en disminución.
Nkhondo ya pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide inachitika nthawi yayitali. Mphamvu za Davide zinkakulirakulirabe, pamene banja la Sauli mphamvu zake zimapita zicheperachepera.
2 Y nacieron hijos á David en Hebrón: su primogénito fué Ammón, de Ahinoam Jezreelita;
Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa: Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli.
3 Su segundo Chileab, de Abigail la mujer de Nabal, el del Carmelo; el tercero, Absalóm, hijo de Maachâ, hija de Talmai rey de Gessur:
Mwana wachiwiri anali Kileabu, amayi ake anali Abigayeli mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimeli. Wachitatu anali Abisalomu, amayi ake anali Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri;
4 El cuarto, Adonías hijo de Haggith; el quinto, Saphatías hijo de Abital;
wachinayi anali Adoniya, amayi ake anali Hagiti; wachisanu, Sefatiya amayi ake anali Abitali;
5 El sexto, Jetream, de Egla mujer de David. Estos nacieron á David en Hebrón.
ndipo wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila, mkazi wa Davide. Ana awa a Davide anabadwira ku Hebroni.
6 Y como había guerra entre la casa de Saúl y la de David, aconteció que Abner se esforzaba por la casa de Saúl.
Pamene kunali nkhondo pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide, Abineri anayamba kudzipatsa yekha mphamvu pakati pa banja la Sauli.
7 Y había Saúl tenido una concubina que se llamaba Rispa, hija de Aja. Y dijo [Is-boseth] á Abner: ¿Por qué has entrado á la concubina de mi padre?
Sauli anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa mwana wa Ayiwa. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, “Nʼchifukwa chiyani unagona ndi mzikazi wa abambo anga?”
8 Y enojóse Abner en gran manera por las palabras de Is-boseth, y dijo: ¿Soy yo cabeza de perros respecto de Judá? Yo he hecho hoy misericordia con la casa de Saúl tu padre, con sus hermanos, y con sus amigos, y no te he entregado en las manos de David: ¿y tú me haces hoy cargo del pecado de esta mujer?
Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu!
9 Así haga Dios á Abner y así le añada, si como ha jurado Jehová á David no hiciere yo así con él,
Mulungu andilange ine Abineri, andilange kwambiri, ngati sindichitira Davide zimene Yehova anamulonjeza iye mwa lumbiro.
10 Trasladando el reino de la casa de Saúl, y confirmando el trono de David sobre Israel y sobre Judá, desde Dan hasta Beer-sebah.
Ndidzachotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazikitsa ufumu wa Davide pa Aisraeli onse ndi Yuda kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba.”
11 Y él no pudo responder palabra á Abner, porque le temía.
Isiboseti sanayerekezenso kunena mawu ena kwa Abineri, chifukwa ankamuopa.
12 Y envió Abner mensajeros á David de su parte, diciendo: ¿Cúya es la tierra? Y que le dijesen: Haz alianza conmigo, y he aquí que mi mano será contigo para volver á ti á todo Israel.
Kenaka Abineri anatuma amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Kodi dzikoli ndi la yani? Uchite mgwirizano ndi ine ndipo ndidzakuthandiza kuti Aisraeli onse azikutsatira.”
13 Y [David] dijo: Bien; yo haré contigo alianza: mas una cosa te pido, y es, que no me vengas á ver sin que primero traigas á Michâl la hija de Saúl, cuando vinieres á verme.
Davide anati, “Chabwino. Ine ndichita mgwirizano ndi iwe. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usabwere pamaso panga pokhapokha utabweretsa Mikala mwana wamkazi wa Sauli, ukamabwera kudzandiona.”
14 Después de esto envió David mensajeros á Is-boseth hijo de Saúl, diciendo: Restitúyeme á mi mujer Michâl, la cual yo desposé conmigo por cien prepucios de Filisteos.
Ndipo Davide anatuma amithenga kwa Isi-Boseti mwana wa Sauli, kumulamula kuti, “Patse mkazi wanga Mikala, amene ndinamukwatira ndi makungu 100 a msonga za mavalo a Afilisti.”
15 Entonces Is-boseth envió, y quitóla á su marido Paltiel, hijo de Lais.
Kotero Isi-Boseti analamulira ndipo anakamutenga kwa mwamuna wake Palitieli mwana wa Laisi.
16 Y su marido fué con ella, siguiéndola y llorando hasta Bahurim. Y díjole Abner: Anda, vuélvete. Entonces él se volvió.
Koma mwamuna wake anapita naye akulira pambuyo pake njira yonse mpaka ku Bahurimu. Kenaka Abineri anati kwa iye, “Bwerera kwanu!” Ndipo anabwerera kwawo.
17 Y habló Abner con los ancianos de Israel, diciendo: Ayer y antes procurabais que David fuese rey sobre vosotros;
Abineri anakambirana ndi akuluakulu a Israeli ndipo anati, “Kwa kanthawi mwakhala mukufuna kulonga Davide kuti akhale mfumu yanu.
18 Ahora, pues, hacedlo; porque Jehová ha hablado á David, diciendo: Por la mano de mi siervo David libraré á mi pueblo Israel de mano de los Filisteos, y de mano de todos sus enemigos.
Tsopano chitani zimenezo! Pakuti Yehova analonjeza Davide kuti, ‘Kudzera mwa mtumiki wanga Davide ndidzapulumutsa anthu anga Aisraeli mʼdzanja la Afilisti ndi kuwachotsa mʼmanja mwa adani awo.’”
19 Y habló también Abner á los de Benjamín: y fué también Abner á Hebrón á decir á David todo el parecer de los de Israel y de toda la casa de Benjamín.
Abineri anayankhulanso nawo yekha anthu a fuko la Benjamini. Kenaka anapita ku Hebroni kukamuwuza Davide zonse zimene Aisraeli ndi fuko lonse la Benjamini amafuna kuchita.
20 Vino pues Abner á David en Hebrón, y con él veinte hombres: y David hizo banquete á Abner y á los que con él habían venido.
Abineri, amene anali ndi anthu makumi awiri, atafika kwa Davide ku Hebroni, Davide anamukonzera phwando pamodzi ndi anthu ake.
21 Y dijo Abner á David: Yo me levantaré é iré, y juntaré á mi señor el rey á todo Israel, para que hagan contigo alianza, y tú reines como deseas. David despidió luego á Abner, y él se fué en paz.
Ndipo Abineri anawuza Davide kuti, “Loleni kuti ndipite msanga kukasonkhanitsa Aisraeli onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuye wanga mfumu, kuti adzachite nanu pangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Kotero Davide analola Abineri kuti apite, ndipo anapita mwamtendere.
22 Y he aquí los siervos de David y Joab, que venían del campo, y traían consigo gran presa. Mas Abner no estaba con David en Hebrón, que ya lo había él despedido, y él se había ido en paz.
Nthawi yomweyo ankhondo a Davide ndi Yowabu anafika kuchokera kumene anakathira nkhondo ndipo anabweretsa katundu wambiri wolanda ku nkhondo. Koma Abineri sanalinso ndi Davide ku Hebroni, chifukwa Davide anamulola kuti apite, ndipo anapita mu mtendere.
23 Y luego que llegó Joab y todo el ejército que con él estaba, fué dado aviso á Joab, diciendo: Abner hijo de Ner ha venido al rey, y él le ha despedido, y se fué en paz.
Yowabu ndi asilikali onse amene anali naye atafika, anawuzidwa kuti Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu ndipo kuti mfumu yamulola kuti apite ndi kuti wapita ndi mtendere.
24 Entonces Joab vino al rey, y díjole: ¿Qué has hecho? He aquí habíase venido Abner á ti: ¿por qué pues lo dejaste que se fuése?
Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Mwachita chiyani? Taonani, Abineri anabwera kwa inu. Nʼchifukwa chiyani mwamulola kuti apite? Tsopanotu wapitadi!
25 ¿Sabes tú que Abner hijo de Ner ha venido para engañarte, y á saber tu salida y tu entrada, y por entender todo lo que tú haces?
Inu mukumudziwa bwino Abineri mwana wa Neri. Iye anabwera kudzakunamizani ndi kudzaona mayendedwe anu ndiponso kudzaona zonse zimene mukuchita.”
26 Y saliéndose Joab de con David, envió mensajeros tras Abner, los cuales le volvieron desde el pozo de Sira, sin saberlo David.
Kenaka Yowabu anachoka pamaso pa Davide ndipo anatumiza amithenga kutsatira Abineri, ndipo anabwera naye kuchokera ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanadziwe zimenezi.
27 Y como Abner volvió á Hebrón, apartólo Joab al medio de la puerta, hablando con él blandamente, y allí le hirió por la quinta [costilla], á causa de la muerte de Asael su hermano, y murió.
Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa.
28 Cuando David supo después esto, dijo: Limpio estoy yo y mi reino, por Jehová, para siempre, de la sangre de Abner hijo de Ner.
Patapita nthawi, Davide atamva zimenezi anati, “Ine ndi ufumu wanga tidzakhala osalakwa pamaso pa Yehova pa imfa ya Abineri mwana wa Neri.
29 Caiga sobre la cabeza de Joab, y sobre toda la casa de su padre; que nunca falte de la casa de Joab quien padezca flujo, ni leproso, ni quien ande con báculo, ni quien muera á cuchillo, ni quien tenga falta de pan.
Mlandu umenewu ukhala pa Yowabu ndi banja lonse la abambo ake! Mʼbanja la Yowabu musadzasowe munthu wodwala matenda a chizonono kapena khate, kapena wolumala woyendera ndodo kapena wophedwa ndi lupanga, kapena wosowa chakudya.”
30 Joab pues y Abisai su hermano mataron á Abner, porque él había muerto á Asael, hermano de ellos en la batalla de Gabaón.
(Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anapha Abineri chifukwa iye anapha mʼbale wawo Asaheli ku nkhondo ku Gibiyoni).
31 Entonces dijo David á Joab, y á todo el pueblo que con él estaba: Romped vuestros vestidos, y ceñíos de sacos, y haced duelo delante de Abner. Y el rey iba detrás del féretro.
Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi anthu onse amene anali nawo, “Ngʼambani zovala zanu ndipo muvale ziguduli, muyende mukulira patsogolo pa Abineri.” Mfumu Davide mwini anayenda motsatira chitandacho.
32 Y sepultaron á Abner en Hebrón: y alzando el rey su voz, lloró junto al sepulcro de Abner; y lloró también todo el pueblo.
Iwo anamuyika Abineri mʼmanda ku Hebroni ndipo mfumu inalira mokweza pa manda a Abineri. Ndipo anthu onse analiranso.
33 Y endechando el rey al mismo Abner, decía: ¿Murió Abner como muere un villano?
Mfumu inayimba nyimbo iyi ya maliro a Abineri: “Abineri nʼkufa motere monga mmene chimafera chitsiru.
34 Tus manos no estaban atadas, ni tus pies ligados con grillos: caíste como los que caen delante de malos hombres. Y todo el pueblo volvió á llorar sobre él.
Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulungidwa. Iwe wafa monga mmene amafera anthu pamaso pa anthu oyipa.” Ndipo anthu onse analiranso kulirira Abineri.
35 Y como todo el pueblo viniese á dar de comer pan á David siendo aún de día, David juró, diciendo: Así me haga Dios y así me añada, si antes que se ponga el sol gustare yo pan, ú otra cualquier cosa.
Kenaka onse anabwera kwa Davide kumuwumiriza kuti adye kusanade. Koma Davide analumbira kuti, “Mulungu andilange ine, andilange kwambiri, ngati ndilawe buledi kapena chilichonse dzuwa lisanalowe!”
36 Súpolo así todo el pueblo, y plugo en sus ojos; porque todo lo que el rey hacía parecía bien en ojos de todo el pueblo.
Anthu onse anadziwa zimenezi ndipo zinawakondweretsa ndithu. Zonse zimene mfumu inachita zinawakondweretsa.
37 Y todo el pueblo y todo Israel entendieron aquel día, que no había venido del rey que Abner hijo de Ner muriese.
Kotero tsiku limeneli anthu onse ndi Aisraeli onse anadziwa kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abineri mwana wa Neri aphedwe.
38 Y el rey dijo á sus siervos: ¿No sabéis que ha caído hoy en Israel un príncipe, y grande?
Ndipo mfumu inati kwa ankhondo ake, “Kodi inu simukudziwa kuti lero mu Israeli mwagwa kalonga ndi munthu wamkulu?
39 Que yo ahora aun soy tierno rey ungido; y estos hombres, los hijos de Sarvia, muy duros me son: Jehová dé el pago al que mal hace, conforme á su malicia.
Ndipo lero, ngakhale ine ndine mfumu yodzozedwa, ndilibe mphamvu ndipo ana awa a Zeruya ndi amphamvu kwa ine. Yehova abwezere woyipa molingana ndi zoyipa zake!”

< 2 Samuel 3 >